Dataset Viewer
Text
stringlengths 292
6.6k
| labels
int64 0
19
|
---|---|
Anthu aphunzitsidwe zauindo wawoNice Bungwe la National Initiative for Civic Education (Nice) Public Trust lati dziko lino likulephera kutukuka chifukwa choti anthu ambiri sadaphunzitsidwe za ufulu komanso udindo wawo pa zinthu zosiyanasiyana, kuphatikizapo ntchito za chitukuko.
Mkulu wa Nice Trust, Ollen Mwalubunju, ndi yemwe adanena izi Lolemba potsegulira maphunziro a masiku atatu a ogwira ntchito zophunzitsa anthu kubungweli.
Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Maphunzirowa adachitikira mboma la Blantyre ndi thandizo lochokera ku bungwe la mgwirizano wa maiko a ku Ulaya la European Union (EU).
Mwalubunju adatsindika kuti, kwa zaka zingapo, boma lakhala likugwira ntchito zachitukuko popanda kupereka mpata kwa nzika kuti zitengepo gawo pa ntchitozo.
Choncho, mpofunika kuti boma komanso mabungwe ngati ife a Nice Trust lichilimike pophunzitsa anthu za maufulu omwe ali nawo komanso ndi udindo womwe ayenera kusenza kuti chitukukocho chitheke, iye adatero.
Mwalubunju adapempha ogwira ntchito zophunzitsa anthu mmaboma kuti akhale patsogolo pa ntchitoyi.
Ife a Nice Trust tili ndi kuthekera konse pantchitoyi potengera ntchito yomwe takhala tikugwira pophunzitsa anthu zachisankho mmbuyomu, adaonjeza.
Mkuluyo adathokoza bungwe la EU kaamba ka thandizo lomwe lidapereka kuti Nice Trust igwirire ntchito zake zophunzitsa anthu kwa zaka zingapo.
| 10 |
Aoloka yorodani pamtsinje wa ruo Sukulu adalekera sitandade 4, kuwerenga nkomuvuta, koma kuwerengera ndalama kwa iye si nkhani. Ngakhale sukulu sadapite nayo patali, ntchito zake zikuthandiza anthu oposa 15 000 kwa T/A Mlolo mboma la Nsanje.
Chisale watuluka nkumangidwanso Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Ndi manja ake, mnyamatayu wamanga mlatho wa mamita 100 pamtsinje wa Ruo womwe anthu ambiri tsopano akuolokerapo tsiku ndi tsiku.
Mavuto atha: Ana asukulu, abizinesi ndi opita kuchipatala tsopano akutha kuoloka Ruo Nzoonadi, aja adati wopusa adaimba ngoma, ochenjera navina sadaname, tikatengera nkhani ya Laitoni Anoki, wa zaka 28, yemwe amachokera mmudzi mwa Khasu.
Ngati ena poyamba ankamutenga ngati wopanda phindu kaamba koti sukulu adatulukira pawindo, lero wasanduka momboli wawo. Ngakhale mafumu mderali akuvomereza kuti Anoki ndi ngwazi ya anthu kumeneko.
Njinga zamoto, zakapalasa komanso matumba a chimanga ndi zigubu za mafuta zikuoloka pamenepa popanda vuto.
Zonse zidayamba ndi madzi osefukira amene adavuta chaka chino. Chifukwa chosefukira mtsinje wa Ruo udaiwala khwawa nkuphotchola. Midzi yambiri idakokoloka, anthu makumimakuni adafa pangoziyo, osanena za ziweto ndi kukokoloka kwa minda.
Mtsinjewu udachititsa kuti anthu azilephera kupita kuchipatala ku Makhanga Health Centre, kusukulu yasekondale ya Makhanga, komanso kumsika wa Admarc mderali. Mtsinjewo wachitanso malire ndi dziko la Mozambique komwe anthuwa amapitako kukasuma chimanga kutsatira njala yomwe yagwa mbomali komanso ndiko kukuchokera mafuta ophikira.
Poyamba, anthuwa ankangoyenda osaoloka mtsinje chifukwa padalibe mtsinje. Ankaoloka Ruo pokhapo ngati akupita ku Mozambique.
Anthu a derali, kudzera mwa mafumu awo, akhala akupempha mabungwe komanso boma kudzera mwa phungu wawo Esther Mcheka Chilenje kuti awamangire mlatho pa Ruo koma kuli chuu.
Ngoziyi itangochitika, phungu wathu adabwera kudzationa ndipo adatitsimikizira kuti atimangira mlatho poona kuti sitingathenso kupita kuchipatala ndi madera ena. Koma mpaka lero sitikudziwa kuti lonjezoli litheka liti, adatero gulupu Manyowa.
Adadza ndi nzeru zomanga mlatho: Anoki Manyowa akuti anthu pafupifupi 15 000 ndiwo akhudzidwa mwa magulupu 13 onse a mwa T/A Mlolo.
Ataona kufunika kwa mlatho pamtsinjewu Anoki, ngati wamisala, adayamba kudula mitengo nayamba kukhoma mlathowo.
Pocheza ndi Msangulutso, mnyamatayu akuti adayamba ntchito yomanga mlathowu mvula ili pafupi kusiya, apo nkuti madzi akulekeza mkhosi.
Poona kuti ntchito indikulira ndidakopa anyamata ena kuti tithandizane. Tidalipo 8. Tidadula mitengo ndipo ina ndimachita kugula. Ndidakagula misomali, ina anthu adangotipatsa koma ina ndidachita kukongola pamtengo wa K40 000.
Zida zitakwana, tidayamba kukhoma mitengo pamadzipa. Timasongola kaye mitengoyo ndi kukhoma ndi hamala. Ntchito idalipo chifukwa madzi nkuti ali ambiri moti mwina amandilekeza mkhosi, adatero Anoki.
Pakutha pa miyezi itatu, mlatho wotalika ndi mamita 100 nkuti utatha ndipo anthu adayamba kuolokerapo.
Ngakhale tidamaliza komabe tsiku lililonse timaugwiragwira chifukwa pena umapeza msomali wazuka kapena mtego wachoka chifukwa pamadutsa anthu ambiri, adatero.
Lero Anoki wayamba kudyerera thukuta lake pamlathowu.
Munthu mmodzi amalipira K100 kupita ndi kubwera. Njinga yamoto timalipitsa K200, thumba lolemera ndi makilogalamu 50 timalipitsa K100, koma opita kuchipatala sitimawalipiritsa.
Patsiku Anoki akuti amapanga ndalama yosachepera K20 000. Sungadabwe kumuona mnyamatayu lero akutuluka mnyumba yanjerwa zootcha komanso yamalata, ndipo wagula mbuzi zingapo, kumunda waikako aganyu.
Kupatula apo, Anoki walemba ntchito anyamata asanu kuti azithandizira pamlathowo.
Anthu amaoloka ndi usiku womwe. Komanso pakufunika anthu olondera ndiye pali anyamata asanu amene akuthandiza. Ena amathandizira kuolotsa njinga. Patsiku ndikumawalipira K1 500 aliyense, adatero Anoki.
Anyamata amene adamanga nawo mlathowu akulandiranso zawo. Chomwe tapanga nkuti tizigawana sabata yolandira ndalamazi. Sabata ino ndilandira ndineyo, ndiye kuti wina alandira sabata yamawa.
Mmene tikuteremu ndiye kuti ndalama yokonzetsera mlathowu imakhalanso tasunga. Mukuona anthu akubweretsa mitengo, amenewa tikufuna tiwagule kuti zida zikhale zokwanira, adatero Anoki, uku akusintha ndalama zopatsa kasitomala.
Mphindi 20 zomwe tidakhala pamlathowo, onyamula zigubu za mafuta ndi matumba a chimanga kuchokera mdziko la Mozambique, opita kuchipatala komanso ophunzira ndi alimi ndiwo amaoloka mowirikiza.
Lero dzina la Anoki silisowanso mmudzimo. Gulupu Manyowa akuti alibe naye mawu mnyamatayu.
Mtsinje umenewu ndi waukulu, anthu 9 a mmudzi mwanga adapita akuoloka mtsinjewu. Lero tikutha kumaoloka mwaufulu, zomwe sitidaziganize chifukwa maso anthu adali kuboma. Izi zidatipatsa chimwemwe.
Pano tikumapita kumsika, kusekondale, ku Mozambique komanso ku Admarc mopanda vuto. Simungapite ku Bangula kuchokera kuno osadutsa pamlathowu, adatero Manyowa amene akuti masiku ena samalipitsidwa.
Mkulu wina amene ankapita kuchipatala ndi bambo ake adati mlathowu wawathandiza kopambana.
Mkuluyu, Gift Filipo, wa mmudzi mwa James kwa Gulupu Mchacha, akuti pachipanda mlathowu sakadapita ndi bambo ake kuchipatalako.
| 15 |
Ulimi wa mthirira nchuma Tikudziweni Ndine Moffat Mtalimanja ndipo ndi mkazi wanga Effie timachokera mmudzi wa Kaunde, ku Namadidi kwa Senior Chief Mlumbe mboma la Zomba. Ndife alimi amene timaweta ziweto zosiyanasiyana kuphatikizaponso kuchita ulimi wa mbeu zosiyanasiyana. Pa ulimi wa mbeuzi timachita onse wa mvula komanso wa mthirira.
Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Ulimi wa mthirira mudauyamba liti? Ulimiwu tidauyamba mzaka za mma 1970 pamene bambo amagwira ntchito ku Portland Cement ku Changalume. Chimene chidatiyambitsa kuchita ulimiwu ndi kupewa kugula ndiwo za masamba omwe zimene timaona kuti tikhonza kuzikwanitsa kumazilimira ndi kumadzidyetsa tokha.
Mkati mwa njira ndi pamene tidaona kuti mbeu za masambazi ndi mpamba waukulu chifukwa anthu ozungulira kuno adayamba kumabwera kumatigula ndi pamene tidaonjezera moto kumachita ulimiwu mwakathithi.
Ndi mbewu ziti zimene mumalima? Masambawo amafunika kuthirira Tomato, kabichi, anyezi, beetroot, brocolli, nyemba, chimanga ndi mbeu zina zambiri malinga ndi kukonda kwa anthu ogula.
Kuchokera 1970 pali mtunda ndithu, chinsinsi chake chagona pati kuti muzilimabe mpaka pano? Ulimi wa mthirira uli ndi chuma chobisika chimene alimi ambiri sanachitulukire. Mnyengo ya mvula, mbeu zambiri zikalimidwa ndipo zikakhwima pamsika zimakhala mbweee ndipo zimagulitsidwa pa mitengo yolira pamene mnyengo yopanda mvula ndi mmene za masamba zimakhala zochepa koma ogula ndi ambiri. Apa mpamene mlimi wa nzeru amayenera kugwira mpini.
Ndi phindu lotani limene mumapeza mu ulimiwu? Phindu limene timapeza mulimvetsetse ndi kuwerengera kuti anthu pakutha pa mwezi amagwiritsa ntchito ndalama zingati pogula tomato ndi masamba kuti azidya tsiku ndi tsiku pakhomo pawo. Mukhoza kuona kuti amagwiritsa ntchito ndalama zambiri zimene akanati masambawa alima okha ndiye kuti ndalama zimenezi akanapangira zinthu zina zofunika pakhomo pawo.
Pachifukwa chimenechi, sitigula chilichonse chokhudza masamba komanso timagulitsa masambawa kusonyeza kuti timapha mbalame ziwiri ndi ulimi wa nthilirawu. Pa chifukwa ichi ndalama zimene taziteteza posagula masambazo timapangira chitukuko chosiyanasiyana pakhomo pathu pano.
Ndi zovuta zotani zimene mukukumana nazo ndipo mumathana nazo motani? Vuto lalikulu ndi madzi. Malo amene timalimawa tidayetsetsa kusaka madzi kuti tikumbe chitsime koma madzi sanapezeke. Kotero madzi adapezeka patali ndithu pamene tinakumba chitsimecho choncho tinalemba ntchito anthu amene amakatunga madzi pa chitsimepo ndikumazathira mu migolo imene timatungamo ndi kumathilira mbeuzi.
Pakadali pano tili ndi malingaliro opeza makina opepera madzi amene adzipopa madzi pachitsimepo ndikumabweretsa ku dimba kuno kuti ulimiwu ufike pa mponda chimera.
Ulimi wa mthirira uli ndi phindu? Kwambiri. Mwachitsanzo, talima tomato mitengo 650. Ndipo mbeu yakeyi imabereka bwino chifukwa imatha kubereka tomato osachepera 50. Ndiye pa mitengo 650 mtengo uliwonse ubereke tomato osachepera 50 ndiye mwachitsanzo tomato mmodzi adzigulitsidwa K50 mukapanga masamu mukupeza bwa? Komanso kabichi amene timalima ndi mbeu yaikulu bwino amene mmodzi timagulitsa K250 ndiye ngati tadzala oposa 100 mukhoza kuona kuti paphedwa makwacha ochuluka bwanji? Chimanga chachiwisi nacho cha nthilira chikachita bwino chimasanduka chitsulo cha ndege pa msika, kotero ngati walima chochuluka mlimi satola chikwama? Mbeu zina monga nyemba, tanaposi, beetroot, brocolli nazo ndi golide kale mchilengedwe chake kotero ngati mlimi akulima zimenezi mwakathithi umphawi ungakhale ndi ulamuliro pa moyo wake? Ngati dziko titani kuti ulimi wa nthilira udzipindulira dzikoli? Chofunika alimi asinthe kaganizidwe ndipo avomereze kuti ulimi wa nthilira ndi ulalo opititsa chuma chawo chomwe komanso cha dziko pa tsogolo. Zimatiwawa kumaona munda umene uli pafupi ndi msinje wakuti suphwera koma palibe chikulimidwapo kudikilira mvula basi uku kumakhala kuseweretsa ndalama.
Boma komanso mabungwe amene amalimbikitsa ulimi ayedzeke chidwi chawo powapatsa mphamvu alimi ndi zipangizo zimene zingatakasile ulimi wa nthilira kuti upite pa tsogolo chifukwa nthaka ndi madzi mdziko muno ndi zambiri. Ngati ife tikukwanitsa kuchita ulimi ndi madzi a pa chitsime tsono amene minda yawo ili pafupi ndi madziyo angapindule bwa? Tilimbikitsenso achinyamata kuti pamene akusakasaka ntchito zamu ofesi aganizirenso zochita ulimi chifukwa ulimi ukhoza kusintha miyoyo yawo nkuthwanima kwa diso.
Ndi ubwino wotani umene ulipo ochita ulimi ngati banja? Pamakhala kudalirana kwakulu, mwachitsanzo, ulimi umenewu amene amakhala patsogolo ndi mayi ndipo ine ndimangothandizira mapeto ake nzeru zawo ndi zanga tikaziphatikiza pamodzi ndi zimene zimachititsa kuti zinthu zizitiyendera bwino chotere. Muli mphamvu mukudalirana.
| 2 |
Wa gulewamkulu atuluka pa belo Bwalo la milandu mboma la Kasungu lapereka belo kwa munthu yemwe adayerekeza kuvala gulewamkulu ndipo akuganiziridwa kuti adagwirira mwana wa zaka 7 pomwe mwanayu amachokera kusukulu pamodzi ndi anzake ena awiri pa mtsinje wa Mkazimasika mbomalo.
Gule wa mkulu Apolisi a mbomalo adagwira mnyamata wa zaka 16 ndi kumutsekera mchitokosi sabata ziwiri zapitazo pomuganizira kuti ndiye adapalamula mlanduwo atavala gulewamkulu.
Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndipo mnyamatayu adadziwika chigoba chomwe adavala chitagwa pomwe adali mkati mogwirira mwanayo.
Malinga ndi mneneri wa polisi mbomalo Harry Namwaza, mnyamatayu adavomera kuti adapalamula mlanduwo pamaso pa woweruza milandu Damiano Banda.
Namwaza adati pakadalipano mnyamatayo wapatsidwa belo poyembekeza lipoti kuchokera ku nthambi ya boma yowona za chisamaliro cha anthu.
Malinga ndi malamulo oteteza ana mdziko muno, mwana saweruzidwa pamlandu nthambi ya bomayo isanapereke lipoti lokhudza mwana amene wapalamula mlandu.
Koma mkulu wa nthambiyo mboma la Kasungu, John Washali adati sakudziwa kalikonse za nkhaniyo ndipo sadalembe lipotilo.
| 7 |
Apolisi, Asilikali Ati Akhwimitsa Chitetezo mu Nthawi Yosayendayenda Apolisi mdziko muno mogwirizana ndi asilikali a nkhondo, anenetsa kuti apereka chitetezo cholimba motsatira malamulo a dziko lino amene amawalora kuti awonetsetse kuti mdziko muli bata ndi mtendere komanso kuti aliyense akutsatira malamulo.
Anayitanitsa msonkhano wa atolankhaniwo-Mwapasa Wogwilizira udindo wa mkulu wa apolisi mdziko muno a Danken Mwapasa limodzi ndi mkulu wa asilikali a nkhondo mdziko muno a Peter Lapken Mathanga anachititsa msonkhano wa atolankhani omwe wachitika lachinayi mu mzinda wa Lilongwe, pokonzekera masiku 21 osayendayenda omwe pulezidenti Peter Mutharika walengeza kuti ayambira pakati pa usiku wa loweruka sabata ino mpaka pakati pa usiku wa pa 9 May chaka chino.
Nthambi ziwirizi zapempha anthu mdziko muno kuti atsatire bwinobwino malamulo omwe aikidwa ponena kuti opezeka akuyenda mopanda chilolezo adzalangidwa moyenera monga waphwanyira malamulowa.
Pamenepa atolankhani anafunitsitsa kudziwa kuti anthu adzalandira chilango chotani potengera kuti ndendenso za dziko lino, potengera nkhani ya Corona Virus yomweyi sikukuyenera kuti kudzaze. Iwo anayankhapo kuti anthuwa adzatengeredwa kupolisi ndipo mwachangu adzakawonekera ku bwalo la milandu komwe adzikalandira chilango mwachangu.
Nkhani ina yomwe inamanga nthenje kumeneku ndiyokhudza ntchito zakumunda pamene anthu ena akukololabe mbeu zawo. Pamenepa akuluakuluwa ati mpofunika anthu afunse komwe akuyenera kuti akatenge chilolezo choti agwirire ntchitozo momasuka.
Iwo anenetsanso kuti sikufuna kwawo kuti adzagwire ntchito yawo mwa nkhanza koma mokhala kumbali ya wanthu komanso anenetsa kuti anthu akuyenera kutsatira malamulowa kaamba koti ndi anthu omwewo amene apindule ndi mfundozi.
| 7 |
World Vision Yapempha Anthu Alimbikitse Ukhondo Bungwe la world vision mboma la Dedza lati anthu akuyenera kumadzisamalira nthawi zonse pofuna kupewa kachilombo ka Coronavirus.
Mkulu wa bungweli mboma la Dedza a Thokozani Chibwana amalankhula izi pomwe bungweli limapereka katundu wosiyanasiyana pa chipatala cha Dedza wa ndalama zosachepera 13 Milion Malawi Kwacha.
A Chibwana ati bungwe la World Vision ndilokhudzidwa ndi mmene matendawa akufalikira ndipo anawona kuti ndi koyenera kuti achitepo kanthu pofuna kupewa mliriwu.
Mukudziwa kuti ntchito imeneyi kuti iyende imafunika kuti tikhale ndi zipangizo zokwanira monga ma Anti-Biotics, ma glove, ndowa ndi zina zambiri zoti zitithandize pa nkhani za ukhondo makamaka madera omwe tikugwiramo ntchito mboma lino, anatero a Chibwana.
Mwazina bungweli lapereka mankhwala, ma pail 20, sopo 50, ma glove okwana 7 thousand komanso zovala zozitetezera zokwana 1500 kwa anthu owona za umoyo mbomali.
| 6 |
Aletsa zionetsero za madzi Mkulu wa bungwe loona za ufulu wa ogula la CAMA John Kapito Lachinayi adalepheretsa zionetsero ngakhale mpaka lero anthu ozungulira Blantyre akusaukirabe madzi.
Chionetserochi chidakonzedwa ndi mkulu wa pamene amati ayende kukadandaulira kampani yogulitsa madzi ya Blantyre Water Board (BWB).
Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Zionetserozi zimadza pamene kwatha mpaka miyezi iwiri madzi mmadera ena amumzindawu asakutuluka mumzindawu. Koma Kapito adati: Tidakumana ndi akuluakulu a bungweli ndipo atitsimikizira kuti ayamba kupereka madzi. Taona kuti palibenso chifukwa chochitira zionetsero pamene atilonjeza kuti ayamba kupereka madzi, Kapito adauza atolankhani.
Koma pofika Lachinayi, madera ambiri mumzinda wa Blantyre madzi adali akuvutabe zomwe zidachititsa anthu ena kukwiya nazo.
Mmodzi mwa anthuwo, Rawjazz Siula akuti ndi bwino tsiku lina kudzachita zionetsero zosagwirizana ndi bungwe la Cama popusitsa Amalawi.
Basi bwana Kapito akatinamize pamene tikunena kuti patha sabata zambiri madzi asakutuluka? Bwanji sadayitane anthu omwe amawauza kuti ayende pamsewu kuti zionetsero zalephereka? sakumvetsa Siula.
Mwayi Mbwelera akuti nkhani ya madzi yavuta kotero zionetsero si bwenzi zitalephereka. Kuno ku Mbayani anthu tikusaukira madzi, nthawi yonseyi bwanji samatibweretsera madziwo? Zalakwika, adatero.
| 2 |
Zungulizunguli mu Lilongwe Abale anzanga, inetu ukwati, nkhani ya ukwati, sindikamba nawo. Nkhani imeneyi, kwa ine ndimangoionera apo!!! Chifukwa chake nachi: Pali ana ena amene amaganiza kuti mayi awo ndi amami, chonsecho mayi awo ndi anti. Komanso pali ana ena amene amaganiza kuti bambo awo ndi adadi chonsecho ndi ankolo.
Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Musayerekeze kundifunsa kuti ndikutanthauza chiyani chifukwa sindikuyankhani. Ndakwiya nanu chifukwatu ndili muno mu Lilongwe momwe ndimakumana ndi anyamata ena.
Musayerekezenso kundifunsa ngati nkhani yake inali ya ukwati kapena ayi. Mukadziwa mukufuna mutani? Ndidatsika basi ya Lilongwe tsikulo chifukwa Abiti Patuma adandiuza kuti mzindawo uvuta.
Abale anzanga nanga nkadatani? Nkadachitanji chifukwatu ena adandiuza kuti uku nkwa gule ndipo ukwatiwo ndi wa abale.
Mwinatu sindidakuuzeni. Nthawi ija ankamanga ukwati anyamata aja, nthawi ya Moya Pete, ine ndidali pomwepo limodzi ndi Abiti Patuma.
Inde, anyamata aja adatchuka.
Chongoti mu Lilongwe fikeni, abale anzanga, inetu zikwama ndimachita kupanira ngati chiyani kaya! Tidayenda kamtunda ndithu ndipo tidaona umo apolisi amatapira ndalama muno mu Lilongwe: Kwa Biwi, inde Lower Biwi! Kugonetsa abambo olemekezeka pansi ati vakabo yawatapula! Umo mu Devils Street, ati kumene chiwanda cha Satana chidafikira, asungwana kukopa abambo; anyamata kufwamba abambo ndipo ana kutoleza zimene ataya abambo.
Lilongwe iyooo! Za kwinako sindikamba. Ati Kumpanda kwa Mafumu, inde ku Side kofikira Madonna; apa paakazembe ngakhalenso kumabedi ndiye eeeeh! Nkhani ili apa ndi ya anyamata amene tidawapeza akuchita zawo. Musadandaule, aka si koyamba, komanso kumbukirani anyamata a mu Mchesimu tsiku lina adafuna kuphwanya hotela ati chifukwa mwini hotela adazembetsa ana ena! Lilongwe iyooo! Tsono nkhani yakula apa ndi yakuti Moya Pete tsono wakumana ndi zija adakumana nazo Mfumu Mose nthawi ija ankafunsidwa ngati Mustafa angasiyire mngono wake Ajibu mpando woyanganira ife ojiya, osolola ndi osenza pano pa Wenela.
| 15 |
Phindu kawawa ndi ulimi wa tsabola Akulipirira ana awiri ku sekondale; wagula mbuzi 19 ndi nkhuku 30. Njinga, ziwiya za pakhomo komanso banja lake silikugona ndi njala. Nkhani ya Jimmy Maliwu, mlimi wa tsabola ku Mulanje ndi chitsanzo kuti ulimi wa tsabolawu ndi kawawa. BOBBY KABANGO akucheza ndi mlimiyu: Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Maliwu: Ndidagulitsa mosavuta Wawa achikumbe Wawa, imani komweko musafike pafupi, kuno ndi kwa alimi okhaokha.
Kuli chiyani mukuchita kukanizira? Tikusankha tsabola ndiye mphepo yake inuyo simungayandikire, mukuona aliyense akungoyetsemula.
Ndiye tidziwanetu Ndine mlimi wa tsabola, dzina ndine Jimmy Maliwu wa mmudzi mwa Sazola kwa Senior Chief Mabuka mboma la Mulanje.
Mudayamba liti ulimiwu? Mu 1999 ndi pamene ndidayamba kulima tsabola.
Chidachitika nchiyani kuti muyambe ulimiwu? Pa nthawiyo nkuti ndikulima chimanga komanso mbewu zina. Ndiye ndinkafuna ndichite ulimi wina womwe ndizipezerapo ndalama. Apa ndi pamene ndidasankha tsabola.
Chifukwa chiyani mudasankha ulimi wa tsabola? Ndinkafuna ulimi wa fodya, koma kuno sachita bwino. Ulimi wa tsabola ndi omwe ndidaona kuti akuphamo ndalama.
Mudayamba bwanji? Ndidalima mizere yochepa, ndimafuna kuti ndione ngati ndingathe komanso ngati msika wake uchite bwino. Zidayenda koma osati kwambiri, ndidaikamo chidwi.
Chidayenda nchiyani? Kumunda zidatheka komanso pamsika ndidagulitsa mosavutika ngakhale mtengo wake udali wolira.
Mtengo udali bwanji? Ndidagulitsa K39 pa kilogalamu pamene alimi ena amagulitsa K50.
Kuchoka 1999 kufika lero, ulimiwu ukuyenda bwanji? Mitengo ndiyo yakhala yovuta koma kumunda ndiye zonse zili bwino. Ndidaonjezera munda ndipo pano ndikulima wokula ndi mamita 35 mulitali ndi 17 mlifupi.
Munda umenewu mukukolola wochuluka bwanji? Ndikumapeza tsabola makilogalamu 150 ngati mvula yagwa bwino komanso ngati matenda sadafike.
Chaka chatha zidayenda bwanji? Nanga pamsika padali bwanji? Chaka chatha ndidakumana ndi vuto la matenda ndiye ulimi udavuta moti ndidapeza makilogalamu 45 okha chifukwa alangizi adafika mochedwa. Pamsika ndiye zidali bwino chifukwa amagula K2 500 pa kilogalamu.
Ndi matenda ati amene adavuta? Tsabola amapanga zilonda komanso mitengo imauma. Zikatere zimakhala zovuta kuti abereke bwino. Panopa matendawa tawakonzekera chifukwa tidali ndi maphunziro a momwe tingathanirane ndi matendawa. Koma vuto lomwe lidalipo kuti tikumane ndi matendawo nchifukwa cha manyowa amene tidagwiritsira ntchito.
Tsabola wakupindulirani bwanji? Muli ndalama, chaka chatha ndidapeza K112 500 kuchokera mmakilogalamu 45 amene ndidakolola. Ndagula mbuzi 19 komanso nkhuku 30. Ndili ndi ana atatu, mmodzi ali Fomu 2 wina 4 ndi wina ali ku pulaimale. Onsewa ndalama zake zikuchokera mu tsabola. Sindinagonepo ndi njala chifukwa ulimiwu umandisuntha.
Tifotokozereni za kumunda, kuli bwanji pano? Panopa tikuwokera pamene mitengo ya chaka chatha tikuthyolera kuti ipange nthambi.
| 4 |
Nkhanza za mbanja zikupitirira kuchuluka Mzimayi uyu adakhapidwa ndi mwamuna wake ku Thyolo Ngakhale chaka ndi chaka dziko lino limakhala ndi masiku 16 othana ndi nkhanza mogwirizana ndi maiko ena padziko lapansi, zenizeni sizikuoneka pamene nkhani za nkhanza mmaboma zakula msinkhu.
Malinga ndi mneneri wa polisi Rhoda Manjolo, mu 2013 anthu 4 499 adachitiridwa nkhanza kuchokera mwezi wa January mpaka June.
Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Chaka chino, Manjolo wati kuyambira January mpaka September nkhani zotere zakwana 9 842, chomwe ndi chiwerengero chokwera kuyerekeza ndi 2013.
Nkhani zoti mayi waphedwa ndi mwamuna wake kapena bambo waphedwa ndi mkazi wake nazonso zakhala zikumveka.
Komatu izi zikuchitika pamene chaka ndi chaka amabungwe padziko lapansi amakhala ndi kampeni yomemeza anthu kuti asiye nkhanza kuyambira pa 25 November mpaka pa 10 December.
Lipoti lomwe unduna wa za jenda ukuyembekezereka kutulutsa sabata ikudzayi ukusonyeza kuti nkhani zophana ndizo zidakula msinkhu mchakachi.
Mlembi muundunawu, Dr. Mary Shawa, dzana Lachinayi adakana kuuzaTamvanizomwe zili mlipotimo ponena kuti tidikire sabata ikudzayi.
Sindinganene momwe nkhanza zachitikira mchaka chino, komabe pali kusintha kuti anthu akutha kukanena kupolisi akachitiridwa nkhanza. Abambo tsopano ayamba kukadziwitsa apolisi pamene achitiridwa nkhanza, adatero Shawa pokambapo pangono za lipotilo.
Chaka chino ndiye pali nkhani zophana zoposa zisanu. Iyi ndi nkhani yachisoni kwambiri komanso tidali ndi nkhani yomwe amayi atatu adagwiririra mnyamata wa zaka 13; abambonso aphedwa ndi akazi awo. Mumva zambiri tikatulutsa lipotili pa 9 December pano, adawonjeza Shawa.
Mkulu wa bungwe lomwe limalimbana ndi kuthetsa nkhanza la Umunthu Foundation, David Odali, adati nzachisoni kuti nkhanza zikungochulukira ngakhale iwo ali kalikiriki kudziwitsa anthu kuti asiye mchitidwewu.
Nzachisoni kumamva nkhani ngati izi pamene ife tikuyenda maboma onse kudziwitsa anthu koma nkhanza zikupitirirabe, adadandaula Odali.
Koma Odali akuti pali mfundo zinayi zomwe zikuchititsa kuti mchitidwewu ukhale ukukulirabe. Iye wati mchitidwe wa amayi ena amene amati akavulazidwa ndi amuna awo amakathetsa nkhani kubwalo kuti isapitirire ndicho chimodzi chikuchititsa kuti mchitidwewu uzipitirira.
Munthu amuvulaza koma akuti nkhani ithe ponena kuti ndi mwamuna wake, kodi izi zingapereke phunziro lanji? Amayi aphunzire kulolera kuti lamulo lizigwira ntchito yake ngati munthu wawavulaza, adatero Odali.
Iye adati mfundo ina ndi kuti anthu ena salolanso kuti nkhani zotere zikachitika zizikanenedweza kupolisi ponena kuti ndi nkhani ya mbanja yomwe imayenera ikambidwe ndi bambo kapena mayi wa pabanjapo.
Odali watinso ndi bwino abambo azikanena kupolisi ngati achitiridwa nkhanza. Abambo ena akachitiridwa chipongwe ndi mkazi wawo samanena, iwo amati akupirira koma akuchulukitsa mchidwewu. Pasakhale kupirira pakati pa abambo, adatero.
Komabe iye adayamika kuti ngakhale nkhanzazi zikutenga malo, anthu ambiri aphunzira kumakanena kupolisi pamene achitiridwa nkhanza kusiyana ndi kale pamene zimathera mnyumba kapena kwa amfumu a deralo.
Ndipo polankhula pomwe bungwe la amayi a Chikhristu la Young Women Christian Association (YWCA) limakhazikitsa ntchito yothandiza asungwana kuzindikira za ubereki ku Mulanje Loweruka, nduna ya za jenda, Patricia Kaliati, adati nkhanza kwa amayi ndi asungwana zikuchuluka kwambiri. Iye adati amayi ambiri akuchitiridwa nkhanza chifukwa chosowa maphunziro.
Asungwana ambiri atalimbikira maphunziro, nkhanza zikhoza kuchepa chifukwa akhoza kuzindikira ufulu wawo. Nchifukwa chake tikubweretsa lamulo lakuti ana asamakwatiwe asanafike zaka 18.
Mafumu ali ndi udindo waukulu woteteza ana pokhazikitsa malamulo apadera. Mwachitsanzo, madera ena mafumu adakhazikitsa malamulo akuti makolo amene akusiyitsa ana sukulu kuti akakwatiwe amalipitsidwa dipo, adatero Kaliati.
| 15 |
Maepiskopi Akatolika Awunikira Akhritsu Awo za Mtsogoleri Woyenera Kumusankha Maepiskopi a mpingo wa katolika mdziko muno atulutsa kalata yomwe mwa zina yaunikira dziko ndi akhristu a mpingowu zina mwa zomwe akuyenera kudziunika pofuna kukonza maziko abwino a dziko ndi miyoyo yawo.
Kalatayi yayamba ndi mau a mbukhu loyera kuchokera pa Mateyo mutu wa 20 kuyambira ndime ya 25 mpaka ya 27, pomwe pali mawu akuti Yesu adawaitana ophunzira ake nawauza kuti mukudziwa kuti olamulira amadyera anthu awo masuku pa mutu. Koma pakati pa inu zisamatero ayi.
Aliyense ofuna kukhala wamkulu akhale mtumiki wanu ndipo aliyense wofuna kukhala mtsogoleri pakati panu, akhale kapolo wanu.
Alemba chikalatacho-Maepiskopi aku Malawi Malinga ndi kalatayi yomwe mutu wake ndi kusindika za kufunika kosintha zinthu ndi kuyambanso moyo watsopano mMalawi, yalimbikitsa anthu kuti atenge gawo posintha zinthu mdziko muno.
Chisankho chatsopano cha mtsogoleri wa dziko chomwe chikudzachi ndi njira imodzi yomwe aMalawi angasinthire zinthu zomwe zakhala zisakuyenda bwino. Ofunika kusankha atsogoleri okhawo omwe angathandize aMalawi kuti akhale amodzi ndi ogwirizana, ochita zinthu mwadongosolo, owopa Mulungu, olemekza malamulo a bwalo la milandu komanso osakondera chigawo kapena chipani, chatero chikalatacho.
Iwo adandaulanso ndi khalidwe losankhana mitundu lomwe lakhala likuchitika, zipolowe pa ndale komanso kuchuluka kwa katangale ndi kusalangidwa kwa anthu akaphwanya malamulo ndipo alimbikitsa kampeni yamphamvu yothana ndi nthenda ya COVID-19.
Kalatayi ndi ya namabala 26 kulembedwa ndi maepiskopi a mpingo wa katolika mdziko muno kuchokera mu 1961 pomwe analemba kalata yoyambilira.
| 11 |
Agundidwa akuthawitsa katundu wakuba Bambo wina wagundidwa ndi galimoto ku Mzuzu pomwe amathawitsa mapaketi awiri a khofi omwe amamuganizira kuti adaba pa Mzuzu Coffee Den.
Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Bamboyo, yemwe ndi Laston Kaunda wa zaka 32 ndi wochokera mmudzi mwa Chiphanzi, T/A Nkumbira mboma la Nkhata Bay.
Mneneri wapolisi mumzinda wa Mzuzu, Patrick Saulosi, adati mnyamatayo adapita ku Coffee Den mmawa wa Lachiwiri sabata yatha ndi nsuweni wake komwe adakanyamula mapaketi a khofiwo.
Woganiziridwayo akutuluka mu Coffee Den muja adatuluka ndi mapaketi awiri a khofi osalipira. Mnyamata wogwira ntchito pamalopo ataona zomwe amachita Kaunda adayamba kumuthangitsa, adafotokoza Saulosi.
Saulosi adati pa nthawi yomwe Kaunda amafuna kuoloka nsewu galimoto idamuomba ndipo iye adavulala kwambiri mwendo.
Iyeyo ali kuchipatala cha Mzuzu Central Hospital (MCH) koma akangotuluka kuchipatalako atengedwa ndi apolisi pamlandu wakuba, adatero Saulosi.
Saulosi adati kaamba ka kuchepa kwa mlanduwo palibe wapolisi amene akudikirira Kaunda kuchipatala podikirira mlandu.
Msangulutso utapita kuchipatalako udakumana ndi Kaunda yemwe akadali mchipatala kulandira thandizo.
Kaunda adati sakukumbukira chilichonse chomwe chidachitika patsikulo chifukwa adali ataledzera kwambiri.
Sindikudziwa chomwe chidachitika ndidangozindira kuti ndili kuchipatala kuno, iye adayankha motero.
| 7 |
Apolisi sakununkha kanthu pa chitetezo Ngombe zayangana kudazibomu! Ubale wa anthu ndi apolisi wafika pa wa mphaka ndi galu moti apolisi sakununkhanso kanthu pa ntchito yawo yoteteza anthu ndi katundu wawo. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Asirikali a Malawi Defense Force kusungitsa mtendere pa zionetsero Sabata zitatu zapitazo agogo 6 adaphedwa mboma la Karonga powaganizira kuti ndi athakati.
Apolisi atapita kuti akagwire anthu omwe adachita izi, adawathamangitsa ndi miyala, mipini, mipaliro ndi zibonga moti adalephera kukwaniritsa zolinga zawo.
Aka sikadali koyamba izi zichitike mbomalo. Chaka chathachi apolisi kwa Nyungwe adamenyedwa ndi anthu atatsekera anthu omwe adakatenga namulondola kuti adzawathandize kugwira mfiti mderalo.
Nako ku Ntchisi anthu okwiya adapha agogo awiri powaganizira kuti adalodza mnyamata wina wa zaka 15 mmatsenga. Ngakhale izi zidachitika mwezi wa October chaka chatha, mneneri wa polisi mbomalo Richard Kaponda wauza Msangulutso kuti mpaka lero palibe yemwe wamangira mokhudzana ndi nkhaniyo.
Nako ku Neno komwe anthu adapha nkhalamba zomwe amaziganizira kuti ndi mfiti, apolisi adachita chidodo kuti akagwire ndi kuzenga mlandu anthu omwe adachita izi.
Anthu adali ndi mkwiyo waukulu moti apolisi amachita mantha kuti awagwire. Nazo zionetsero zosonyeza kukwiya ndi momwe bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) lidayendetsera chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino zaikanso pambalambala kufooka kwa apolisi moti boma lidapempha asirikali a nkhondo a Malawi Defense Force (MDF kuti awathandize kuteteza anthu ndi katundu wawo.
Mkulu wa apolisi Duncan Mwapasa adavomera pa msonkhano wa atolankhani kuti apolisi ali ndi mphamvu zochepa ndipo sangakwanitse kuteteza anthu omwe akuchita zioneserozo.
Apolisi akhala akuona mbwadza pa zionetserozo. Mmalo moti apolisi azisaka amtopola, anthuwo ndiwo akumasaka apolisi nkumawavula, kuwamenya, kuwalanda mfuti, kuwatsatira mmakomo nkukachita chipongwe mabanja awo moti wapolisi wina, Imedi Usumani, adaphedwa.
Kuphwando la kumapeto a chaka chino, mkulu wa apolisi wa mchigawo chakummwera Sladge Yousuf adati ntchito yoteteza anthu ikuvuta kaamba kakusakhulupirirana pakati pawo ndi anthu akumudzi.
Yousuf adati chodandaulitsa kwambiri ndi kuphwanyidwa, komanso kuotchedwa kwa mapolisi mdziko muno.
Amalawi okwiya akumatsatira munthu yemwe ali mchitokosi mpaka kukaphwanya kapena kuotcha polisi nkumutulutsamo.
Nkhamenya ku Kasungu ndi Chilobwe ku Blantyre ndi ena mwa mapolisi omwe adaphwanyidwa kaamba kosemphana Chichewa pakati pa apolisi ndi anthu akumudzi.
Mmodzi mwa aphunzitsi a pa sukulu ya ukachenjede ya University of Livingstonia George Phiri adati apolisi asuluka chifukwa cha katangale, komanso utsogoleri wa dziko lino omwe wakoledzera moto kuti ntchito.
Phiri adati kwakhala kukutuluka malipoti ambiri a katangale yemwe apolisi amachita zomwe zamachititsa kuti Amalawi asowe chikhulupiriro mwa apolisi.
Tsopano nkhani za katangale zonsezi zikatuluka, tikuona kuti palibe chomwe atsogoleri akuchitapo pofuna kuthana naye.
Pachifukwa ichi anthu angoganiza zotengera malamulo mmanja mwawo, iye adatero.
Phiri adati pakadali pano nzovuta munthu kuthawira ku polisi kuti ukapezeko chitetezo chifukwa anthu akakwiya, akumathamangitsa omangidwayo komanso apolisi omwe akumuteteza.
Atsogoleri a dziko lino akufunika kuti apeze njira zobwenzeretsa chikhulupiriro cha anthu mwa apolisi, iye adatero.
Mwapasa atakumana ndi aphungu a chizimayi a ku Nyumba ya Malamulo pa nkhani yoti apolisi ena adagwiririra amayi ku Mpingu, Msundwe ndi Mbwatalika ku Lilongwe, adavomera kuti pali kusakhulupirirana pakati pa apolisi ndi anthu ndipo ayetsetsa kubwezeretsa chikhulupiriro mwa anthu pogwira ntchito mwachilungamo.
| 7 |
Papa Wapempha Mabungwe Achilimike Polimbana Ndi Mchitidwe Wogwiritsa Ntchito Ana Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco wapempha maiko ndi mabungwe kuti achilimike pa ntchito yolimbana ndi mchitidwe wogwiritsa ntchito ana.
Malinga ndi malipoti a wayilesi ya Vatican, Papa walankhula izi lachitatu ku likulu la mpingowu ku Vatican.
Iye wati ndi udindo wa aliyense kuchitapo kanthu pofuna kuthetsa mchitidwe woipa wogwiritsa ntchito ana womwe ukukulirakulirabe chifukwa cha umphawi.
Mzolankhulalankhula zake lachitatu Papa Francisco wati ndi wokhudzidwa ndi mchitidwe wonyasa wogwiritsa ntchito ana ntchito zomwe sizigwirizana ndi msinkhu wawo kotero kuti ana amasanduka akuluakulutu nthawi yao isanakwane.
Pamenepa iye wapempha maiko ndi mabungwe kuti achilimike polimbana ndi mchitidwewu ndipo waonjezeranso kunena kuti ndi ntchito ya munthu aliyense kuyetsetsa kuchitapo kanthu polimbana ndi mchitidwewu.
Papa Francisco wati nthenda monga ya COVID-19 yomwe yakhudza dziko lonse la pansi yabweretsa mavuto osiyana-siyana ndipo yakakamiza ana ambiri mmaiko osiyana-siyana kuti anke nagwira ntchito zoposa msinkhu wao pofuna kuthandiza mabanja awo omwe ali mu umphawi wadzaoneni.
Iye wati ntchito zolemetsa zomwe ana akugwira ndi zochititsa kuti matupi awo aonongeke komanso makamaka nzoononga ndi kusokoneza maganizo awo.
Papayu wati ana ndi chiyembekezo cha mabanja komanso maiko awo kotero kuti akuyenera kuyanganiridwa bwino.
Uthenga wa Papa Francisco wabwera pa nthawi yoyenera pomwe lachisanu pa 12 June, 2020 dziko lonse la pansi likhale likuganizira za mchitidwe wogwiritsa ntchito ana World Day Against Child Labour.
| 14 |
Phungu Wakale Akagwira Ukayidi Chifukwa Cha Katangale Bwalo la milandu ku Zomba lalamula phungu wakale wa nyumba ya malamulo mdera la Zomba Malosa Anderson Undani kuti akakhale ku ndende kwa chaka chimodzi ndi theka pa mlandu wa katangale.
Wasayinira kalatayo-Ndala Malinga ndi kalata yomwe bungwe lothana ndi katangale ndi ziphuphu mdziko muno la Anti-Corruption Bureau (ACB) latulutsa, yomwe yasayinidwa ndi wofalitsa nkhani wake Egritta Ndala, phungu wakaleyu komanso omuthandizira wake Pangani Nazombe anasokoneza ndalama za thumba la Contsituency development Fund (CDF) zomwe zimayenera kugwiritsidwa ntchito pomanga nyumba ya mphunzitsi pa sukulu pulaimale ya Mapalo.
Ndalama zina akuti zinali zoti amangire zimbudzi pa sukulu ya Domasi CCAP, kukonzanso nsewu wa Domasi-Kasonga komanso kumanga mlatho pa mtsinje wa Malonga.
Bungwe la ACB linamanga awiriwa pa 1 October mchaka cha 2018. Awiriwa anatengeredwa ku bwalo la milandu komwe a Undani amayankha mlandu wogwiritsa ntchito ofesi yawo molakwika, kuba komanso kupeza ndalama kudzera mu njira yachinyengo. Pomwe a Nazombe amayankha mlandu wothandizira munthu kupalamula mlandu komanso kupeza ndalama kudzera mu njira yachinyengo.
Pa 3 July bwaloli linawapeza olakwa pa nkhaniyi ndipo pa 13 ndi pomwe bwaloli lapereka chigamulo chake pa nkhaniyi pomwe a Undani alamulidwa kukakhala ku ndende kwa miyezi 18 pa mlandu uliwonse omwe anapalamula. Pamene a Nazombe alamulidwa kukakhala ku ndende kwa miyezi 12 pa mlandu uliwonse omwe anapalamula ndipo akuti chilango chonsechi chidziyendera limodzi.
| 7 |
Akufuna mayankho pa njala ya mzipatala Mabungwe omwe si aboma ku Rumphi ati akudikirabe yankho kuchokera kwa mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika pa zakusowa kwa chakudya mzipatala zosiyanasiyana mdziko muno.
Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mwezi wathawu, mabungwe omwe ali pansi pa Civil Society Network ku Rumphi adachita zionetsero ngati njira imodzi youza boma kuti lichitepo kanthu pa zakusowa kwa chakudya pachipatala cha Rumphi.
Banda kuwerenga chikalata chomwe adalembera boma Mabungwewa adauza Mutharika, kudzera mchikalata chomwe adapereka kwa akuluakulu a boma, kuti awayankhe pasanadutse sabata ziwiri.
Wotsogolera mabungwewa, Eunice Banda, wauza Tamvani kuti boma silinayankhebe chikalata chawocho.
Iye wati mabungwewa akufuna kukhalanso pansi kuti apeze njira ina yopezera mayankho kuchokera ku boma.
Titachita zionetsero boma lidapereka matumba 100 a chimanga. Koma chakudya chimenechi chitha kumapeto a mwezi uno. Izi zikutanthauza kuti kukhalanso njala kuyambira mwezi wamawa, adatero Banda.
Nduna ya za masewero ndi chikhalidwe, Grace Chiumia, masiku apitawa adauza mabungwe kuti achepetse zionetsero chifukwa chakuti boma limamva kamodzi.
Chiumia, polankhula ku Nkhata Bay pamene amakhazikitsa ntchito zolimbana ndi nkhanza mbanja, adati ndalama zomwe mabungwe akugwiritsa ntchito pazionetsero azipititse kuntchito zachitukuko.
| 6 |
Bishop Tambala Apempha Akhristu Asamalire Atumiki Wolemba: Thokozani Chapola ontent/uploads/2019/11/bishop-tambala.jpg" alt="" width="310" height="362" />Tambala: Asisteri amasowa kusamalidwa komanso chitetezo Episkopi wa dayosizi ya Zomba ambuye George Desmond Tambala loweruka wapempha akhristu kuti aziwonetsa chikondi posamalira atumiki mu mpingowu.
Iwo amalankhula izi ku Domasi parish pa mwambo wa misa yotsegulira nyumba ya sisteri a chipani cha Our Lady Of Mercy chomwe achikhazikitsa kumene mu dayosiziyo.
Iwo ati asisteriwa afika ku parishiyi kuti adzatumikire choncho akhristu nawo akuyenera kuwasamalira mu njira zosiyanasiyana.
Tisangowona kuti asisteri abwera kuzatitumikira koma monga anachitira Abraham, asisteri amasowa kusamalidwa monga chitetezo chawo komanso kuwathandiza kuti ntchito yawo agwire bwinobwino, anatero Ambuye Tambala.
Ambuye Tambala ati ndi okondwa ndi kufika kwa asisteriwa mu dayosiziyi kaamba koti athandiza kupeputsa ntchito yaikulu yomwe ili mu dayosiziyi.
Ndine okondwa kwambiri chifukwa linali khumbo lathu komanso akhristu kwa nthawi yaitali kuti tikhale ndi asisteri chifukwa ntchito ya mmunda mwa Ambuye yakula ansembe sakanatha pawokha kufikira anthu onse komanso utumiki womwe abweretsa kuno ndikuwona kuti ndi wofunika kwambiri, anatero Ambuye Tambala.
Chipanichi chili ndi likulu lake mdziko la Italy koma chikupezeka mmayiko osiyanasiyana.
| 13 |
Zigawenga Zapha Alonda Awiri pa Estate ku Mangochi Apolisi mboma la Mangochi akusakasaka anthu omwe sakudziwika omwe apha alonda awiri komanso kuba katundu wa ndalama zokwana 3.5 million-kwacha pa estate ya Lilimbe mbomalo.
Watsimikiza za nkhaniyo Daudi Wachiwiri kwa wofalitsa nkhani za apolisi mbomalo Sub-Inspector Amina Tepani Daudi watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati alondawa ndi a Jafali Matola a zaka 72 komanso a Idrissah Ngochela a zaka 66 zakubadwa.
Apolisiwa ati anadziwitsidwa izi ndi mlonda yemwe amasintha anzakewa pa ntchito mmamawa pomwe anawapeza akutaya magazi kaamba kovulazidwa ndi akubawa.
Ndizoona kuti ife apolisi kuno ku Mangochi tikuyangana anthu omwe aba katundu okwanira 3.5 million komanso apha alonda awiri pa estate ya Lilimbe, anatero Daudi.
Iwo atinso apolisi ambomalo adakasakasakabe anthuwo mbomalo ndi cholinga choti akayankhe milandu yomwe apalamulayi.
| 14 |
Kafukufuku wa chamba watha Zotsatira za kafukufuku wa ulimi wa chamba zomwe Amalawi akhala akudikira zatuluka koma mlembi wa unduna wa zamalimidwe, mthilira ndi chitukuko cha madzi Gray Nyandule Phiri wati zotsatirazi akuzisunga mwachisinsi.
Phiri wati zotsatirazi zomwe kafukufuku wake watha zaka zitatu ziyamba zapita ku ofesi ya presidenti ndi nduna zake (OPC) kuti akaziunike zisadaulutsidwe kwa Amalawi.
Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Kafukufukuyu adatenga zaka zitatu ku Chitedze ndi ku Salima ndipo zotsatira zake zatuluka tsopano koma tikudikira kuti akaziunike ku OPC kenako tidzazitengere ku Nyumba ya Malamulo, adatero Nyandule Phiri.
Phungu wa dera la kumpoto kwa Ntchisi Boniface Kadzamira ndiye adabweretsa nkhani yololeza kulima chamba mNyumba ya Malamulo zaka zitatu zapitazo ndipo aphungu adavomereza nkhaniyi atakambirana.
Akadaulo osiyanasiyana akhala akuthirira ndemanga za kufunika kothamangitsa kafukufukuyu kuti dziko la Malawi liyambe kulima nkugulitsa chamba chomwe ena akuti chikhoza kusintha chuma cha dziko lino.
Katswiri wina wa bizinesi yokhudza malonda a chamba wa ku Canada wa Green Quest Pharmaceuticals adati chamba chili ndi mtengo wabwino pamsika wa maiko ndipo chikhoza kubweretsa ndalama zambiri mdziko.
Chamba chomwe akadaulowa akulimbikitsa ndi chomwe amagwiritsa ntchito mmafakitale popanga zinthu zosiyanasiyana monga mankhwala ndipo akatswiri amati mphamvu zake nzochepa poyerekeza ndi chamba chosuta chija chimazunguza bongo.
Polankhula ndi Tamvani, mlembi wa nthawi yoona za mbewu zogwiritsidwa ntchito mmafakitale Industry Crops Association (ICA) Hellen Chabunya adati boma likuyenera kukhala ndi chidwi pa kafukufuku wa ulimi wa chamba kuti dziko lino litukuke.
Chongofunika apa nkuwonetsetsa kuti tapanga malamulo ogwira okhudza kayendetsedwe ka ulimi ndi malonda a chambachi. Zina mwa izi nkuwonetsetsa kuti taunikaso malamulo ena okhudza mbeu ngati zimenezi, adatero Chabunya.
| 2 |
Ogwira Ntchito ku Chipatala cha Zomba Akupitilirabe Kunyanyala Ntchito Ogwira ntchito ku chipatala chachikulu cha boma la Zomba ati apitilirabe kunyanyala ntchito ngakhale kuti boma lawatsimikizira kuti lawawonjezera ndalama zomwe amapempha.
Mmodzi mwa anamwinowa yemwe sadafune kudzitchula dzina wauza Radio Maria Malawi kuti iwo achita izi kamba koti ndalama yomwe imakhala ya chipepeso choyika miyoyo yawo pa chiwopsezo yomwe amalandira poyamba ya 1, 800 kwacha idakhalitsa komanso inali yochepa. Iwo atinso anamwinowa sakugwirizana nazo zomwe unduna wa zaumoyo wanena kuti ndalama zimenezi alandira nthawi ya mliri wa Coronavirus yokha.
Mwazina iwo ayamikira boma kaamba kowatsimikizira kuti alemba anthu ena owonjezera ogwira ntchito mchipatala pomwe ku chipatala cha Zomba kutumizidwe anthuwa okwana 70.
Ndizoona kuti a boma anena kuti pakhala kuwonjezera kwa ndalama zachiwopsezo zomwe timapempha ndipo kukambirana kwathu ndi akuluakulu ena ati zipangizo zafika ndipo padakali pano zilipo koma ife ndondomeko zomwe zilipo pakadali pano za ndalama zachiwopsezo chathu ndi yomwe tisakugwirizana nayo, anatero namwinoyo.
| 14 |
HRDC Yachita Ziwonetsero Zokwiya ndi Kusankhidwanso kwa Makomishonala Awiri Bungwe la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) lero lachita ziwonetsero zosagwirizana ndi kusankhidwanso kwa ma commissioner awiri a bungwe la MEC ndi mtsogoleri wa dziko lino Professor Peter Mutharika.
Mu mzinda wa Zomba ziwonetserozi zinayambira ku Chinamwali mpaka ku ofesi ya bwanamkubwa wa bomalo.
Ziwonetsero za mmbuyomu zokonzedwa ndi HRDC Polankhula kwa atolankhani atapereka chikalata cha madandaulochi, wapampando wa bungwe la HRDC mchigawo chaku mmawa a Madalitso Banda ati akufuna mtsogoleri wa dziko lino avomereze kuti chisankho chichitike pa 23 June pano, momwe aphungu akunyumba ya malamulo agwirizanirana komanso akufuna kuti ma commissioner awiri a bungwe la MEC omwe ndi Dr. Jean Mathanga, komanso Linda Kunje asagwire ntchito pa chisankho chimenechi, chifukwa choti mabwalo a milandu anawapeza kuti adalephera kugwira bwino ntchito pa chisankho chomwe chidachitika pa 21 May chaka chatha.
Polalankhulapo atalandira chikalatacho mmalo mwa bwanamkubwa wa bomalo a Chris Nawata ati chikalatachi achipereka kwa anthu oyenelera ndipo chikafika mmanja mwa mtsogoleri wa dziko lino.
Ziwonetsero za mtunduwu zachitikanso mmizinda ya Blantyre, Lilongwe ndi Mzuzu.
| 11 |
Akupopa zimbudzi pochepetsa matenda Ena zimbudzi zawo zikadzadza amagwetsa ndi kukumba china. Uku ndi kutha malo. Lero zinasintha chifukwa khonsolo ya Blantyre mogwirizana ndi Waste Advisers agwirizana zopopa zimbudzi zomwe zadzadza.
Iyitu ndi njira yomwe mbalizi zamvana pofuna kulimbikitsa ukhondo mumzinda wa Blantyre pamene matenda a kolera akugwetsa anthu moti kufika lero anthu 26 amwalira.
Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Kupatula izi, khonsoloyi ikuyenda khomo lililonse mumzinda wa Blantyre kuphunzitsa anthu zaukhondo ndipo nyumba 10 000 azifikira.
Amene akuwongolera ntchitoyi ku bungwe la Waste Advisers, Marcel Chisi, adati kupatula ntchitoyi, amanga zimbudzi 30 mwa zimbudzi 100 mumzindawu kuti ukhondo upite patsogolo.
Tisamangonena kuti anthu asakodze paliponse koma tikuyenera kumanga zimbudzi kuti anthu azilowa mmenemo polipira kangachepe, adatero Chisi.
Tagwirizana ndi makampani amene akugwira ntchito yopopa komanso kumanga zimbudzi zamakono. Anthu akatipeza, tiwalumikizitsa kwa amene angawathandize.
Chimpopa chimodzi chimapopa zinthu zochuluka malita 3 600 ndipo munthu alipira K30 000.
Komanso mtengo umasintha malinga ndi kutalika kwa malo amene akapopawo.
Wachiwiri woona nkhani za umoyo ku khonsolo ya Blantyre, Samden Seunda adati zonyansazo zikapopedwa azizipititsa ku Chirimba, Soche, Blantyre ndi ku Limbe komwe azikazithira mankhwala.
Tili ndi chikonzero kuti zonyasazo tizizithira mankhwala ndipo kutsogolo kuno tizipangira nkhuni zomwe mutha kuphikira, adatero Seunda.
| 6 |
Kwaya ya Sts Symon and Jude Ithandiza Radio Maria Malawi Kwaya ya Saints Symon and Jude ku Chileka mu parishi ya Lunzu mu arkidayosizi ya Blantyre ya mpingo wa katolika, yati ndi udindo wa aliyense kuthandiza Radio Maria ndi zinthu zosiyanasiyana.
Mkhalapampando wa kwayayi, Mayi Florence Chirwa, alankhula izi pambuyo popereka thandizo lawo ku wailesiyi mboma la Mangochi.
Mayi Chirwa, ati ngakhale kwayayi si ya anthu ochita bwino, komabe anachiona cha nzeru kuti agawane ndi wailesiyi zochepa zomwe ali nazo, pofuna kuthandizira ntchito yofalitsa uthenga wabwino padziko lonse.
Titakhala pansi ngati kwaya tinaona kuti ndi kofunika kuthandiza wayilesiyi popeza imathandiza mpingo wathu mu njira zosiyanasiyana ndipo tathandiza ndi ndalama yokwanira 40 thousand kwacha, anatero mayi Chirwa.
Polankhulapo mkulu wowona ntchito zokweza wailesiyi a Martha Mwandira, ayamikira kwayayi kaamba kofika ndi thandizo lawo mu nthawi yoyenera, pomwenso wayilesiyi ikukumana ndi mavuto ambiri a zachuma.
Ife ndi othokoza kamba koti kwayayi yagwira ntchito yaikulu yothandiza wayilesiyi ndipo thandizoli ligwira ntchito yoyenera, anatero Mwandira.
Iwo apephanso anthu akufuna kwabwino kuti adzithandiza wayilesiyi molowa manja kuti ntchito zake zipite patsogolo maka pa nthawi ino ya Coronavirus pomwe zinthu zambiri zayima.
| 13 |
Malawi siidalakwe za al-Bashir Mphunzitsi wa za mbiri yakale ku sukulu ya ukachenjede ya Chancellor College, Pulofesa Chijere Chirwa wati dziko lino silingakhudzidwe mnjira iliyonse pokana kuchititsa msonkhono wa mgwirizano wa maiko a mu Africa.
Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mtsogoleri wa dziko lino, Joyce Banda adaletsa kuti msonkhanowu usachitikenso mdziko muno chifukwa chokakamizidwa kuti limange mtsogoleri wa dziko la Sudan, Omar Hassan al-Bashir.
Mkuluyu wakhala akusakidwa ndi bwalo loona milandu ya upandu padziko lapansi la International Criminal Court (ICC) pamilandu ya upandu.
Dziko lino limayembekezereka kuchititsa msonkhanowo kuyambira pa 9 mpaka pa 16 mwezi wa mawa ku Lilongwe.
Sabata ziwiri zapitazo, Banda adanenetsa kuti ngati al-Bashir angayerekeze zobwera mdziko muno adzamangidwa.
Koma akuluakulu a mgwirizanowo adati Malawi monga dziko lomwe lichititse msonkhanowo likuyenera kulandira munthu aliyense yemwe ndi membala wa mgwirizanowo.
Izi zidasokoneza Banda popeza omwe amathandiza dziko lino adanenetsa kuti dziko lino limange al-Bashir akatera mdziko muno.
Banda adalengeza kuti sachititsanso msonkhanowo ndipo mmalo mwake msonkhanowo uchitikira mdziko la Ethiopia.
Koma Chirwa wati ganizo la Banda lili bwino ndipo silingaike dziko lino pamoto.
Ubwino wake nkuti pali maiko ena monga Zambia ndi Botswana omwe ali mumgwirizanowo koma adaneneratu kuti amanga mkuluyu akafika mdziko lawo.
Ichi ndichitsimikizo kuti sitidalakwitse chifukwa maiko ena amagwirizana ndi ganizo lathu lomanga mkuluyo, adatero Chirwa.
| 11 |
Mwambo woika maliro a khanda lozizira Amalawi ngakhale ali ndi miyambo yosiyanasiyana malinga ndi mitundu yawo monga Achewa, Angoni, Atumbuka, Alhomwe, Amanganga, Asena kaya ndi Ayao, koma pamwambo woika khanda lopitirira zochitika zimakhala zofanana. DAILES BANDA adacheza ndi mayi Catherine Ligowe kuti afotokoze mmene mwambo woika khanda lozizira umayendera. Adacheza motere: Ndikudziweni mayi wanga.
Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Ndine Catherine Ligowe. Ndidabadwa zaka zambiri zapitazo. Ndimachokera ku Ntcheu mmudzi mwa Chikadya, T/A Ganya. Ndili ndi ana asanu ndi awiri. Ndinenso namkungwi kumudzi kwathu komanso ndidali mzamba.
Kuno ku Mzuzu mukupezekako bwanji? Mavuto mwanawe. Kuyeseyesa kuti tipezeko koponyako mkamwamu.
Ku Mzuzu kunonso ndinu namkungwi? Ayi, ku Mzuzu kuno unamkungwi wanga umakhala wa mmakwalalamu koma kumudzi ndi komwe ndimagwira ntchitoyi kuchinamwali, tere chaka chomwechi ndidali komweko.
Mutiuzeko pangono za maliro akhanda lopitirira Inu mufuna mudziwe chani? Tiyambe ndi mwambo wa maliro mmene umakhalira.
Khanda lopitirira limatchedwa kuti khanda lozizira chifukwa mayi a khanda lija amakhala kuti sadakhale kaye pamodzi ndi mwamuna.
Mukutanthauza kuti khanda litamwalira pamiyezi iwiri makolo ake asadakhalire malo amodzi mwambo wake umakhala ngati wa khanda lopitilira? Eya, chifukwa timakhulupirira kuti mwanayo sadatenthetsedwe ndi bambo ake.
Zimayenda bwanji? Mwana uja akamwalira amakaikidwa ndi azimayi okhaokha koma azimayi aja saloledwa kulira malirowo chifukwa kulira kuja kumachititsa kuti mayi uja asadzaberekenso. Manda a malirowa sakhala akuya ngati a maliro a munthu wamkulu.
Chifukwa chiyani sakhala akuya? Kalekalelo makolo athu ankakhulupirira kuti manda a khanda lozizira akakhala akuya kwambiri mayi wa khandalo sadzaberekanso.
Ndiye maliro a mapasa mumachita bwanji? Akamwalira mmodzi mwa ana amapasa azimayi akalira malirowa timakhulupirira kuti mwana wotsala uja amamwaliranso, komanso tikamaika malirowa timaika khanda lomwaliralo ndi mvunguti pambali pake kuti mzimu wake uziona ngati akadali ndi mnzake uja.
Nanga wotsalayo mumatani naye? Ameneyo timamusambitsa mumankhwala kuti mzimu wa mnzake uja usamamubwerere.
Tsopano inu mumati mudali mzamba, mudabadwitsako mwana wopitirira? Ayi, palibe mwana wopitirira amene ndidabadwitsako.
Mudasiyiranji ntchitoyi? Boma lidaletsa komanso anthu amene amabereketsa azimayi amafa maso nchifukwa chake anamwino ambiri ochiritsa azimayi kuchipatala amakhala ovala magalasi. Kalekalelo mzamba asadayambe kugwira ntchito amayamba kaye wasamba mankhwala kuti adziteteze ku ukhungu.
Chimachititsa kufa masoko ndi chiyani? Chimachitika ndi chakuti azimayi akamabereka amachita zinthu zodabwitsa zambiri ndiye ukaona zinthu zimenezo kwanthawi yaitali maso aja amafa, umangoona zinthu mwa mbuu.
Zikomo kwambiri chifukwa cha nthawi yanu.
Zikomo.
| 1 |
Za kulephereka kwa zisankho Muzina Edi mwana Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Edi sebe santu Muzina zizata mfana Ya muzina Sindikudziwa ngati Papa Wemba nyimboyo adaimverapo koma ndimo ndinkayimvera pamene inkaphulika malo aja timakonda pa Wenela. Gervazzio ndiye adaika nyimboyo pokumbukira Papa Wemba amene watsikira kwachete.
Koma dziko ili! Zoona likutenga anthu ofunika ndi otchuka, achina Prince, kusiya ife ojiya, osolola ndi osenza pano pa Wenela. Imfa ikusiya zilengwalengwa.
Tsiku lina ndidzaipha imfa yotenga mayi kusiya mwana akulira.
Tsikulo wina adati ndipite ndikaitanire ku Mibawa. Koma nkadadziwa kuti amandikankhira kunkhondo! Padafika asirikali atavala nkhwani-nkhwani. Komatu eni minibasi samaimva, ati khobwe akatolera kuti? Nawo adabwera ndi mapanza awo, inde magigo.
Sitiimva. Minibasizi ndi zanu kuti muzitolera ndalama? adatero phanza wina, atanyamula miyala.
Kupanda nzeru. Malowa ndi anu? Kodi ogulitsa nkhwani mumsika angamemane kuti azitolera ziphaso ndiwo chifukwa nkhwaniwo ndi wawo? Kupusa! Mnyumba ya mwini saotchera mbewa, adatero wapolisi wina, akukanyanga mmodzi mwa magigowo nkumuponya mchimbaula adachilawa Chihana.
Apo ndeu idabuka koma paja lamulo liposa mphamvu, akhonsolo adawina ndipo adayamba kutolera ndalama kuchokera kwa madalaivala.
Nditabwerera ku Wenela, ndidapeza Abiti Patuma ndi ena onse akumvetsera wailesi.
Chisankho chimati chikhalepo ku Mchinji chalephereka. Boma silidapereke ndalama ati chifukwa lilibe, adatero muulutsi.
Boma lilibe ndalama bwanji? Koma chisankho cha ku Zomba ndiye adapeza ndalama? Pafa khoswe apa, adatero Abiti Patuma.
Paja nawe, kumangomva fungo la khoswe paliponse? Kulitu njala uku, adatero bambo amene adali naye tsikulo.
Zanu. Komabe inetu ndikuona kuti Dizilo Petulo Palibe ikuona kuti kuchititsa chisankho ku Mchinji kukhoza kuchititsa Male Chauvinist Pigs kuoneka mashasha, adayankha Abiti Patuma.
Abale anzanga, musandifunse amatanthauzanji chifukwa nane sindikudziwa. Pajatu ine za matchera ayi.
Padakalipano boma likuphwanya malamulo omwe amaneneratu kuti chisankho chiyenera kuchitika pasanathe masiku mwakuti, adatero Abiti Patuma.
Mukutayatu nthawi. Paja zomatiuza kuti chakuti chichitike pofika tsiku lakuti si mbali yathu, adatero bambo adali naye uja.
Mukutanthauza kuti nthawi yokhala pampando ikadzatha, Mustafa sadzafuna kubweza mpando kwa Ajibu? Adangoti duuu mkulu uja. Adalandira foni.
Mwati bwanji? Shati Choyamba watisiya? Zabodza izo, nkadamva. Ndikudziwa kuti ali ku Tajkstan komwe amuchotsa dzino dzana. Kukonda kupekera ena imfa bwanji? Akukupanitu makofi akabwera, adatero mkuluyo adatero.
Imeneyinso idandipita. Malingaliro adali kwa Papa Wemba komanso Prince.
| 11 |
Mlandu wa Savala ukupendekeka Mlandu wa mayi wa zaka 33, Caroline Savala, yemwe khothi lidamupeza wolakwa pamlandu wakuba ndalama za boma zokwana K84 miliyoni ukuyenda mwapendapenda.
Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Savala yemwe amachita bizinesi ya zomangamanga adamupeza wolakwa ndipo akuyembekeza chigamulo cha khothi pa zachilango chake koma Lachisanu lapitali kudali ngati sewero ku bwalo la milandu pomwe womuimira pamlanduwo Ralph Kasambara adalephera kubwera kubwalolo.
Sadayankhe funso ngakhale limodzi: Savala (kumanzere) Kusabwera kwa Kasambara mmawa wa Lachisanulo kudakwiyitsa wogamula mlanduwo Fiona Mwale yemwe adaimitsa mlanduwo kuti upitirire 2 koloko masana.
Nkhaniyi ipitirira 2 koloko masana ano kuti woimirira mayi Savala abwere ndipo ngati sabwera tikamba nkhani popanda wowaimira,adatero Mwale.
Malingana ndi ndondomeko za ku bwalo la milandu, tsiku likakhazikitsidwa ndipo woimirira munthu pamlanduwo walephera kubwera pachifukwa chilichonse, amayenera kudziwitsa bwalo la milandulo nthawi yabwino kapena kutumiza okamuyimirira.
Mmawa wa Lachisanu, kalaliki wa kukhotilo adali kalikiliki kuyesetsa kulumikizana ndi Kasambara koma sizimatheke zomwe zidachititsa Mwale kuti asinthe nthawi ya mlandu.
Nthawi ya mlandu itafika 2 koloko masana, Kasambara sadaoneke kubwalo la milandulo ndipo mmalo mwake adatumiza womuimirira Tisilira Kaphamtengo, yemwe adapempha wogamulayo kuti mlanduwo awusuntheso poti iye samautsatira bwinobwino.
Ine ndiwongoimirira a Kasambala omwe sakumva bwino mthupi koma poti nkhaniyi sindikuyitsata bwinobwino ndimati ndipemphe kuti isinthudwe ndipo idzakambidwe tsiku lina, adapempha Kaphamtengo.
Mwale adakana kumva pempholi ponena kuti zomwe adauza khothi Kaphamtengo zokhudza kusamva bwino mthupi kwa Kasambala amayenera kuuza bwalolo nthawi yabwino ndipo adati mlanduwo upitirirebe.
Mwale atanena izi, Kaphamtengo adapemphanso kuti alole kuti Savala asayankhe funso lililonse limene afunsidwe poopa kupotoza nkhani ndipo pempholi lidaloledwa.
Savala adafunsidwa mafunso 10 koma sadayankhepo ngakhale limodzi mpaka mlanduwo udayimitsidwa.
Savala adapezeka wolakwa pa 18 July 2015 wogamula yemwe adalinso Mwale atapeza umboni wakuti mayiyu amalandira ndalama zosagwirira ntchito kuchoka ku unduna wa zokopa alendo.
Savala,yemwe samagwira ntchito mboma nthawi yomwe amaganiziridwa kuti amalandira ndalamazo, adauza bwalo la milandu muumboni wake kuti iye adachita kukokeredwa mu kangaude wachinyengowu ndi mkulu wina yemwe amagwira ntchito ku unduna wazokopa alendo Leonard Kalonga komanso mnzake wa ku ubwana Florence Chatuwa omwenso amayimbidwa mlandu omwewo.
| 7 |
Kudzula: Mpeni wofunikira kwa butchala Popha mbuzi kapena ngombe amagwiritsa ntchito zida zosiyanasiyana monga nkhwangwa, zikwanje ndi mipeni. Umodzi mwa mipeniyi umatchedwa kudzula ndipo eni ake akuti mpeniwu amagwiritsa ntchito posenda nyamayo. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi Innocent Chimsewu yemwe amapha nkugulitsa nyama ya mbuzi kuti adziwe chinsinsi chosagwiritsa mpeniwu pantchito zina koma kuphera ndi kusendera nyama basi. Iwo adacheza motere: Tandiuze dzina lako ndi ntchito yomwe umapanga, mnyamata.
Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Dzina langa ndine Innocent Chimsewu ndipo ndimapha mbuzi ndi kumagulitsa nyama yake mumsika wa ku Area 22A ku Lilongwe.
Kodi pali zinsinsi zilizonse zokhudzana ndi bizinesi ya nyama makamaka ya mbuzi kapena ngombe? Chimsewu kusenda mbuzi ndi mpeni wa kudzula Ndikudziwa zomwe mukutanthauza ngakhale mukukhala ngati mukukuluwika pangono ndipo yankho lake ndi ili: bizinesi ya nyama ya mbuzi kapena ngombe nchimodzimodzi bizinesi ina iliyonse. Apa ndikutanthauza kuti momwe anthu amayendetsera bizinesi ina iliyonse, ndimoso zimachitikira mbizinesi ya nyama.
Ndidamvako kuti mpeni wosendera nyama ya malonda sugwiritsidwa ntchito zina, zimenezi nzoona? Nzoona, mpeni umenewu tikamaliza kusendera mbuzi kapena ngombe timautsuka bwinobwino kuusunga pamalo abwino kuti usamalike. Kunena zoona si kuti pali kugwirizana kulikonse koma kuti anthu amangochita izi ngati njira imodzi yosamalira mpeniwu kuti usasowe.
Dzina la kudzula lidabwera bwanji? Ndi dzina basi monga momwe maina ena onse amayambira kapena kubwerera. Ena adangoganiza kuti mpeniwo ukhale kudzula mwina potengera ntchito yomwe umagwira yosendera nyama.
Umakhala mpeni wooneka bwanji? Ndi mpeni monga momwe umakhalira mpeni wina uliwonse koma uwu umakhala wakuthwa kwambiri komanso kawirikawiri, umaninga mmphepete imodzi ngati wosokera nsapato kaamba konolanola. Timanola pafupipafupi chifukwa mpeni wobuntha umanyotsola nyama posenda. Mnofu wambiri umatsalira kuchikopa.
Ndikubwezere mmbuyo pangono. Mpeni wa kudzula utasowa, mpeni wina uliwonse sungagwire nthito yosendera mbuzi kapena ngombe? Ukhoza kusendera bwinobwino popanda choletsa. Komansotu posenda mbuzi kapena ngombe si kuti pamakhala mpeni umodzi wokha, ayi, kungoti si mipeni yonse yomwe ili kudzula, koma wokhawo womwe ndalongosola uja ndipo umenewu ndiwo suloledwa kugwiritsa ntchito ina iliyonse Ntchito ina ya kudzula ndi chiyani? Kudzula amagwira ntchito zambiri pakupha ndi kusenda mbuzi ndi ngombe. Ntchito yoyambirira ndi yothyolera fupa la pakholingo. Wocheka pakhosi akacheka, pamakhala fupa lomwe limatsalira lomwe limasunga moyo ndiye amatenga kudzula nkuthyolera fupa limeneli. Ntchito ina, poti mpeniwu umakhala wakuthwa kwambiri, ndi kuchekera zammimba monga mtima, chifu, matumbo ndi ndulu. Makamaka pa ndulupo, ukagwiritsa ntchito mpeni wobuntha, mwangozi ukhoza kuthudzula ndulu ndiyetu kungotero, ndiwo yonse yaonongeka.
Nanga mubutchala mogulitsira nyamayo kudzula safunika? Si kwenikweni, iye kwake nkophera ndi kusenda koma zikavutitsitsa akhoza kugwira ntchito yochekera mubutchala si kuti china chake chingachitike, ayi, koma kuti ambiri amaumira kutero kuopa kusowetsa.
| 15 |
Kolera yaluma mano Nthenda ya kolera imene idayamba ngati njerengo mwezi wa November chaka chatha, ikukwererabe moti kuchoka Lachisanu sabata yatha chiwerengero cha anthu odwala nthendayo chidachoka pa 420 kufika pa 459 Lachiwiri.
Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Malinga ndi zikalata zochokera ku Unduna wa Zaumoyo, anthu 6 amwalira ndi matendawa ndipo anthu 14 akulandira thandizo mmalo apadera amene undunawo udakhazikitsa mmaboma ena. Matendawa akhudza maboma a Karonga, Kasungu, Dowa, Nkhata Bay, Lilongwe, Salima, Mulanje, Nsanje, Chikwawa, Likoma, Rumphi ndi Blantyre.
Matendawa adafala ndi msodzi wina, amene adaitenga ku Wiliro mboma la Karonga ndipo adafika nayo ku Ngala, kumene asodzi amafikira ndi kugulitsa nsomba zawo. Msodziyo adafika padokopo ali wefuwefu ndipo adachita chimbudzi mphepete mwa nyanja.
Malinga ndi Idah Msiska, yemwe ndi wapampando wa komiti ya chitukuko ya mmudzi mwa Muyereka ku Ngala, matendawa adafala kwambiri chifukwa cha kusowa zimbudzi komanso utchisi wa deralo.
Wodwala woyamba adafika pagombe nkuchita chimbudzi ndipo tizilombo tidafalikira mmadzi. Chovuta china nchoti nsomba zimaola kwambiri kumalowa ndipo zimaitana ntchentche zomwe zimafalitsa matendawa. Padakalipano tikuyendera khomo ndi khomo kuti tithane ndi matendawa ndipo amene sakutsatira malangizowa amakumalipa chindapusa, adatero Msiska.
Iye adati chodziwikiratu kuti matendawa afala chifukwa ena amachita chimbudzi mnyanja momwe enanso amatunga madzi ogwiritsa ntchito pakhomo.
Malinga ndi mmodzi mwa anthu 258 amene apezeka ndi matendawa ku Karonga, Baxter Nyondo, matendawa ndi wovuta ndipo akungoyamika Mulungu kuti akadali moyo. Iye Lachiwiri tidamupeza akulandira thandizo pachipatala chachingono cha Ngala.
Sindinkadziwa chinkandichitikira. Ndinkangothulula osalekeza. Pano bola. Ndikuyamika chifukwa achifundo adanditengera kuchipatala msanga, adatero iye.
Iyi ndi nkhani yolingana ndi yomwe adatambasula Mercy Kachepa yemwe ankadikirira mbale wake pamalo a padera a odwala kolera ku Bwaila ku Lilongwe.
Adafika kunyumba kuchoka kosewera akudandaula mmimba. Posakhalitsa adayamba kugudubuka, uku akudziyipitsira. Kupanda kuikapo mtima akadapita, adatero Kachepa.
Lolemba Nduna ya za Umoyo Atupele Muluzi idakayendera malowo komwe adatsimikiza kuti zinthu zaipa.
Nkhondo ndiye ikumenyedwa kuti vutoli lithe koma kunena zoona, matendawa atikakamira ndipo liwiro lomwe akufalira likuopsa kwambiri, adatero iye.
Muluzi adauza Nyumba ya Malamulo sabata yatha kuti katemera wa kolera yemwe boma likupereka akhoza kuthandiza kuthetsa kufala kwa matendawa ataperekedwa mmadera ambiri makamaka omwe ali pachiopsezo.
Oyanganira ntchito za umoyo mmaboma a Lilongwe ndi Karonga kumene kolera yafala kwambiri, adati sakugona tulo kaamba ka matendawa.
Woyanganira ntchito za umoyo mboma la Lilongwe, Alinafe Mbewe, adati vutoli lakula kwambiri kwa Mitengo ku Area 36 ndi Kauma komwe anthu ambiri omwe apezeka ndi matendawa amachokera.
Zinthu sizikusintha kwenikweni koma tikuyesetsabe. Kuchoka pa 28 December, 2017 kudzafika pa 23 January, 2018, anthu 35 ndiwo adapezeka ndi kolera koma kuchoka pa 24 January kudzafika pa 12 February, anthu 82 ndiwo apezeka, adatero Mbewe.
Ndipo Dr Phinias Mfune ku Karonga wati vutoli likukula chifukwa tsiku lililonse pakupezeka munthu mmodzi wotenga nthendayi.
| 6 |
Apha mkazi ndi apongozi kaamba kothetsa banja Mnyamata wina wa ku Mangochi wagwa mmanja mwa apolisi atapha mkazi ndi apongozi ake kaamba kothetsa banja.
Stephen Sani wa zaka 25 adavomera mlandu wopha mkazi wake Annie Smoke ndi apongozi ake, Enifa Smoke, ndipo pomwe timasindikiza nkhaniyi nkuti iye akuyembekezera kukaonekera ku khoti.
Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Sani adati adachita zaupanduzo kaamba koti makolo a mtsikanayo adathetsa banja lake ndi cholinga choti akapitirize maphunziro.
Mayi ndi gogo wa ophendwawo, Alida Moyenda, adati awiriwo adalowa mbanja atachimwitsana. Panthawiyo nkuti Annie ali ndi zaka 16, komanso ali folomu 1.
Gogo Moyenda adati poona kuti mtsikanayo adali wamngono, komanso wanzeru kwambiri pamaphunziro adaganiza zomubwezera kusukulu, koma mwamunayo adakana.
Timafuna Annie apitirize maphunziro, koma popeza mwamunayo amakana tidangoganiza zothetsa banja kuti pasakhale kupingana kulikonse, adatero gogoyu.
Iye adati banja la awiriwo lidatha pa August 5 2017 ndipo mtsikanayo adakayambiranso sukulu. Gogoyu adati banja la Sani ndi Annie mudalibe mavuto ena aliwonse, koma chomwe makolowo amafuna ndi choti mkaziyo aphunzire.
Padalibe mavuto ena aliwonse, koma chomwe chimatikhudza nchoti mtsikanayo adali wangono woyenera kukhala pasukulu osati pabanja, adatero Moyenda.
Mneneri wa polisi wa mboma la Mangochi, Amina Tepani Daudi, adati pa August 13 2017 Annie ndi amayi ake adatengana ulendo wokaona mbale wawo wina mmudzi mwa Mbapi mboma lomwelo.
Popeza mwamunayo amakhala moyandikana ndi makolo amtsikanayo, adadziwa za ulendowo ndipo adawatsatira mpaka pa famu ya Funwe pomwe adawaimitsa ndi kuwachita chiwembu.
Titalandira uthenga woti mu famu ya Funwe mwapezeka mitembo iwiri, tidaitengera ku chipatala chachingono cha Monkey Bay komwe adatiuza kuti anthuwo adamwalira kaamba ka kutaya magazi kwambiri atabaidwa ndi mipeni pakhosi, adatero Daudi.
Iye adati apolisi adagwira Sani pomuganizira kuti ndiye adachita zaupanduzo. Atamufunsa, adavomera mlanduwo moti akuyembekezera kuyankha mlandu wakupha womwe ukutsutsana ndi ndime 209 ya malamulo a dziko lino.
Akapezeka wolakwa, Sani akagwira ndende moyo wake wonse.
Mkazi wa mtsogoleri wa dziko lino, Gertrude Mutharika, wakhala akulimbikitsa atsikana omwe adalowa mbanja akadali a angono kuti abwerere kusukulu.
Malingana ndi kafukufuku wa mabungwe osiyanasiyana kuphatikizirapo la UNDP, atsikana ambiri mdziko muno amalowa mbanja asadafike zaka 18.
Mkulu wa bungwelo, Dan Odallo, adati vutoli ndi lomwe likuchititsa kuti atsikana ambiri azisiira panjira sukulu.
Pafupifupi theka la atsikana a mdziko muna amalowa mbanja asadafike zaka 18, adatero Odallo.
Pofuna kuthana ndi vutoli, Nyumba ya Malamulo idakhazikitsa malamulo woti atsikana azilowa mbanja akakwana zaka 18 kapena kupotsera apo.
| 7 |
Usi Wapempha Amalawi Alemekeze Mutharika Pomuchotsa pa Mpando Wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha UTM, Dr. Micheal Usi walangiza anthu mdziko muno kuti akavote pa chisankho chikudzachi ndi cholinga chochotsa President Peter Mutharika pampando.
Dr. Usi amalankhula izi mboma la Mangochi pamene amalandira a Yusuf Kusweje omwe anayimira ngati phungu mchipani cha UDF mdera lapakati mboma la Mangochi yemwenso anali wachiwiri kwa mkulu wokopa anthu mchipanichi yemwe tsopano walowa chipani cha UTM ndi akuluakulu ena asanu ochokeranso ku UDF.
Dr. Usi ati ulemu waukulu umene amalawi angapereke kwa President Mutharika ndi kukavota kuti asakhalenso mtsogoleri wa dziko lino ndipo azipuma.
Pamenepa iwo ati kulowa kwa anthu mchipanichi kukuwonetsa poyera chikhulupiliro chomwe ali nacho mu utsogoleri wa Dr. Saulos Chilima.
Tachilandira bwino kwambiri ndipo chilichonse chimayangana mtsogoleri ndipo mmene zakhaliramu zasonyeza kuti anthu ayamba kuzindikira, anatero Usi.
Polankhulapo a Yusuf Kusweje ati achita kampeni yamphamvu mboma la Mangochi ndi cholinga chakuti mgwirizano wa UTM ndi MCP upeze mavoti ochuluka mbomalo.
| 11 |
Apempha Boma Liyike Chidwi Mzipata za Mdziko Muno Mmodzi mwa anthu omwe amatsatira bwino nkhani zochitika mdziko muno a Coxley Kamange apempha boma kuti liyike chidwi chake pa zipata zolowera ndi kutulukira mdziko muno pofuna kuti nthenda ya COVID-19 isapitilire kufalikira mdziko muno.
Zipata za dziko lino zidakali zotsekula A Kamange amalankhula izi mu mzinda wa Blantyre pothilirapo ndemanga pa momwe boma likugwilira ntchito yolimbana ndi kufala kwa kachilombo komwe kakuyambitsa nthendayi ka Corona-virus mdziko muno.
Tati tipemphe ku boma kuti mmaboda mukhale chitetezo chokwanira poyika malo oti anthu obwera kuchokera ku maiko a kunja azisungidwa kumeneko kufikira masiku omwe achipatala akunena, anatero a Kamange.
Iwo anapemphaso boma kuti liyike nthawi zapadera zosiyana mmisika pofuna kuchepetsa chiwerengero cha anthu opezeka mmisikayi.
| 14 |
Milandu mbweee! mu 2016 Chapita chaka cha 2016 chomwe dziko lino lidaona ina mwa milandu ikuluikulu ikulowa mmabwalo a milandu ndi kuweruzidwa.
Umodzi mwa milanduyi udali wa yemwe adali nduna ya za chilungamo zaka zapitazo yemwenso ndi kadaulo pa malamulo, Ralph Kasambara.
Kasambara, pamodzi ndi Pika Manondo komanso MacDonald Kumwembe adayankha mlandu woti adakonza chiwembu chofuna kupha mkulu woyendetsa ndondomeko za chuma wakale Paul Mphwiyo mu 2013.
Kasambara (wasuti) kupita kundende Mwezi wa July, bwalo la milandu lalikulu mumzinda wa Lilongwe lidamupeza Kasambara wolakwa pamlanduwo ndipo mwezi wa August adagamulidwa kukasewenza jere kwa zaka 13.
Manondo ndi Kumwembe adagamulidwa kukasewenza jere zaka 15 ndi 11 aliyense pa milandu iwiri: yochita upo pofuna kupha komanso mlandu wofuna kupha Mphwiyo panja pa nyumba yake ku Area 43 mumzinda wa Lilongwe usiku wa September 13 chaka cha 2013. Milanduyi asewenza paderapadera. Pamodzi, Mandondo ndi Kumwembe asewenza zaka 26.
Mlanduwutu tsopano uli kubwalo la apilo.
Mchakachi tidaonanso fisi wa ku Nsanje, Eric Aniva, akukalowa mchitokosi pogona ndi amayi 104 mbomali.
Aniva yemwe ndi wa zaka 45, wochokera mmudzi mwa Tosina kwa mfumu yaikulu Mbenje, mbomalo adapezeka wolakwa pa milandu iwiri yokhudza kuika miyoyo ya ena pachiswe potsatira miyambo ya makolo.
Aniva adanjatidwa pomwe adauza wailesi ya atolankhani a British Broadcasting Corporation (BBC) za ufisiwu mwezi wa July.
Ngakhale Aniva adaukana mlanduwu pa November 22, woweluza milandu Innocent Nebi adamugamula kukasewenza zaka ziwiri ku ndende. Padakali pano, womuyimira Michael Goba Chipeta wachita apilu.
Nawo mlandu wa mtsogoleri wagulu lomenyera ufulu wolanda malo mmaboma a Thyolo ndi Mulanje la Peoples Land Organisation (PLO) Vincent wandale udali mkamwamkamwa mwa anthu mchakachi.
| 7 |
Anatchezera Akufuna mwana Zikomo Gogo, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Banja ndi mwamuna wanga lidatha mu 2011. Ndidapeza mwamuna wina yemwe timamvana ndipo tidakayezetsa komwe adatipeza kuti tilibe kachilombo koyambitsa Edzi.Vuto ndi lakuti bwenzi langalo limakonda zogonana komanso limandiletsa kuchita za kulera. Wina adandiuza kuti bwenzi langalo lili ndi mkazi koma nditamufunsa adakana. Tsiku lina ndidaimba foni 5 koloko mbandakucha ndipo ndidamva kulira kwa mwana wa khanda. Nditamufunsa adakana ndipo adati ndi wa khomo loyandikana nalo. Ndizimukondabe? R, Chiradzulu Wokondeka R, Mwakumana ndi chilombo cha bodza. Wakunamizani kuti akufuna mwana chonsecho pansi pamtima akudziwa kuti akakupatsani mwana adzakuthawani nkupitiriza kukhala ndi mkazi wake. Wakunamizaninso kuti mwana amalira ndi woyandikana nawo nyumba. Ngati zili zoona, bwanji adadula foni? Asakutayitseni nthawi ameneyo.
| 15 |
Za maukwati, mabanja Money is gooooood Musayense njerego, awa ndi mawu ochokera munyimbo ya Miracle Money ya mnyamata wodziwa kuimba nyimbo zauzimu, Onesmus. Poyamba, ndinkamva ngati akuti God is good! Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Iyitu ndi nyimbo yauzimu imene imakamba za ndalama zozizwitsa zimene zingapezeke mkachikwama kanu kapena kubanki modabwitsa. Akhoza kukhala mamiliyoni. Si za kashigetitu! Major do it! Major do it! Pamenepanso ndimayesa akuti God do it! God do it! Zoona, ambiri timalambira dzuwa mmalo molambira wolenga dzuwalo.
Musayambe kundinena kuti ine zindikhudza bwanji. Inetu ndimakhulupirira kwambiri Mateyu 7 vesi ya 1: Osaweruza ena chifukwa ndi mlingo umene uweruzira ena, nawenso udzaweruzidwa. Ndine ndani ine, kapunthabuye, kafucheche, kwakwananda ndipo ndikadakhala nsalu bwenzi ndili kilimpulini.
Sindinakumalizireni nkhani ija sabata yatha. Tidaika zovuta kumanda ena pafupi ndi pa Wenela. Ubwino wake, wotisiyayo adali atagula kale puloti yake kumasanoko.
Titaika zovutazo, mkulu wina adanditengera pambali: Tade kodi panthumbira paja anaikapo maluwa chifukwa chiyani? Kodi malemuwo adali kalipentala? Nanganso anaikapo mtanda wa thabwa, kodi malemuwo adali kalipentala? Sindikaika kutsogoloku adzawaka mandawo ndi simenti ndi quary ngati malemuyo anali kontilakita.
Sindidamuyankhe.
Titafika malo aja timakonda pa Wenela, kudatulukira mkulu wina atanyamula zibonga ndi mikondo.
Tiwaphe basi! Amenewa aphedwe basi! Ndithu pa filling station munthu angathire mafuta kotulukira utsi? adafunsa mkulu wa zikwanjeyo.
Dzina lake ndi Nike Masonda, mnzake wa Adona Hilida ku Polisi Palibe. Tsono akadati alowe kumpanda ku Sanjika bwenzi ataika malamulo wotani mkuluyo? Zidandipita.
Koma Abiti Patuma akuoneka kuti adazitolera. Pezani zina zokamba. Ndimayesa muzinena za chimbudzi choyendayenda cha Moya Pete. Zomwe mukunenazo tidazimva kale. Ati Mugabe adawauza akwatirane ndipo mubadwe mwana, apo ayi awakhiya pakhosi, adatero.
Ndipo izo zili apo, tidamvaponso za wina amene ankanena kuti satana akadakhala wa maganizo otere bwenzi atapusitsa Adam osati Hava kuti adye chipatso cha pakati pamunda. Koma zochitika kuchipinda kwa wina inu zimakukhudzani chiyani? adafunsa Abiti Patuma.
Mkulu uja adati: Musathe mpweya, malamulo amaletsa kuchita zosayenerazi. Ngakhale malembo oyera amaneneratu.
Malamulowo amaneneratu kuti si bwino kugonana motsutsana ndi chilengedwe. Titati tilowe mzipinda mwa inu mukudzitcha olungama sitikapeza mukuphwanya lamulo? adaphaphalitsa funso Abiti Patuma.
Abale anzanga, mwinatu mukufuna kumva maganizo anga pankhaniyi. Ndine mmodzi mwa anthu amene amakhulupirira kuti ngakhale nyerere zimadziwana kuti iyi ndi yaimuna, iyo yaikazi, chimodzimodzi agalu, abakha, nguluwe ndi akamba. Chinanso nchakuti tikadati tonse tiziganiza chomwechi, bwenzi dziko ndi anthu ake alipo? Koma mbali inayi, zochitika kuchipinda kwa ena ine sizindikhudza; ndilibe nazo ntchito. Pamene ena akuchita kusaweruzika ine sindikhala nazo ntchito.
Zonse zili apo, ndimakhulupirira kuti chilengedwe chiyenera kutsatidwa basi. Ndimaopa kuti zipata zitatsegulidwa, mwana wanga Zeno akhoza kuona ngati kukhalira limodzi atambala okhaokha palibe chachilendo.
| 15 |
Zikhulupiliro Zikukolezera Milandu Yogwililira ku Ntchisi Zikhulupiliro akuti ndi zimene zikukolezera kuchuluka kwa milandu yogwililira mboma la Ntchisi.
Kaponda: Ena amawona ngati akhwima Wofalitsa nkhani za apolisi mbomalo Richard Kaponda wauza Radio Maria Malawi kuti pali anthu ena omwe amaganiza kuti akagona ndi mwana wachichepere achira ku matenda a edzi, komanso ena amatenga zizimba zochitira bizinesi.
Komabe Kaponda wati kudzera mu ntchito yawo yozindikirtsa anthu za kuyipa kwa mchitidwewu, milanduyi yatsikirapo mmiyezi itatu yapitayi poyerekeza ndi miyezi ngati yomweyi chaka chatha.
Malinga ndi Kaponda, bomalo linalandira milandu yogwililira 15 mmiyezi ya January mpaka April 2019 ndipo mchaka cha 2020 bomalo lalandira milandu ya mtunduwu yokwana 13.
| 14 |
Anthu Osadziwika Avulaza ma Monita a Chipani cha UTM ku Mulanje Anthu ena omwe sakudziwika avulaza mamonitor a chipani cha UTM pa malo ena ochitira kalembera wa chisankho mdera la kumwera kwa boma la Mulanje.
Anathawitsidwa ndi apolisi-Kaliati Malinga ndi ofalitsa nkhani za apolisi mbomalo Gresham Ngwira, anthuwa atavulazidwa anapita ku polisi kukadandaula ndipo akuluakulu ena a chipanichi omwe ndi a Patricai Kalioati komanso a Bon Kalindo anafikanso ku polisiko kuti akamve mmene zakhalira.
Koma anthu ena akuti anayamba kuwowoza akuluakuluwa komanso kuwatsekera njira zomwe zinachititsa kuti apolisi aponye utsi wokhetsa msonzi ndi kubalalitsa anthuwo Anthu ena omwe ndima monitors achipani cha UTM avulazidwa pa malo olembetsera kalembera wa chisankho ndi anthu omwe sakuziwika ndipo atsogoleri awo anafika ku polisi kuti adzawaone koma posakhalitsa kunabwera gulu la anthu ena lomwe linayamba kuwawowoza atsogoleriwo, anatero Ngwira.
| 11 |
Papa Wapempha Akhristu Athandize Anthu Ovutika Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wati kusamalira anthu ovutika komanso okalamba ndi njira yokhayo yoonetsa kuti akhristu mu mpingowu amaopa Mulungu.
Papa Francisko Papa amayankhula izi pa mwambo wa misa yomwe watsogolera ku likulu la mpingo-wu ku Vatican.
Iye wati panthawi ino pomwe anthu ambiri akunva zowawa kumanso kuvutika kamatenda a COVID-19 akhristu akuyeneranso kumadzipereka pothandiza ndi kusamalira anthu ovutika ndikupitiliza kutetedza anthu okalamba.
Kumbari ya mantha omwe adza kamba ka matenda a COVID-19 ndi zina zopinga Papa Franciso wati anthu omwe amakhulupilira Mulungu sakuyenera kuchedwa ndi kuchita mantha koma kupempha mulungu kuti awachotsere zovuta zomwe zawagwira pakati pawo.
| 14 |
Boma likukhazikitsa misika ya zakudimba Boma lili mkati momanga malo ogulitsira zokolola zakudimba ngati njira imodzi yochulukitsira phindu lomwe alimi amapeza pogulitsa zokolola zochokera mu ulimi wamthirira.
Ntchitoyi ndi gawo limodzi la ntchito yotukula ulimi wamthirira pokonzanso masikimu 11 mchigawo cha zaulimi cha Blantyre Agricultural Development Division (ADD).
Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mkulu woyanganira ntchito yotukula zipangizo za ulimi wamthirira, Cosmos Luwanda wati misikayi, yomwe ilipo 6, imangidwa ku Neno ndi kuchigwa cha mtsinje wa Shire.
Iye wati ntchitoyi, yomwe ikugwirika ndi thandizo la ndalama zokwana 12 biliyoni kwacha kuchokera ku African Development Bank (ADB), imanga manthu wa misika mumzinda wa Lilongwe komwe kutakhale zipangizo zapamwamba zotha kusungira ndiwo zamasamba ndi zipatso kwanthawi yaitali.
Cholinga cha misikayi ndi kulumikiza alimi ndi ogula mosavuta, adatero Luwanda.
Mkulu woyanganira ntchito yomanga msika wa zokolola za kudimba wa Chikwawa, Khama Kammwamba, adati malowa adzakhala ndi malo osungira zokolola, malo otsukira zokolola, magetsi, madzi apampopi ndi zimbudzi zamakono.
Misikayi izidzagulitsa zokolola mwachipiku kwa amalonda ochokera kutali. Adindo oyendetsa masikimu ndi amene azidzayendetsa misika imeneyi, adatero Kammwamba.
Padakalipano ntchito yokonza masikimu amene ali mupolojeikiti imeneyi ili mkati ndipo masikimuwa akuyembekezeka kuyamba kugwira ntchito yawo usanafike mwezi wa June chaka chamawa.
| 4 |
Abwenzi Ayamikira Dongosolo la Mariatona Wolemba Richard Makombe Abwenzi a Radio Maria Malawi ati ndi okhutira ndi momwe nyengo ya Mariatona yayendera chaka chino.
Mariatona ndi nyengo imene Radio Maria imakonza chaka chilichonse pofuna kupeza thandizo loyendetsera ntchito za wayilesiyi komanso kubwenza ngongole zomwe wayilesiyi ili nazo.
Ena mwa abwenzi a wailesiyi ku mwambo wotsekera Mariatona ku Dedza Wapampando wa Abwenzi a Radio Maria mu dayosizi ya Blantyre a James Ngombe awuza Radio Maria Malawi kuti kuyambira pomwe Mariatona inayamba mwezi wa May akhala akutsatira bwino mwa chidwi ndipo ndi osangalala kuti zinthu zayenda bwino mpaka kufikira kumapeto pomwe nyengo ya Mariatona yatsekedwa.
A Ngomba ati ngakhale panali zovuta zina monga kusowa kwa mabuku olembapo mmene munthu waperekera thandizo lake anthu ambiri ayesetsa kuthandiza wayilesiyi.
Ndipemphe kwa akuluakulu kuti ayesetse kuti mabuku olemberapo maina a anthu omwe apereka thandizo lawo ku wayilesiyi azifikira anthu aku midzi komwe nawo azithandiza wayilesiyi, anatero a Ngomba.
A Ngomba apempha akhristu komanso antu kuti apitilize kuthandiza wayilesiyi ngakhale Mariatona yatsekedwa pa 27 July 2019.
Poyankhulapo wapa mpando wa Abwenzi a Radio Maria mu dayosizi ya Dedza mayi Elina Tcheza wati iwo ndiokondwa kuti zomwe anakonza kuti zichitike potsekera Mariatona zachitika ndipo zayenda bwino.
Ndithokoze onse omwe anatengapo mbali poonesetsa kuti Mariatona wa chaka chino akhale wapamwambaanatero a Tcheza.
A Tcheza ati ngakhale panali zovuta zina komabe zambiri zayenda bwino Kamba koti anthu ambiri athandiza ndi katundu osiyansiyana.
Mariatona inatsegulidwa pa 4 May ku Zomba Cathedral ndipo yatskedwa ku Mtendere Parish mu dayosizi ya Dedza.
| 13 |
Galu kusaka mbuyake
Nkhani ya agogo anayi amene adaphedwa ku Neno kaamba koganiziridwa kuti adapha munthu mmatsenga idakhudza Amalawi ambiri. Zoona, ngakhale mkulu wa apolisi Lexten Kachama amene Lachitatu adapita komweko kukalangiza anthu za milandu yokhudza ufiti. Chomwe chidapatsa ena chidwi ndi galu ali apayu amene amaoneka kuti amasakasaka mbuye wake. Galuyo adalowa mgulu la anthu nkubwerera osapeza mbuye wakeyo. Kapena naye amangofuna kumva nawo uthenga wa ufitiwo? | 15 |
Ulimi wamthirira usangokhala nyimbo Mkonzi, Ndimamva chisoni njala ikamagwa mdziko muno chifukwa choti mwagwa chilala pamene tili ndi nyanja ndi mitsinje yambiri yomwe simaphwera nthawi yachilimwe, zomwe zingatithandize paulimi wamthirira.
Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mthirira ungatipulumutse Kodi, Amalawi anzanga, ndi zoona tizifa ndi ludzu mwendo uli mmadzi? Ndithudi maiko a anzathu amene sadadalitsidwe ndi nyanja ndi mitsinje ngati ku Malawi kuno amaseka chikhakhali akationa tikupempha chakudya kumaiko ena chonsecho tili ndi kuthekera kopeza chakudya chokwanira chaka ndi chaka choti chikhoza kudyetsa fuko la Malawi chaka chathunthu popanda vuto lililonse.
Vuto ndi boma lathu lomwe limatsogoza ndale kuposa chitukuko cha dziko ndi miyoyo ya anthu ake. Ndi liti lija adayamba za kulimbikitsa ulimi wamthirira pofuna kuthetsa vuto la njala mdziko muno? Tonse tikudziwa bwino za nkhambakamwa ya Green Belt Initiative. Ndani lero angandilozere kuti Green Belt ili apa? Tidamva zoti boma lagula mathirakitala kuchokera ku India kuti athe kuthandiza alimi mmidzimu pachitukuko cha ulimi. Ali kuti ndipo akuchita nawo chiyani pano? Kugula chakudya kumaiko akunja pofuna kudyetsa fuko la Malawi kuli apo, ndi bwino koposa kuti boma likhazikitse mfundo zolimbikitsa ulimi wamthirira mmbali mwa nyanja ya Malawi ndi kuchigwa cha Shire komanso mmbali mwa mitsinje ina monga North ndi South Rukuru, Runyina, Limphasa kuchigawo cha kumpoto; mitsinje ya Linthipe, Lilongwe ndi Bua mchigawo cha pakati; mitsinje ya Thutchira ndi Ruo kummwera mongotchurapo malo ochepa.
| 2 |
Apolisi alandira uphungu paziphuphu Bungwe lolimbana ndi mchitidwe wa ziphuphu ndi katangale la Anti-Corruption Bureau (ACB) laphunzitsa apolisi a mumzinda wa Mzuzu za momwe angapewere mchitidwewu.
Malingana ndi kafukufuku yemwe lidachita bungwe la Centre for Social Research mu 2013 nthambi ya polisi ya Road Traffic and Safety Services lidapezeka kuti ndiyo ili patsogolo polandira ziphuphu komanso kuchita za katangale mdziko muno.
Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Kafukufukuyo adapezanso kuti nthambi ya Road Traffic Commission nayo ili patsogolo kuchita mchitidwewu.
Mmodzi mwa akuluakulu olimbana ndi mchitidwewu kubungwe la ACB, Patrick Mogha, adati iwo adachiona chofunika kuti awaphunzitse apolisi komanso anthu a madera ozungulira pankhani za ziphuphu kuti athandize kuchepetsa mchitidwewu.
Tidaona kuti ndi chinthu chanzeru kuti tiwaphunzitse a polisi za momwe angapewere kapena kudziteteza kumchitidwe wakatangale ndi ziphuphu. Tidazindikira kuti anthu ena pochita mchitidwewu sadziwa kuti akulakwira malamulo komanso akubwezeretsa chitukuko cha dziko mmbuyo, adatero Mogha.
Mogha adaonjeza kuti iwo ali ndi chikhulupiriro kuti akaphunzitsa apolisi zithandiza kuchepetsa mchitidwewu.
Wachiwiri kwa komishonala wa polisi, yemwenso ndi mkulu wa nthambi yoonetsetsa kuti apolisi akuchita zinthu moyenera (Professional Standards Unit), Esther Wandale, adati iwo ali ndi cholinga chothana ndi mchitidwe wa katangale ndi ziphuphu pakati pa apolisi ndipo ati ali ndi chikhulupiliro kuti zinthu zisintha.
Cholinga chathu ndi kulimbikitsa apolisi athu kuti azikhala otsata malamulo komanso odalirika. Izi ndi zikhoza kutheka pokhapokha iwo akudziwa kuti katangale ndi chiyani kwenikweni, adatero Wandale.
Mmodzi mwa oyendetsa galimoto zahayala (taxi), Happy Soko, adati akuona kuti maphunzirowa athandiza kuchepetsa mchitidwe wa ziphuphu ndi katangale pamsewu.
Iye idadati apolisi ndi omwe amathandiza kulimbikitsa mchitidwewu pamsewu chifukwa akadakhala kuti amatsatira malamulo moyenera si bwezi oyendetsa galimowo akuchita mchitidwewu.
Maphunzirowa athandiza koma ndikuona kuti akadaphatikizanso anthu ngati ife zikadathandiza kuthana ndi vutoli mwachangu, adatero Soko.
| 7 |
Atsikana Osiyira Sukulu Panjira Akuchulukira ku Ntcheu Ofesi yoona za maphunziro mboma la Ntcheu yalimbikitsa atsikana kuti azipitiriza maphunziro awo pofuna kuti atsikana akhale ozidalira pa nkhani za maphunziro mdziko muno.
Mlangizi wazamaphunziro mbomali mu zone ya Bunyenga a Sidney Makwecha anena izi pambuyo pa ulendo wao wokayendera maofesi a boma la Ntcheu ndi atsikana ochokera pa school ya Saiwa komwe ndi dera lomwe lili ndi atsikana ochuluka osiyira sukulu panjira mbomalo.
A Makwecha ati atsikana ambiri sakupitiriza maphunziro awo kaamba kopatsidwa pathupi zomwe zinachititsa kuti ofesiyi pamodzi ndi amayi ogwira ntchito zosiyanasiyana atsikanawa akazionere okha mmaofesiwa mmene amayi akugwirira ntchito zawo kuti atengerepo chitsanzo pa amayiwa.
Taona kuti atsikana ambiri mderali akumasiyira sukulu panjira nde tinawatengera ku boma la ntcheu kuti akakumane ndi amayi anachita bwino pa maphunziro ndipo akuwoneka kuti pamapeto pa ulendowu anawa aphunzirapo kanthu, anatero a Makwecha.
Sukulu ya Saiwa ili ku dera la kumudzi ndipo ana ambiri amasiyira sukulu panjira kaamba ka moyo otengera makhalidwe achitawoni zomwe zikumachititsa kuti anawa azitenga pathupi adakali aangono.
| 3 |
Anatchezera Chikondi amatero? Agogo, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndine mtsikana wa zaka 20 ndipo ndili kukoleji. Ndili ndi chibwenzi chomwe tidagwirizana kuti tidzamange banja mtsogolo muno. Mnzangayu amati akufuna kuti adzandidziwire mbanja chifukwa akayamba kundigona panopa atha nane filimu. Ndiye akuti poti iyeyu ndi munthu pena zimavuta ndiye akuti akufuna apeze mkazi woti azigonana naye popewa kugonana ndi ine kuti inyeyo adzandikwatire. Kodi kumeneku ndi kukonda? Ndithandizeni, agogo, nditani.
Ndine L, Lilongwe Wokondeka L, Bwenzi lakolo ndi munthu wachilungamo, inde, koma chilungamo chake chaonjeza. Munthu wotere osamukhulupirira chifukwa ndi kamberembere. Iyeyu wanena chinthu chanzeru kwambiri kuti pakalipano musamagonane chofukwa akuopa kuti akatero atha nawe chilakolako chifukwa wakudziwa. Koma akuti akufuna apeze mkazi wina wapambali kuti azikapumirako poti iye ndi munthu, nanga iwe wakuuza kuti nawe utha kupeza wina woti uzicheza naye pamene mukudikira kuti mudzakwatirane? Akunama ameneyo; akufuna kuti azioneka ngati munthu wokhulupirika pomwe ndi wachimasomaso ndi akazi ena. Tikamati kudzisunga ndi nonse awiri, osati wina aziti mnzangawe udzisunge koma ine ndikayendayenda. Kunjaku kwaopsatu, ndiye wina azipanga dala zachibwana ngati zimene akunenazo, si zoona ayi. Ngati ndi wachilungamo, iyenso ayenera kupirira kuchilakolako cha thupi kufikira tsiku lomwe mudzalowe mbanja. Koma ngati adayamba kale zogonana ndi akazi ena, mchitidwe umenewo sadzausiya. Ndiye, kunena zoona, mwamunayo sali woyenerera kumanga naye banja chifukwa alibe chikondi chenicheni ndi iwe. Amati mbuzi ikalawa mchere sigwirika! Safuna zoyezetsa Anatchereza, Ndakhala ndili pachibwenzi ndi mtsikana wina kwa chaka chimodzi ndipo timakondana kwambiri. Ndine Mkhristu ndipo ndikhulupirira kuti sibwino kumagonana ndi wachikondi wako musadalowe mbanja lomanga. Ndakhala ndikumva malangizo oti masiku ano ndi bwino kukayezetsa magazi musanaganize zolowana, koma mnzangayu nditamuuza zimenezi adati ine zimenezo ndiye ayi. Kumufunsa chifukwa chake adati ineyo ngati ndikudzikaikira ndipite ndikayezetse, osati iyeyo. Akuopa chiyani? MJ Lilongwe Odi MJ, Akuopadi chiyani ameneyo? Pati bii, pali munga, ife akale timatero. Chilipo chimene akuopa chifukwa akanakhala kuti ali bwinobwino, si bwenzi akuchita kukanira patalitali kuti ine toto, pita wekha. Kudziwa mmene munthu ulili usanalowe mbanja ndi chinthu chabwino kwambiri, makamaka masiku ano pamene kuli mliri wa kachilombo ka HIV/Aids. Mundimvetse bwinobwino pamenepa: si kuti munthu akapezeka ndi HIV ndiye kuti sayenera kukwatira kapena kukwatiwa, ayi. Munthu aliyense ali ndi ufulu wokhala pabanja, koma zimakhala bwino kudziwa mmene mthupi mwako mulili pofuna kukonza tsogolo la banja lanu. Ngati wina apezeka ndi kachilombo kapena matenda ena kumphasa mumadziwa chochita pofuna kudziteteza kuti nonse mukhale moyo wathanzi. Komanso ngati mukufuna mwana mbanja mwanu madotolo amadziwa njira zokuthandizirani kuti mwana wanu asatenge nawo kachilomboko. Chachikulu ndi chikondi pakati panu-pali chikondi palibe mantha. Mufotokozereni wokondedwa wanuyo zimenezi kuti amvetsetse, koma ngati akumenyetsa nkhwangwa pamwala, musiyeni ameneyo, muyangane wina amene angakumvetsetseni pankhani yoyezetsa magazi.
Nsalu ya lekaleka Anatchereza, Ine ndi mwamuna wanga takhala pabanja zaka ziwiri ndipo nthawi yonseyi takhala tikugwiritsa ntchito njira zolera chifukwa mwamuna wanga amati nthawi yoti tikhale ndi mwana sinakwane-titoleretolere kaye kuti tisadzavutike tikadzakhala ndi mphatso ya mwana mnyumba mwathu. Kunena zoona zimene amati titoleretolere kaye sindikuziona, komanso anthu kunjaku ndiye akumatiseka ndi kumatinyogodola kuti sitibereka. Ine ndiye ndatopa nazo zimenezi.
KB Mzimba KB, Nkhani yanu ndi yovuta kuimvetsa, komabe ndikuthandizani. Choyamba, kodi pamene mumagwirizana zomanga ukwati wanu, mudayamba mwakhala pansi nkukambirana za mapulani anu pa nkhani yokhala ndi ana kapena izi munagwirizana mutalowana kale? Ndikufunsa chifukwa ukwati ndi anthu awiri. Ine ndikuona ngati mwamuna wanu chilipo chimene sakufuna kuti mudziwe ndipo akunamizira kuti nonse mukulera. Zaka ziwiri mukutolera za mwana? Mukutolera chiyani? Mwanena kale kuti palibe chimene mukuona kuti mwatolerapo mpakana pano. Mumufunse ameneyo kuti nthawi yakwana tsopano kuti mulandire mphatso yomwe mwakhala mukuiyembekeza ija. Mumuuze kuti simupanganso zolera koma zenizeni, mumve chimene ayankhe. Ngati pali vuto lomwe akuchita nalo manyazi kukuuzani, mumuuze kuti asaope chifukwa inu ndi thupi limodzi-mavuto ake ndi anu omwe. Kuli asinganga odziwa kusula kunja kuno! Akakanika, kuchipatala amathandizanso! Ndani safuna mwana? Sakundilankhula Zikomo Anatchereza, Ndili pabanja ndi mkazi wina ndipo timakondana kwambiri. Koma akwawo sagwirizana nawo ndipo ngakhale akumane panjira salankhulana. Ngakhale ine ndikawalankhulitsa sandiyankha. Ndichitenji chifukwa ndikuopera mawa atadwala kapena kumwalira kumene. Thandizeni.
| 12 |
Nanawa: Mlowammalo wa kupitakufa Matenda a HIV/Edzi asokoneza miyambo ina monga mwambo wa kupitakufa, womwe umapereka mphamvu kwa fisi kuti akakonze maliro pocheza ndi namfedwa kwa sabata ziwiri ndipo machezawo amachitika katatu patsiku. Chifukwa cha matendawa, kwabwera njira ya nanawa yomwe yazilalitsa mwambo wa kupitakufawu. BOBBY KABANGO adali mboma la Nsanje komwe adacheza ndi mlembi wa nyakwawa Masanzo kwa T/A Mlolo.
Chisale watuluka nkumangidwanso Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Kodi amfumu tawapeza? Ayi, iwowa adzukirira kudimba. Akuyembekezereka kubwerako madzulo chifukwa ntchito yakula kumeneko.
Tidalire kuti inu mutithandiza pa vuto lathu? Musakaikenso, ndine mlembi wa amfumuwo ndiye palibe chomwe sindikuchidziwa chokhudza mudzi uno ndi miyambo yomwe timatsata.
Mkaka: Mwambo wa nanawa timangomwa mankhwala othamangitsa imfa Kodi mwambo wa kupitakufa ukuchitikabe kuno? Zikuchitika koma mobisa chifukwa momwe matenda a Edzi aopseramu sungayerekeze kumachitabe mwambowu. Amabungwe akhala akufika kumemeza anthu kuti miyambo yoipa, monga umenewu, itheretu ndipo zipatso zake zikuonekadi pano.
Ndiye mukutani kuti imfa ithawe pakhomo? Timagwiritsa mankhwala a nanawa amene amathamangitsa imfa pakhomo. Kuno anthu ambiri tikutsata zimenezi.
Nanawa nchiyani? Ndi mankhwala amene singanga amachita pakhomo pamene pagwa maliro. Anthu, maka achibale, amamwa mankhwalawo molandirana ndipo pakhomopo pamakhala bwino.
Zimachitika nthawi yanji? Maliro akachitika monga lero, mawa timakaika ndiye timasweretsa tsiku limodzi pamene timasonkhana kudzasesa. Nthawi yosesa mpamene mwambo wa nanawa umachitika. Mungathe kuchita mwambowu nthawi iliyonse kaya ndi masana kapena madzulo.
Kodi mankhwalawa mumatemera kapena mumadya? Mankhwalawa ali pawiri. Ena amakhala a madzi. Amawaika mkapu ndiye aliyense wachibale amalandirana mankhwalawo kumamwa pangono mpaka nonse achibale akukwaneni. Pamene mankhwala ena amawaika kudenga kwa nyumba yomwe mumagona malemuwo. Mumawasomeka kudenga mbali yomwe kuli khomo kuti anthu akamalowa mnyumbamo azigwira mankhwalawo.
Mukutanthauza wachibale aliyense amayenera amwe mankhwalawo? Zimatero kumene. Nonse mumalandirana, kumwa pangono basi, aliyense kamodzi komanso momapatsirana.
Nanga achibale amene sadafike pamwambowo mumawatani? Achibale amene nthawi ya malirowo kapena tsiku la kusesalo palibepo, timawasungira mankhwalawo. Mankhwala ake ndi amene tawasomeka kudenga aja. Tsiku lomwe akonza zodzafika pakhomopo, timawalandira ndi kuwatengera kunyumba yomwe kudachitika malirowo. Ndiye pamene tikulowa mnyumbayo, timawapatsa mankhwala aja kuti agwire. Akangotero basi amabwezeretsa mankhwalawo kudengako.
Amachitanso china chiti? Palibe, ngati agwira mankhwalawo ndiye kuti nawonso akonzedwa ku imfa yomwe idakangogwa pakhomopo.
Nthawi yomwe munkatsata mwambo wa kupitakufa zinkakhala bwanji? Maliro akachitika chonchi, timapeza fisi kuti apite kunyumba yomwe kwachitika malirowo akacheze ndi namfedwayo. Katatu patsiku kapena zikavuta atha kumacheza nawo kawiri patsiku kwa sabata ziwiri. Fisiyu ntchito yake idali yoti achotse mzimu wa imfa womwe wakuta pakhomopo.
Mpaka katatu? Ndiye zidalikolikotu Hahaha! Eeh, amasangalala kwambiri koma pano zimenezi zidatha.
Nanga akamwalira wamkazi, afisi aakazinso amapezeka? Ayi, zikatere ndiye tinkapanga mankhwalawa kapena apo ayi mupemphe banja lina kuti likupitireni kufako.
| 6 |
Kusamala anapiye a mikolongwe Amati nkhuku ndi dzira, kusonyeza kuti ngati susamala dzira ndiye kuti udzalandira nkhuku za matenda zomwe sizichedwa kufa. Komanso kupanda kusamalira bwino anapiye, akhonzanso kufa. Koma chisamaliro ichi nchotani? BOBBY KABANGO adakacheza ndi Rose Mphepo, mphunzitsi wa kusukulu ya ziweto ya Mikolongwe mboma la Chiradzulu. Adacheza motere: Tidziwane mayi Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndine Rose Mphepo. Ndine Assistant Hatchery Managerwachiwiri kwa woyanganira malo oswera nkhuku. Koma tikuopeni? Mphepo kuyanganira anapiye Tikufuna timve momwe tingasamalire anapiye a mikolongwe. Kuno tilibe nkhuku mtundu wake mikolongwe. Anthu amangoti nkhuku za mikolongwe, koma palibe mtundu wa mikolongwe. Nkhuku zimenezi ndi ma Black Austrolorp koma chifukwa zimachokera kuno, anthu amangoti mikolongwe. Ndikufotokozerani momwe timasamalira anapiye koma tipite kuofesi kwathuko. Tsono tidaika madzi amene mukaponde musadalowe kuofesiko, madzi amenewo ndi a mankhwala kuti musabweretse matenda kukholako.
Chisamaliro cha anapiye amtundu umenewu chimakhala chotani? Ngati ukufuna kuweta nkhuku zimenezi, choyamba samala mazira. Ndiye tili ndi khola ilo lomwe tikusungako nkhuku 300. Tambala mmodzi ali ndi misoti 10. Zimaikira komweko ndipo mmawa cha mma 10 koloko timakatolera mazira komanso madzulo cha mma 3 koloko.
Mazira amenewa amapita kuti? Tikatolera, timapita nawo ku hatchery. Iyi ndi nyumba yofungatilitsa mazira kuti anapiye atuluke. Koma tisadawaike mnyumbayi, timawaika mu Egg Chamber. Awa ndi malo amene timasankhira mazira. Timaikapo zongendawa amene amapha timajeremusi tomwe dzira latenga kuchokera kukhola kuja. Timawasungamo kwa sabata imodzi. Tikawatulutsa mmenemu ndiye timawaika moti akafungatilitsidwe. Dzira ndi chinthu cha moyo, ngati taliyika mu incubator lili ndi majelemusi, ndiye kuti anapiye adzabadwanso ndi matenda. Komanso panthawiyo timasankha mazira amene ali ndi mavuto monga amene ali angonoangono komanso osweka.
Fotokozani zomwe zimachitika mu incubator-mo.
Incubator yathu imalowa mazira 30 000 koma chifukwa cha mavuto ena, sitikwanitsa kuikamo mazira 30 000, mapeto ake timangoika momwe tapezera koma sabata iliyonse Lachiwiri timatulutsa anapiye 4 000. Mavuto enanso nkuti tilibe zakudya zokwanira zosamalira anapiye ngati achuluka. Tikawaika mmenemu, timadikira padutse masiku 18, apa timasankha mazira amene satulutsa anapiye. Dziwani kuti tambala akaphonya pamene akukwera thadzi, dzira limenelo limakhala lakufa loti simutuluka napiye.
Zimakhala bwanji kuti Lachinayi lililonse muzitulutsa anapiye? Nchifukwa choti sitiika mazira 30 000 monga ilili incubator-yi. Ndiye sabata ino timaikamo mazira, ena timaika sabata yotsatira, zomwe zimachititsa kuti anapiye azitulukanso mosiyana. Ena amatha masiku 21 sabata ino pamene ena sabata ya mawa.
Kodi anapiye sangapse mmenemu atati atuluka chifukwa cha kutentha? Kutentha kwa incubator ndi kofanana ndi nkhuku, timaonetsetsa kuti incubator ikutentha madigiri 37.5.
Magetsi akazima zimakhala bwanji? Magetsi akazima mutha kulumikiza jeneleta koma ngati mulibe ndiye azime kwa masiku awiri mutafungatilitsa mazira amene adutsa masiku 18, ndiye mazira onse amaonongeka. Amenewo katayeni chifukwa anapiye amakhala afa.
Anapiye akabadwa, mumalowera nawo kuti? Amabwera mnyumba iyi. Ndi motentha chifukwa amakhala mwana wathu ali mchikuta. Kupanda kutentha kumeneku samachedwa kufa chifukwa ndi osakhwima.
Katemera mumawapatsa atakula bwanji? Tsiku lomwe abadwa timapereka katemera woteteza ku matenda. Kenaka timawapatsa madzi ndiye timadikira padutse mphindi 30 tisadawapatse zakudya. Zikatha sabata imodzi, timazipatsa katemera wa gumbolo, sabata yachiwiri timazipatsa katemera wa LaSota, sabata yachitatu timawapatsa gumbolo, yachinayi LaSota, ndipo yachisanu wa firepox. Sabata ya 6 timawagulitsa kwa alimi ndipo mlimi savutika nazo. Alimi amagula K500 mwanapiye mmodzi.
Nanga zakudya? Zakudya timapanga tokha, zikangobadwa kumene mpaka atakula timawapatsa chicken mash.
| 4 |
Apempha Akatolika Amvere Maepiskopi Awo pa Kapewedwe ka Coronavirus Akhristu a mpingo wa katolika mdziko muno awapempha kuti atsatire ndondomeko zomwe maepiskopi awo ananena kudzera muchikalata chomwe analemba sabata zapitazo, ngati njira imodzi yopewera mliri wa COVID-19.
Analemba chikalata choyimitsa mapemphero mmatchalitchi onse Mkulu wofalitsa nkhani mu dayosizi ya Dedza, bambo Josephy Billiati ati chikalatachi chinapempha akhristuwa kuti asamakumane ku tchalitchi koma mmalo mwake azipemphera mnyumba zawo ndi cholinga chofuna kupewa kutenga kapena kufalitsa kachilomboka kudzera mu kukumana mmatchalitchi.
Iwo atinso akhristuwa akuyenera kukhala omvera atsogoleri awo kuphatikiza pa ndondomeko zomwe dayosizi yawo yakonza.
Zoonadi ma episkopi athu anatilembera kalata kuti tisamakumane kuti tipewe kufalitsa matenda a COVID-19 koma akhristu ena sakutsatira zimenezi. Koma ndi koyenera kuti tiphunzire kutsatira zomwe akuluakulu athu akutilamula, anatero bambo Biliati.
Iwo pempha akhritsu kuti atsatire zomwe ma episkopiwa anapempha ndipo asadikire kuti mbindikiro uchite kuyamba.
| 6 |
Womukaikira zopakula ku Kapitolo adzipereka Adakali ku South Africa: Mphwiyo Wabizinesi Osward Lutepo, amene wakhala akusakidwa ndi apolisi a dziko lino, komanso polisi ya maiko osiyanasiyana ya Interpol, Lachitatu adatera mdziko muno kuchokera kunja ndipo adakadzipereka kulikulu la polisi ku Area 30 mumzinda wa Lilongwe.
Lutepo, yemwenso ndi mmodzi mwa akuluakulu a chipani cholamula cha Peoples Party (PP), akumuganizira kuti amagwirizana ndi ogwira ntchito mboma ena kuti azipakula ndalama zaboma kupyolera mmakampani ake amene amalandira mamiliyoni ochuluka koma osagwira ntchito iliyonse.
Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Padakalipano, anthu oposa 20 akhala akukaonekera kukhoti pokhudzidwa ndi kusowa kwa mabiliyoni a boma. Ena mwa iwo amagwidwa ndi mamiliyoni osaneneka kumabuti a galimoto ngakhalenso mnyumba zawo, ndalama zimene akuganiza kuti zimasololedwa kunjira yolipirira pantchito ndi katundu yemwe boma limagula ya Integrated Financial Management System (Ifmis).
Chongofika mdziko muno, Lutepo adapita kupolisi motsagana ndi womuimira pamlanduwo, Jai Banda.
Wachiwiri kwa mneneri wa likulu lapolisi Kelvin Maigwa adati Lutepo, yemwe ndi wa zaka 35, adakadzipereka yekha.
Tili naye ndipo tikumufunsa mafunso angapo. Padakalipano, milandu imene timuzenge sinadziwike, adatero Maigwa.
Bungwe lothana ndi ziphuphu la Anti-Corruption Bureau (ACB) lidatseka mabuku akubanki a makampani 20 amene akuwakaikira kuti akukhudzidwa ndi chipwirikiti chopakula mabiliyoni a boma. Makampani 8 adali a Lutepo, kapena amene amayendetsa mogwirizana ndi anthu ena.
Izi zili choncho, Pika Manondo, mkulu wina amenenso akusakidwa ndi apolisi pomuganizira kuti akukhudzidwa ndi mlandu wofuna kupha mkulu woonetsetsa kuti ndondomeko ya chuma cha boma ikuyendetsedwa bwino, Paul Mphwiyo, adauza nyuzipepa ya The Nation kuti abwera mdziko muno pofika mawa.
Iye adati ndi wokonzeka kuthandiza apolisi pazofufuza zawo zokhudza kuomberedwakwa Mphwiyo pa September 13, 2013 pomwe amati azilowa pachipata cha nyumba yake ku Area 23. Nthawiyo nkuti Mphwiyo atagwira ntchitoyo kwa miyezi iwiri.
Apolisi adanjata MacDonald Kumwembe yemwe adakhalapo msirikali, komanso Robert Kalua powaganizira kuti ndiwo adaombera Mphwiyo. Apolisiwo adagwiranso Dauka Manondo, mngono wake wa Pika.
Kupakula kwa ndalama kwakhudza kwambiri boma la mtsogoleri wa dziko lino Joyce Banda, yemwe sabata zapitazo adachotsa nduna zake zina, kuphatikizapo yemwe adali nduna ya zachuma Ken Lipenga ndi yemwe adali nduna ya za malamulo Ralph Kasambara.
Ndipo apolisi sabata yatha adakachita chipikisheni kunyumba kwa Kasambara, kuyangana galimoto imene akuti idagwiritsidwa ntchito pokaombera Mphwiyo, yemwe akadali ku South Africa ngakhale adatuluka kuchipatala kumene amalandira thandizo.
| 7 |
Chipatala cha Vatican Chasiyanitsa Ana Omwe Anabadwa Ophatana Chipatala cha likulu la mpingo wa katolika pa dziko lonse chachita opareshoni atsikana awiri omwe anabadwa mophatikana.
Malinga ndi malipoti a Vatican Radio, chipatala cha ana cha Bambino Gesu mu mzinda wa Rome mdziko la Italy, chakwanitsa kupanga opareshoni atsikana awiri omwe anabadwa mophatikana ndipo pano atsikanawa ali bwino.
Mayi ndi ana ake pambuyo powalekanitsa Atsikanawa anali ku chipatala china mdziko la Central African Republic chomwe Papa Francisco adachiyendera mchaka cha 2015.
Ervina ndi Prefina ndi atsikana omwe adabadwa zaka ziwiri zapitazo ndipo iwo adabadwa ophatikana matupi.
Kwa chaka chathunthu madokotala akhala akuwapima atsikanawa maka kuti apeze njira ya bwino yoti nkuwathandizira kuti choncho aliyense athe kukhala payekha osadalira ziwalo za thupi la mzake.
Poyamba anawo amawoneka chonchi Malipoti ati mkulu woyendetsa chipatala cha ana cha Bambino Gesu cha likulu la Mpingo wa Katolika pa dziko lonse, Vatican, chomwe chili ku Rome mdziko la Italy Mariella Enoc anali ku Bangui mdziko la Central African Republic komwe kulinso chipatala cha ana chomwe chimalandira thandizo kuchokera ku Vatican ndipo Papa Francisco adayendera chipatalachi pomwe anakacheza mdzikolo mchaka cha 2015.
Atawaona anawa Enoc anaganiza zowatumiza anawa moperekezedwa ndi mayi a anawa ku Rome.
Masiku apitawa madokotala anawapanga opareshoni yowasiyanitsa matupi yomwe malipoti akuti inayenda bwino.
Ndipo naye mayi wa anawa wati anawa ali bwino moti akusewera ndi kuchita zonse zomwe ana amachita ndipo akuti nao anawa akufuna adzakhale madokotala kuti adzathandize anthu ena.
Mmawu ake mayi wa anayu wati akuthokoza anthu osiyana-siyana omwe agwira ntchito yotamandikayi ndipo mwa njira ya padera Papa Francisco chifukwa cha chithandizo chomwe akupereka kwa ana osiyana-siyana.
Opareshoni ya anawa akuti inali ya maola 18 ndipo madokotala ndi anamwino opitirira 30 ndi omwe anagwira ntchitoyi.
Ervina ndi Prefina anabadwa pa 29 June mchaka cha 2018 pa tsiku lomwe Mpingo wa Katolika pa dziko lonse umachita chaka cha Petulo ndi Paulo Oyera.
| 6 |
Mtsutso pa za makanda odabwitsa Mtsutso wakula ngati nkoyenera kuti ana obadwa modabwitsa azituluka mchikuta.
Izi zadza mwana wina wankhope yodabwitsa atabadwa kuchipatala cha Salima sabata yatha. Mwanayo adamwalira Loweruka pachipatala cha Lilongwe. Izi zidachitika patangotha sabata zochepa kuchokera pomwe mwana winanso yemwe adabadwa wopanda maso, mphuno ndi makutu adabwadwa ku Nkhotakota. Uyonso adatisiya.
Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Pomwe ena akuti ndi bwino kutsatira zomwe zinkachitika kale, kuti ana otere samatuluka mchikuta, ena akuti kutero nkulakwa chifukwa ndi kuwaphera ufulu wokhala moyo anawo.
Mayi wina wa ku Chilomoni, mumzinda wa Blantyre, Martha Banda, akuti ngakhale akudziwa kuti kupha nkulakwa, si bwino kulola anawo atuluke mchikuta chifukwa adzazunzika.
Mzamba wina wodziwa zitsamba ku Mchinji, Ethel Kwitanda, wati kale anaotere sankatuluka mchikuta koma pankachitika nkhanza moti mpaka mwina moyo wa munthu umatha kupita.
Mwana akabadwa ndi ziwalo zodabwitsa akuluakulu ankatha kumupitiriritsa dala mchikuta momwemo moti nthawi zina mayi wake sankazindikira. Ena ankakhulupirira kuti mwanayo amabweretsa mavuto. Amatha kumupitiriritsa dala nkukanena kuti wabwera wakufa kale, akutero Kwitanda.
Koma Dr Adamson Muula, mmodzi mwa adotolo a nthenda zofala, wati si bwino kuchotsa moyo wa mwana pongotengera momwe akuonekera, polingalira kuti moyo ndi chimodzimodzi, osalingalira za momwe khanda likuonekera.
Funso loti tidzifunse ndi loti kodi kuoneka mosiyana ndi ena kungapangitse khanda kuti lisakhale munthu? Khanda lobadwa mwa mayi ndi bambo ndi munthu basi. Kodi tikapha ana obadwa mosiyana ndi ena, kenako tidzapha ndani? akudabwa Muula.
Mmodzi mwa akadaulo oona za momwe anthu amaganizira Symon Chiziwa akuti nkhani ya ana obadwa modabwitsa yakhala ikuzunguza anthu ambiri padziko lapansi.
Ana otere akabadwa kumakhala manongonongo. Nthawi zambiri azamba amangowasiya anawo kuti afe. Makolo amangouzidwa kuti anawo apitirira, akutero Chiziwa.
Iye wati ena amakhulupirira kuti makolo akhoza kuvutika kwambiri kusamalira ana otere, komanso kuti akhoza kuwabweretsera matsoka.
Kalekale ku Greece ana otere akabadwa amatsamwitsidwa kapena kumizidwa. Mwana akabadwa, makolo amayenera kupititsa anawo kwa akuluakulu ndipo akaona kuti kalibe ndi moyo wamphamvu, amakasiya poyera chifukwa amati sikadzakhala nzika yodalirika, iye akutero.
Koma izi zili choncho, Chiziwa akuti anthu amadziwa kuti moyo ndi chinthu chamtengo wapatali choncho kukonza makanda chifukwa cha ichi nkulakwa.
Makolo amakhulupirira kuti akabereka, alera ana kuti adzaime paokha. Ana otere zikhoza kukhala zovuta kuti adzaime paokha. Choncho nkhaniyi ndi yofunika kufunsa makolowo maganizo awo, akutero Chiziwa.
Malamulo a dziko lino amapereka ufulu wokhala ndi moyo kwa munthualiyense.
Gawo lachinayi la malamulo oyendetsera dziko lino limati: Munthu aliyense ali ndi ufulu wokhala ndi moyo ndipo palibe munthu yemwe ali ndi mphamvu zochotsa moyo wa mnzake pokhapokha imfayo yagamulidwa ndi khothi lodziwika bwino litamupeza munthu woti aphedweyo ndi mlandu wofunika kulandira chilango chotero potsatira zomwe malamulowo akunena.
Mkulu wa Bungwe la anamwino ndi azamba mdziko muno Harriet Kapyepye wati mchitidwewu unali wozunza mizimu ya anthu osalakwa pogwiritsa ntchito mfundo zopanda pake.
Iye adati aliyense ali ndi ufulu wokhala ndi moyo ngakhale atabadwa ndi vuto lalikulu chotani.
Kapyepye wati anamwino ndi azamba amdziko muno amaphunzitsidwa mmene nkhanza zoterezi zingapeweredwe komanso amaphunzitsidwa mmene angalangizire amayi omwe amapempha okha kuti mwana yemwe wabadwa ndi chilema amuphe komanso kuti amulandire mbanjamo.
Ife pantchito yathu timaonetsetsa kuti mwana aliyense yemwe wabadwa akhale ndi moyo komanso asanyozeke chifukwa cha chilema. Tili ndi mabungwe osiyanasiyana omwe timatha kutumizako ana amavuto ena ndipo amatha kukonza mavuto ngati amenewo, akutero Kapyepye.
| 19 |
A Malawi akufuna 2018 wa ngwiro Pomwe chaka cha 2018 changoyamba kumene, mtsogoleri wa zipani zotsutsa boma Lazarus Chakwera ndi akadaulo ena ati boma lisinthe kayendetsedwe ka zinthu kuti chakachi chikhale chokomera Amalawi.
Chakwera yemwe ndi mtsogoleri wa chipani cha Malawi Congress Party (MCP), kadaulo pa zamaphunziro Benedicto Kondowe, kadaulo pa zachuma Dalitso Kubalasa, kadaulo pa zaumoyo George Jobe ndi mtsogoleri wa bungwe la alimi la Farmers Union of Malawi (FUM) Alfred Kapichira Banda aunikira momwe zinthu zikuyenera kuyendera.
Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Chakwera: Amalawi amayembekeza zambiri Akuluakuluwa akhala akudzudzula za momwe boma limayendetsera zinthu zina mchaka chomwe changothachi ndipo poomba mkota wa madandaulo, Chakwera adati boma lidalephera kukwaniritsa malonjezo ake.
Padali zinthu zambiri zomwe Amalawi amayembekezera potsatira malonjezo omwe boma lidalonjeza koma momwe chaka cha 2017 chimapita kumapeto, padalibe chomwe chidaonekapo, adatero Chakwera.
Iye adati mwa zina, boma lidalonjeza kusintha nkhani ya kuthimathima kwa magetsi zomwe sizidatheke mpaka pano, kutukula alimi koma mmalo mwake ndiwo adamva kuwawa kwambiri mchakachi, kuthana ndi katangale zomwe sizidatheke komanso kulemekeza malamulo.
Akuluakuluwa amalankhula ndi Tamvani potsatira mawu a pulezidenti Peter Mutharika polandira chaka chatsopano pomwe adati Amalawi ayembekezere chaka chopambana cha zitukuko.
Mu 2018, titsegulira ntchito yaikulu ya mthirira yomwe idzapindulire mabanja pafupifupi 40, 000, tipitiriza kutsegula mwayi wa ntchito kwa achinyamata, ntchito za mtukula pakhomo ndi ngongole za achinyamata ndi amayi, adatero Mutharika.
Kudali kugona kuchigayo kudikira magetsi ayake Iye adatinso boma lipitiliza kutukula ntchito za chuma powonetsetsa kuti chiwongola dzanja chomwe anthu amapeleka akakongola ndalama ku mabanki chatsika kuti anthu ambiri azitha kutenga ngongole.
Ndikufuna mchaka chimenechi, mlimi, mphunzitsi, namwino, msilikali ndi apolisi azitha kulowa mbanki nkutulakamo atatenga ngongole kuti adzipezere malo ndikumanga nyumba zawo, Mutharika adatero.
Iye adati boma lake lili ndi ndondomeko zomwezidzathandize kuti vuto la magetsi lisadzawonekenso mdziko muno likangotha.
Powonjezerapo pa malonjezowa, nduna ya zamalimidwe, mthilira ndi chitukuko cha madzi Joseph Mwanamvekha adati mchaka cha 2018 boma lipezera alimi misika yabwino ya zokolola kuti apukute misozi yawo.
Chaka chatha sitikadachitira mwina koma kutseka zipata kuti mbeu zisatuluke mpaka tigule chakudya chokwanira koma poti chaka chino chakudya chiliko kale chokwanira, alimi ayembekezere misika yabwino, adatero Mwanamvekha Koma chakwera adati, Bola izi zisakhale zongofuna kupeleka chiyembekezo kwa Amalawi kuti aziti boma litithandiza. Nthawi yopanga ndale zonamiza anthu idatha, pano ndi nthawi yolankhula ndi ntchito.
Pounikira za momwe chuma chikuyenera kuyendera, Dalitso Kubalasa yemwe ndi kadaulo pa za chuma adati boma likuyenera kumanga mabawuti kuti nthambi zonse za boma zizitsatira malamulo oyendetsera chuma cha boma.
Iye adati mu 2017, nthambi zina za boma zidapezeka ndi mirandu yosapeleka malipoti a kayendetsedwe ka chuma cha boma zomwe ziapangitsa kuti papezeke mavuto ambiri pa kauniuni wa chuma ha bomachi.
Tidaona mmene malipoti adalili mchakachi okhudza kauniuni wa chuma cha boma pomwe ndalama za nkhaninkhani sizidaoneke momwe zidagwirira ntchito. Pamenepa pakuyenera kusinthidwa mchakachi, adatero Kubalasa.
Iye adati ngati izi sizitheka, ndiye kuti Amalawi ayembekezere chaka china chowawa ku mbali ya za chuma ndipo mabala ake adzavuta kupola kaamba koti chaka chotsatiracho ndi chachisankho.
Benedicto Kondowe yemwe ndi mkulu wa mgwirizano wa bungwe oyanganira za maphunziro adati boma lisakakamire kutsegula sukulu zokha ndi kusintha maphunziro koma kuti liyike mtima kwambiri pa maphunzirowo apamwamba.
Iye adati maphunziro otukula aphunzitsi apite patsogolo, sukulu zikhale ndi aphunzitsi okwanira, zipangizo zophunzilira ndi ndi kuphunzitsizira zizipezeka mokwanira ndipo oyendera sukulu akhale odzipeleka.
Ndibwino kuti sukulu zikutsegulidwa koma tikuyenera kuwonetsetsa kuti zipangizo zilimo, aphunzitsi ndiwokwanira komanso ophunzitsidwa bwino ndipo pakhale timu ya akadaulo oyendera kuwona kuti maphunzirowo akuyenda bwinodi, adatero Kondowe.
Kadaulo wa zaumoyo George Jobe wati potukula ntchito za umoyo, boma liyambe kukwaniritsa mlingo wa mgwirizano wa mayiko oyika K15 pa K100 mu bajeti yake yopita ku unduna wa zaumoyo.
Iye wati mpofunikanso kukhwimitsa malamulo olangira anthu opezeka akuzembetsa mankhwala ndi zipangizo za chipatala kuti zipangizo zoterezi zizikhalamo mzipatala nthawi zonse.
Nkhani yayikulu apa ndi kukhulupilika ndi kukhala ndi ndondomeko zokhwima bwino zotetezera zipangizo za chipatala. Pamenepa pakukhudzidwanso ndi kukhala ndi ogwira ntchito za chipatala okwaira, adatero Jobe.
Pulezidenti wa alimi Alfred Kapichira Banda adati alimi sakufuna zambiri koma kudzipeleka ku mbali ya boma pa nkhani yotukula alimi makamaka pa nkhani yolimbana nsi mbozi zomwezikuvuta komansomisika.
| 11 |
Akhristu Apewe Kuyika Mtima pa za Mdziko-Papa Mtsogoleri wa Mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisko wati akhristu aleke kuyika mtima kwambiri pa zinthu za mdziko la pansi.
Papa Francisko walankhula izi lachiwiri pa nsembe ya misa yomwe anatsogolera ku likulu la mpingowu ku Vatican. Iye wati kuika mtima kwambiri pa zinthu za dziko lapansi kumachititsa anthu kukhala mu mdima wosasiyanitsa pakati pa chinthu chabwino ndi choipa.
Papa Francisko Pamenepa Papa Francisko wapempha anthu kuti akhazikike nthawi zonse pa zinthu zomwe ndi zokweza ufumu wa Mulungu.
Polankhula mtchalichi cha lalingono la Santa Marta ku Vatican, Papa Francisko wati mavuto ambiri monga katangale ndi ziphuphu akhazikika pakati pa anthu chifukwa choika mtima kwambiri pa zinthu za dziko lapansi mmalo motsogoza Mulungu.
Papa Francisko wati anthu akuyenera kumadzifunsa nthawi zonse ngati chomwe akufuna kuchita chikuchokera kwa Mulungu kapena mzimu woipa.
Pamenepa iye wati munthu aliyense akuyenera kumasinkhasinkha nthawi zonse zomwe zikuchitika pa moyo wake kuti adziwe ngati akuchita zosangalatsa Mulungu kapena ayi.
Pomaliza iye wati nkofunika kumapemphera kwambiri pofuna kuima njiiii pa za Mulungu.
| 13 |
Msika wa osewera watentha Pamene matimu ali kopumira kukonzekera ndime yachiwiri ya 2015 TNM Super League, msika wa osewera wafika potentha pamene matimu ali kalikiriki kugula ndi kugulitsa osewera ncholinga chofuna kuchita bwino mligiyi ikayamba mndime yachiwiri.
Tiyamba ndi timu yomwe ikuteteza ligiyi yomwenso ikutsogola ndi mapointi 32. Iyi ndi Big Bullets, yomwe padakalipano ikukambirana ndi timu ya Mzuni FC kuti itenge mnyamata womwetsa zigoli wa ku Burundi, Aimable Niyikiza, amene tikukamba pano ali kukampu ya Bullets.
Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Timuyi ikufunanso itenge mnyamata wosewera pakati kutimu ya Azam, Yamikani Chester, koma timu yakeyi ikukaniza kuti wosewerayu sali pamalonda.
Bullets yatenganso Chisomo Mpachika wosewera kumbuyo mtimu ya Dedza Young Soccer ngakhale timu yake ikukaniza kumugulitsa ponena kuti ngati Bullets ikumufuna ndiye iwapatse Sankhani Mkandawire ndi Yamikani Fodya.
Tipite ku Silver Strikers yomwe yakanika kutenga goloboyi wa Mighty Be Forward Wanderers Richard Chipuwa ndipo mmalo mwake yatenga Bester Phiri, yemwenso amagwirira pagolo ku Wanderers.
Padakalipano Wanderers yatchaja Silver kuti ipereke K2 miliyoni pokana kuti Silver itenge wosewerayu pangongole.
Silver yatenga kale John Banda yemwe adali pangongole ku Young Soccer kuchokera ku Evirom pamtengo wa K500 000. Timuyi ikufunanso kutenga mnyamata wosewera kumanzere chakumbuyo kwa Epac, Dalitso Mwase, pamtengo wa K2 miliyoni.
Nayo Wanderers ikufuna kutenga Boston Kabango kuchokera ku Epac pamtengo wa K3 miliyoni. Koma Silver ndi Fisd Wizards nawonso maso awo ali pa mnyamata yemweyu.
Wanderers ndi Bullets akulimbirananso Chester, yemwe Azam ikukanitsitsa kugulitsa. Wanderers yaonetsanso chidwi kufuna kutenga Kelvin Hara, Dave Mwalughali, George Hawadi ndi Hastings Banda komanso George Kasambara kuchokera kutimu ya Chilumba Barracks ngakhale timuyi ikukana kuti sakuwagulitsa osewera awo.
Timuyi ikufunanso itenge John Lanjesi wa Civo pamtengo wa K4.5 miliyoni.
Azam Tigers yatenga kale Abraham Kamwendo kuchokera ku Blantyre United ndipo yatoleranso osewera ena achisodzera pamene Moyale yatenga Komani Msiska yemwe akutsogola ndi zigoli ku Chilumba.
Red Lions yagula wosewera wapakati wa Zomba United Stanley Dube.
Mphunzitsi wa timuyi Collins Nkuna akuti wakhala akuyendayenda mmidzimu ndipo wapeza osewera ambiri mboma la Salima.
Civo United sikumveka kuti ikusaka osewera mitunda iti koma timuyi yaitanitsa Josophat Kwalira kuchokera ku Dedza Young Soccer.
Wizards yatola Godfrey Masonda. Fisd ikufunanso kugula Precious Msosa kuchokera ku Wanderers.
Msikawu utsekedwa pa 18 September usiku ligiyi isanayambirenso pa 19 September.
| 16 |
YODEP Ipereka Mbuzi kwa Ana Olumala Wolemba: Thokozani Chapola Bungwe la Youth and Development Productivity (YODEP) lapereka thandizo la chimanga komanso mbuzi kwa ana omwe ali ndi ma ulumali osiyanasiyana mboma la Zomba.
Mkulu woona za mapulogalamu ku bungweli a Joy Mwandama, ati bungwe lawo lachita izi ngati njira imodzi yofuna kuwalimbikitsa anawa kupeza chakudya pomwe akumapita ku sukulu.
Pamenepa a Mwandama alangiza makolo a anawa, kuti asamachite manyazi pomwe akufuna kutumiza anawa ku sukulu, ponena kuti aliyese ali ndi ufulu wolandira maphunziro mdziko muno.
Makolo ena amachita manyazi ndi ana awo chifukwa ndi olumala koma sizimayenera kukhala choncho ayi mwana aliyense atumizidwe ku sukulu posatengera kuti ndi olumala kapena wa lungalunga, anatero a Mwandama.
Mwa zina bungweli laperekanso ndalama zokwana 3 hundred sauzande kwacha kwa anawa.
Mai Nduuzayani Wasili a mmudzi mwa Makambanjira ndi mmodzi mwa makolo a anawa ndipo ayamikira bungweli kaamba ka thandizoli.
Zomwe achita a bungwezi ndi zosangalatsa chifukwa zipangitsa kuti miyoyo ya anawa pamodzi ndi ife ipite patsogolo, anatero mayi Wasili.
| 14 |
Shuga apezeka posachedwaIllovo Mkulu wa kampani yopanga shuga ya Illovo Malawi Mark Bainbridge wati kampaniyo iyesetsa kuti shuga azipezeka chaka chonse osati kumasowa momwe zakhalira sabata zingapo zapitazi.
Bainbridge adanena izi Lachitatu pomwe nduna ya zokopa alendo ndi malonda Joseph Mwanamvekha adayendera kampaniyo kuti akamvetsetse za gwero la kusowa kwa shugayo. Kusowa kwa shuga kudachititsa kuti ogulitsa akweze kuchoka pa K750 kufika pakati pa K950 ndi K1 200.
Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Ogwira ntchito ku Illovo pakalikiliki kupanga shuga Malinga ndi Bainbridge, chaka chino kampaniyo inagulitsa shuga olemera matani 244 000, pomwe dziko lino limalira matani 160 000 ndipo anadabwa kuti shugayo akusowa bwanji.
Tinali ndi shuga wokwanira chaka chino ngakhale mvula siyinagwe bwino nthawi yomwe timabzala nzimbe. Ogulitsa ena amagula shuga wochuluka nkumusunga zomwe zimadzetsa mavuto ngati awa, adatero iye.
Iye adati padakalipano, kampaniyo ikuyesetsa kuti iwonjezere shuga amene imapanga kuti azikwanira chaka chonse.
Mwanamvekha adati ndi wokondwa chifukwa kampaniyo yalonjeza kuti izipanga matani 650 a shuga patsiku, pomwe dziko lino limalira matani 411 patsiku.
Tazindikira kuti pali shuga wochepa pamsika, zimene zachititsa kuti mtengo ukwere. Kwa amene akukweza shuga mopweteka Amalawi, malamulo agwirapo ntchito. Tili ndi chiyembekezo kuti Illovo ikwaniritsa lonjezo lake kuti shuga ayambe kupezeka, adatero Mwanamvekha.
Pomwe Amalawi akudikira shugayo kuti ayambe kupezeka, Amalawi amene tidacheza nawo anadandaula ndi kusowa kwa shugako, ponena kuti izi zikuchititsa moyo kuthina.
Mmodzi mwa Amalawiwo, Joana Chimphamba wa kwa Senti ku Lilongwe, adati abizinesi ena kumeneko akumaphwatula paketi ya kilogalamu imodzi ndi kuigawa pawiri. Gawo lililonse akuligulitsa K600 kapena K650.
Izi zikutanthauza kuti yomwe timagula K780 pa paketi tikugula K1 200 kapena K1 250. Nanga akapitirira kusowa shugayu, zitithera bwanji? adadabwa iye.
Chimvano Moyo wa ku Area 25 wati poyamba sadakhulupilire atatuma mwana kukagula shuga Lamulungu lapitali ndipo pobwera adamuuza kuti adagula pa mtengo wa K970 chikhalirecho, amagula pamtengo wa K780.
Iye wati atapita kukatsimikiza kumsika, adapeza kuti magolosale ambiri alibe shuga ndipo pomwe adamupezapo adamutsimikizira kuti shuga akusowa ndipo akapezeka akukhala okwera mtengo.
Mmodzi mwa anyamata ogwira ntchito mushopu yaikulu ya Spar mumzinda wa Lilongwe adati patenga nthawi shopuyi isanalandire shuga kuchokera ku Illovo.
Iye adati anthu ambiri akhala akubwerera mushopuyi akafuna shugayo ngakhale kuti eni ake adapereka kale oda ya katunduyu koma sadanene kuti shugayo samabwera chifukwa chiyani.
Ndipo mumzinda wa Blantyre, anthu ochuluka amakhamukira kusitolo zosiyanasiyana monga Shoprite kumene kumakhala miyandamiyanda ya anthu pamzere kufuna kugula shuga akapezeka.
Davie Chilikumwendo wa ku Namiyango mu mzinda wa Blantyre adati wasiya kumwa tiyi chifukwa ndalama ya shuga siyikukwanira.
Shuga yemwe akupezeka akugulitsidwa pamtengo wokwera. Padakalipano tizigwiritsa mchere mphala ndipo tiyi adzamwedwa shuga akayamba kugulitsidwa pa mtengo woyenera, adatero Chilikumwendo.
Nawo ochita malonda mumzindawu ati kusowa kwa shuga kukusokoneza bizinezi chifukwa amadalira yemweyi popanga phindu lochuluka. Mmodzi mwa iwo, Clement Chafoteza wa ku Chilobwe, adati shuga wochepa yemwe akupezeka akugulidwa modula ndipo anthu wamba akukanika kuagula.
| 2 |
Dayosizi ya Mangochi Yapereka Ndondomeko Zatsopano Zopewera COVID-19 Mpingo wa katolika mu dayosizi ya Mangochi walangiza akhristu ake ndi njira zatsopano zomwe akuyenera kutsatira pochita mapemphero, potsatira kupitilira kufala kwa mliri wa Coronavirus mdziko muno.
Walemba kalatayo-Bishop Stima Kalata yomwe yalembedwa ndipo yasayinidwa ndi episkopi wa dayosiziyi ambuye Montfort Stima, yapempha akhritsu kutsatira njira zina zowonjezera pamene akupitilira kutsatira njira zomwe mpingo komanso boma linakhazikitsa kale. Zina mwa njira zatsopanozi ndi monga kuvala chotchingira kukamwa ndi mphuno pamene akuchita mwambo wa nsembe za misa.
Zina ndi monganso kukhala malo odutsa mpweya pamene akuchita mwambo wa mapemphero komanso kupewa kugwiritsa ntchito ma fan; kugwiritsa ntchito sopo komanso kulolini pamene akukonza mmalo opempherera, kukhala motarikirana ma mita awiri komanso kusamba mmanja ndi sopo.
Ambuye stima kudzera mu kalatayi yomwe alembera ansembe, asiteri komanso akhristu eni ake, ati miyambo ya nsembe ya misa idzichitika kosapitirira ola limodzi ndipo akhristu apewe kupereka mphatso pamanja, kulandilira ukalistiya mmanja komanso ati pakuyenera kukhala ndondomeko yabwino komanso yokhazikika pamene akhritsu akutuluka mu tchalitchi kuti apewe kugundana-gundana.
Pomaliza kalatayi yaimitsa ena mwa masakramenti monga sakrameneti la ubatizo, zinamwali za mpingo komanso maphunziro akatikisimu wa ana.
Ngakhale izi zili chomwechi, episkopiyu wapereka chilorezo kwa masakramenti ena koma motsatira ndondomeko zopewera mliriwu. Ma sacramentiwa ndi monga la kulapa, kudzodza komanso ukwati pomwe akuti opereka komanso olandira ma sacramentiwa onse adzivala chotchingira kukamwa ndi mphuno komanso azitsatira ndondomeko zonse zomwe mpingo komanso boma lakhazikitsa. Pomaliza ambuye stima apempha akhristu kuti akonde kutsatira njira zozitetezerazi kulikonse ngakhale kumalo oti si kutchalitchi.
| 6 |
Maepiskopi ati ndi Okonzeka Kuthandiza Anthu Odwala Matenda a COVID-19 Maepiskopi a mpingo wa katolika mmaiko a Malawi, Zambia komanso Zimbabwe ati ali limodzi ndi anthu onse omwe akukhudzidwa ndi mliri wa CoronaVirus omwe wavuta kwambiri padziko lonse kuphatikizapo mmaiko atatuwa.
Mu uthenga wawo wa Pasaka wopita kwa atumiki onse, akhritsu komanso anthu akufuna kwabwino, ma episkopiwa ati mliriwu, wasokoneza kwambiri chikondwelero cha Pasaka cha chaka chino, choncho pofuna kuonetsa umodzi wawo ndi akhristu onse komanso anthu omwe pakadali pano akudwala nthendayi,iwo akuwayikiza mmapemphero anthuwa kuti Mulungu awachiritse.
Mu kalata yomwe yalembedwayi ati, ena mwa anthu, akukhala mwa mantha kamba ka mliriwu, komanso kuti achibale awo ena, akusungidwa ku malo awokha, zomwe zikukulitsa kutaya mtima pakati pawo, choncho iwo ati uthenga wa Pasakawu, uwalimbikitse za chikondi cha Mulungu.
Onse omwe akudwala matendawa ndi omwe akuthandiza odwalawa akuyenera kudalira Mulungu, komanso polimbana ndi matendawa akhristu akuyenera kutsatira zomwe Papa Francisco anapempha kuti kusonkhedwe limodzi limodzi kuti tithadizire onse omwe akhuzidwa, yatero kalatayo.
Iwo apemphaso akhritsu kuti akhale olimba mtima monga momwe akazi awiri aja analili pokawona manda a Ambuye Yesu, zomwe zikusonyeza kuti zonse zatha ndipo nayo imfa yagonja.
| 6 |
Anthu a Ulumali Sanachite Bwino pa Chisankho-MUB Bungwe lomenyera maufulu a wanthu osaona mdziko muno la Malawi Union of the Blind (MUB) lati anthu ambiri osaona omwe anapikitsana nawo pa chisankho chapitachi sanachite bwino kamba koti anthu ambiri mdziko muno adakalibe maganizo oti anthu osaona sangathe kuwathandiza pa ntchito zotukula dziko lino.
Mkulu wa wabungwe-li mdziko muno a Ezekiel Kumwenda amayankhula izi kwa mtolankhani wathu amene amafuna kudziwa nambala ya anthu osaona omwe anapambana pa mipando yosiyanasiyana yomwe amapikitsana nawo pa chisankhochi.
Kumwenda: Anthu ambiri sanawakhulupilire anthu osawona A Kumwenda ati ndi zomvetsa chisoni kuti mwa anthu asanu ndi mmodzi (6) omwe amapikisana nawo pachisankhochi mmodzi yekha ndi amene wapambana pa mpando wa ukhansala mdera lina mboma la Machinga.
Anthu ambiri sanawakhulupilire anthu osaona kuti angawatsogolere pa mipando yosiyanasiyana, anatero a Kumwenda.
Iwo anaonjezera kuti vuto la kusowa kwa ndalama zochititsira misonkhano yokopa anthu ndi lomwe lawonjezeranso kuti anthu wa asachite bwino pa zisankhozi.
A Kumwenda ati ali ndi chiyembekezo kuti chiwerengero cha anthu osaona omwe adzapikisane nawo pa chisankhochi mchaka cha 2024 chidzakhala chokwera kamba koti chimenechi chinali chiyambi chabe.
| 11 |
Makhoti ayambanso kugwira ntchito Sitalaka yomwe ogwira ntchito mmakhoti amachita yatha Lachinayi.
Mtsogoleri wa ogwira ntchitowa, Charles Lizigeni, adatsimikizira Tamvani kuti makhoti onse a mdziko muno ayambanso kugwira ntchito.
Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Tagwirizana zobwerera kuntchito kaamba koti Amalawi amavutika kuti apeze chilungamo chifukwa cha sitalakayi, adatero Lizigeni.
Ogwira ntchito mmakhoti atenga masabata anayi akunyanyaka ntchito pofuna kukakamiza boma kuti liziwapatsa ndalama zolipirira nyumba ngati momwe likuchitira ndi majaji ndi mamajisitiliti.
Koma nduna ya zachuma, Goodall Gondwe, idali yodabwa kuti majaji ndi mamajisitiliti akulandirira padera ndalama zolipirira nyumba.
Boma lidasintha ndondomeko zolipirira ogwira ntchito ake mu 2014 moti munthu aliyense sakuyenera kulandirira padera ndalama za nyumba.
Malipiro omwe ogwira ntchito ntchito mboma amalandira [clean wage] adaphatikizamo kale malipiro apamwezi a munthu ndi ndalama zolipirira nyumba.
Ngati majaji ndi mamajisitiliti akulandirira padera ndalama za nyumba ndiye kuti boma lidangolakwitsa, idatero ndunayo.
Boma, kudzera mwa mlembi wa zachuma Ben Botolo, lidadzudzula ogwira ntchitowa ndipo lidawauza kuti sitalaka yawo siyovomerezeka ndi malamulo a dziko lino. Boma lidauza anthuwo kuti abwerere ku ntchito.
Botolo adati nzosatheka kuti boma liziwapatsa ndalama za nyumba zoyambira mchaka cha 2012.
Koma Lizigeni adatsutsa zomwe mlembiyu adalankhula. Sitalaka yathu ndi yovomerezeka. Ngakhale tikubwerera kuntchito sizikutanthauza kuti sitalaka yathu idali yosavomerezeka.
Anthuwa adayenera kuyamba ntchito Lachitatu, koma adakana kutero ndipo adapempha kuti apolisi omwe adadzadza mmakhoti achokeko kaye.
Sitalakayi idayamba pa July 31 mmakhoti onse a mdziko lino.
| 11 |
Mayi Akagwira Ukayidi kwa Zaka Zitatu Kamba Kovulaza Ana Owapeza Bwalo la milandu ku Lilongwe lalamula mzika ina ya ku Rwanda Silvia Mukunoheri wa zaka 25 kuti akakhale ku ndende ndi kugwira ntchito ya kalavula gaga kwa zaka zitatu kamba kovulaza ana owapeza.
Miyendo ya ana amene anavulazidwawo Malinga ndi woyimira boma pa milandu Sergeant Abigail Chirwa, pa 3 March chaka chino mayiyu adapezeka akukakamiza ana awiri omwe ndi owapeza kuti akwawe pansi pokhakhala dzuwa likuswa mtengo ati kamba kowononga shuga komanso mpunga.
Atawonekera ku bwalo la milandu, Mukunoheri anawukana mlanduwu zomwe zinachititsa woyimira boma pa mulandu kuti abweretse mboni zinayi zomwe zinachititsa kuti mayiyu apezeka olakwa.
Popereka chigamulo chake Magistrate Sarah Beza anati zomwe anachita mayiyu ndi zosemphana ndi gawo 254 la malamulo a dziko lino ndipo anamulamula kuti akakhale ku ndende ndi kukagwira ntchito ya kalavula gaga kwa zaka zitatu.
| 7 |
Bzalani mbewu zocha msangaLipita Woyendetsa ntchito za ulangizi ndi njira zamakono za ulimi muunduna wa zamalimidwe, Wilfred Lipita, wati alimi akuyenera kutengerapo phunziro pa zomwe zidaoneka muulimi wa chaka chatha ndi kusankha mwanzeru mbewu zolima chaka chino.
Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Polankhula ndi Uchikumbe paulangizi, Lipita adati masiku ano nkovuta kutchera kuti mvula iyamba lero ndipo idzatha mawa mmalo mwake njira yabwino nkusankha mbewu zocha msanga.
Upangiri wa zanyengo ndi umenewo komanso payekha mlimi ayenera kukhala wozindikira kumwamba kukhoza kusintha nthawi iliyonse malingana nkusintha kwa nyengoku, adatero Lipita.
Lipita: Alimi ena apulumukira chinangwa Iye adati kunjaku kuli mbewu zocha msanga zomwe mvula itati yadulira panjira, mlimi akhoza kupeza popumira kusiyana nkukakamira mbewu zokhalitsa mmunda chifukwa izi ndizo zingalowetse njala.
Mkuluyu adatinso pomwe alimi akubzala mbewu zachizolowezi monga chimanga, nyemba, fodya ndi zina ayeneranso kulingalira za mbewu zina zopirira kuchilala monga chinangwa ndi mbatata.
Mu ulangizi wake, Lipita adati alimi ena chaka chino apulumukira chinangwa ndi mbatata kupatula ulimi wa mthirira malingana nkuti ulimi chaka chatha sudayende bwino chifukwa cha mvula yokokolola ndi ngamba.
Mbewu ngati chinangwa zili mgulu la mbewu zomwe timati zachitetezo chifukwa ngakhale mvula idule, izo zimaberekabe. Palibe kanthu kuti mitsitsi yake ndi yaikulu kapena yochepa bwanji koma nkhani ndi yakuti mbewu zina zitakanika, mlimi amakhala ndi pogwira, adatero Lipita.
Mmadera ambiri chimanga chidatuluka ndipo mlangizi wamkuluyu adati imeneyi si nkhani yokhazikika pansi koma kulimbikira ntchito za mmunda monga kupalira kuti mbewu zisamalimbirane chakudya ndi udzu.
Iye adati mbewu zokulira mtchire zimanyozoloka ndipo sizibereka bwino ngakhale mlimi ataononga ndalama zambiri kugulira feteleza.
Omwe chimanga chawo chatuluka, ino ndiye nthawi yoyamba kulingalira kupalira ndipo chikafika mmawondo ndi nthawi yothira feteleza wina ndi kubandira kuti chinyamuke ndi mphamvu, adatero Lipita.
Iye adati chimanga chikanyamuka ndi mphamvu maberekedwe ake amakhala osiririka ndipo mbewu yake ikakhala yabwinonso, phesi limodzi limabereka chiwiri kapena chitatu podzakolola nkudzakhala ngati minda iwiri pomwe udali umodzi.
| 4 |
Anthu Anayi Aperekera Umboni pa Mlandu wa Chamthunya Mboni zinayi za mbali ya boma zaperekera umboni wawo pa mlandu omwe a Misonzi Chanthunya akuganiziridwa kuti anapha bwenzi lawo Linda Gasa mchaka cha 2010.
Mboni zitatu zinachokera ku Monkey bay komwe kuli cottage ya a Chanthunya ndipo mboni imodzi ndiyochokera ku ofesi ya boma yoona zolowa ndi kutuluka mdziko muno ya Immigration.
Malinga ndi lawyer oyimira boma Dr. Steve Kayuni, mbonizi zilipo zisanu ndi imodzi ndipo pali chiyembekezo choti mbonizi zikhala zikupitilira kubwera ku bwaloli kudzapereka umboni wawo.
Mmodzi anali ogwira ntchito kwa oyimbidwa mlandu komanso ena anali ogwira ntchitoku immigration. Mboni zinazo sizinabwere chifukwa amagwira ntchito koma lachinayi masana adzapezeka kuti adzayikire umboni, anatero Dr. Kayuni.
Polankhulapo ku mbali ya ozengedwa mlandu a Micheal Goba Chipeta ati sangayankhulepo zambiri chifukwa mlanduwu udakali mkati.
| 14 |
Kudali kukwaya ku Mtima Woyera Udali ulendo wokhetsa thukuta lowopsa kuti zonse zilongosoke pakati pa Gray Lizimba ndi Iness Chimombo koma zonse zidafika pampondachimera Loweruka lapitali pomwe awiriwa adapatsana malonjezano omaliza.
Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Inde, pamtendere ndi pamavuto, moyo wabwino kapena matenda sadzasiyana. Awa ndiwo adali malonjezo pakati pa Gray ndi Iness omwe amachokera ku Bembeke mboma la Dedza ndipo onse amachita bizinesi mumzinda wa Lilongwe komanso amayimbira limodzi kwaya ku Mtima Woyera Parish ya mpingo wa Katolika mumzinda wa Lilongwe.
Gray akuti ulendo udayamba mchaka cha 2009 awiriwa atakumana kutchalitchi ndipo Gray sadafune kuchedwa koma kufunsira pomwepo koma akuti sizidayende.
Adandiyankha kuti ndisadzayerekeze kumulankhulanso za nkhaniyo, koma sindikadakwanitsa kutero. Mtima wanga udali pa iye ndipo ndidapitiriza kutchetcherera mpaka mu April, 2012 mpomwe adandilola, adatero Gray.
Gray ndi Iness kupsopsonana patsikulo Iye adati atangomva mawu oti ndavomera adamva ngati wanyamula dziko lonse mmanja mwake, mtima ukudumphadumpha uku mmasaya muli chimwemwe chokhachokha.
Iye akuti adakhala pachibwenzi mpaka mchaka cha 2014 mwezi wa November pomwe awiriwa adapanga malonjezano oyamba pachinkhonswe ndipo adagwirizana kukhala zaka zina ziwiri asadapange ukwati kuti akonzekere mokwanira.
Kuchoka apo tinkakonzekera ukwati wathu ndipo tonse tidaikapo mtima mpakana zonse zidatheka pa 4 June, 2016. Tidakadalitsira ku Mtima Woyera ndipo madyerero adali kubwalo la St Peters Anglican ku Lilongwe, adatero Gray.
Iye akuti Iness ndi chimwemwe komanso ufulu wake chifukwa amamulimbikitsa mzinthu zambiri ndi kumuthandiza mmaganizo pomwe mutu waima.
Iness sadafune kunena zambiri koma kungotsimikiza kuti iye ali ndi chimwemswe kuti mtunda womwe adauyamba zaka 7 zapitazo wafika pampondachimera.
| 13 |
Ghana Igulira Apolisi Mifuti Wolemba: Thokozani Chapola /08/ghana-police.jpg" alt="" width="550" height="366" />Alandira mifuti ndi ma bullet proof-Ghana Police Boma la dziko la Ghana lati lipereka mifuti kwa apolisi onse ogwira ntchito za pansewu (Traffic) kutsatira ziwembu zomwe apolisiwo akuchitidwa.
Malipoti a wailesi ya BBC ati apolisi asanu anaphedwa mwezi watha komanso ena awiri aphedwa lachitatu lapitali pamene zifwamba zina zinawombera apolisiwa pamene zimakana kuyimitsa galimoto yawo, zitayimitsidwa ndi achitetezowa.
Padakalipano boma la dzikolo lati laganiza zogulira apolisi malaya omwe amateteza anthu ku chipolopolo cha mfuti (Bullet Proof) komanso kupereka mifuti ndi zida zina kwa apolisiwa.
Nduna yoona za mdziko Ambrose Dery yati zida zatsopanozi zithandiza apolisi kulimbana ndi zauchifwamba zomwe zikuchitika mdzikolo komanso kudziteteza okha.
| 7 |
Kutetedza Okalamba ndi Udindo wa Aliyense MANEPO Wolemba: Thokozani Chiwaya Bungwe lolimbikisa ufulu wa anthu okalamba dziko muno la Malawi Network of Elderly Persons Organisation (MANEPO) lero lapempha anthu komanso mabungwe dziko muno kuti agwirane manja pothana ndi nkhaza zomwe anthu okalamba amakumana nazo dziko.
Polankhulapo mu mzinda wa Blantyre, pambuyo maphuziro omwe bungwe la MANEPO linakonzera ma komiti a madera olandira madandaulo kuchokera kwa anthu okalamba omwe akuwatcha complaints response mechanism pachingelezi, mmodzi mwa akuluakulu ku bungweli a Louisa Kanyongolo ati maphuzirowa athandiza bungweli kufikira okalamba omwe akhuzidwa ndi nkhanza zosiyanasiyana ku madera kwawo komweko kuzela ku makomiti a pansi pa bungweli.
Mamembala a komiti za MANEPO kulandira maphunziro Anthu amene ali mmakomiti abungweli omwe ali madera akufunika maphunziro ngati amenewa pofuna kusula kagwiridwe kawo ka ntchito pothandiza okalamba, anatero a Kanyongolo.
Mai Louisa anatipitiliza kunena kuti makomitiwa ndi amenenso ali ndi kuthukera kofikira zosowa za anthu okalamba kamba koti ndi omwe amakhala nawo okolambawa kumidzi komweko.
Mai Kanyongolo apempha mzika za dziko lino kuti zigwirane manja poteteza komanso kumenyera ufulu wa anthu okolamba pozindikila kuti tonse tizakalamba ndithu.
Tonsefe tizakalamba ndithu choncho tizizindikira kuti ndi udindo wa aliyense wotetedza okalamba posayanganira ntsikhu wake, anaonjezera motero mai Louisa.
Mau ake mmodzi mwa anthu amene anatenga nawo gawo pa maphuzirowa a Peter Mambala, anati maphuzirowa awathandiza kudziwa pamene amasalira pakagwiridwe kawo ka ntchito makamaka pofikila okalamba.
Taziwa malire anthu komanso udindo wathu poteteza achikulire mdziko muno makamaka madera athu owenso ndikumene kukupezeka okalamba, anatero a Mambala.
Mwadzina a Mambala anathokoza bungwe la MANEPO kamba kamaphunzirowa ponena kuti ntchito za mabungwe zimayenda bwino ngati anthu amenenso bungwelo likuwafikila ali nawo limodzi ngati momwe bungwe la MANEPO lachitila.
Ntchito za mabungwe zimakanika kufikira cholinga chake cheni cheni ngati anthu akumudzi eni ake sakuyikidwamo kudzera ku makomiti ngati athuwa, anaonjedzera motero a Mambala.
Maphuzirowa anakwanitsa kubweretsa pamodzi ma komiti a bungweli omwe amapezeka mboma la Blantyre.
| 14 |
Zikavuta, nawo anthu amakoka ngolo
Ngolo imakokedwa ndi ngombe kapena abulu, koma pena zikavuta nawo anthu amakoka. Pachithunzipa, anyamatawa adakoka ngoloyi ngombe zitathawa. Nanga titani? Kodi ngoloyi ena satibera? Iwo adangoganiza zoyamba kukoka ulendo nayo pakhomo. Zikavuta zilibe dolo.
| 10 |
Kulingalira malumbiro Abale anzanga, tidakhala pa Wenela kuonera kulumbiritsa kwa atsogoleri.
Woyamba kulumbiritsidwa adali Adama Barrow wa ku Gambia. Musandifunse kuti ameneyu ndidamudziwa bwanji, chifukwa sindikuyankhani. Mumafuna mumudziwe nokha? Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mwinatu sindidanene. Gambia ndi dziko limene anthu ake adachokera ku Zambia, muja anthu a ku Malawi adachokera ku Malaysia ndipo a ku Austria adachokera ku Australia! Ndife amodzi.
Tsonotu Barrow adalumbilitsidwa kuofesi ya kazembe wa Gambia ku Senegal patatha sabata zingapo atakwapula mkulu uja Yahaya Jammeh pachisankho. Bolatu kwa anzathu amakhala sabata zingapo wina asanalumbire koma pano pa Wenela usiku siudutsa! Mwaiwala kale muja Moya Pete adalumbirira? Uyu Barrow adalumbira ku Senegal paja chifukwa Yahaya amakana kuchoka pampando. Demokalase ndiye imeneyo! Yaponda yamwa! Yalakwa yalakwa! Yahaya adaziona.
Tsono sindikamba za kulumbira mdziko la eni. Kodi pa Wenela wina atakana kuti sanapambane pachisankho, wosankhidwa angakalumbire ku Mpanyira patsidya pa Tsangano? Zingatheke wosankhidwa pa Wenela kukalumbira ku Mbeya kapena Masvingo chifukwa sizingatheke pabwalo la pa Wenela? Winatu amalumbira adali mkulu uja Donal J Trump. Pajatu K2 000 ikutchedwa Trump chifukwa cha kukula mtima kwake. Iyetu adalumbira atagwira mabaibulo awiri. Loyamba lidali la mkulu wamtali uja, Abraham Lincoln. Kukadakhala kuno, bwenzi tikuti Moya Pete adalumbira atagwira baibulo lija adalumbirira gogo uja adandipeza ndikulima kwathu kwa Kanduku.
Koma zingatheke? Ndipo popita kokalumbira, Trump adayamba wamwa tiyi ndi uyu akutulukayu, Barrack Obama. Kenako, onse adakwera galimoto imodzi. Kuno kwathu zingatheke? Abiti Patuma ndi Moya Pete kukwera galomoto limodzi? Tsonotu sindili pano kukamba za Barrow kapena Trump. Yanga nkhani ndi ya Saulo Chagalauza. Pajatu mkuluyo adabwera ndi moto, kukamba zosintha zinthu kuphiri.
Mkuluyu lero wangoti ziiii! Sakukambapo kanthu za Joloji Mmera Chadyaka mkulu amene wafufuta chimanga chopezeka pambendera ya Dizilo Petulo Palibe, adatero Abiti Patuma.
Palibe chimene ndidatolapo.
Komatu Chadyaka adya ndalama zambiri. Nanga umboni wakuti adanyambita khusa uli kuti? adafunsa Gervazzio, akuika nyimbo ya Lucius Banda: Mabala.
Malume ndalama kubisa kubanki Pamene Mbumba yawo ikufa ndi njala Adya ndalama bwanji? Zonsetu tiziona mwezi uno ukamatha chifukwa ndiye tsikulo kuli kokakatula ndi sizala, adatero Abiti Patuma.
Adandipindanso.
Chomwe ndikunena, uyu Saulo akupenya, akumva ndipo pakamwa ali napo koma sakulankhula. Watsamwa. Mwinatu akuopa Chadyaka paja mpandowu ngolimbirana. Ndani safuna kukhala Barrow kapena Trump? 2019 ndi chaka chinacho, adatero Abiti Patuma.
| 10 |
Kusowa kwa mpikisano nkwachabe Pali mantha kuti zipani za mdziko muno zingayoyoke ngati makatani ngati mipando yonona yachipani monga wa pulezidenti ndi wachiwiri wake ipitirire kukhala yongotola popanda wopikisana naye ku misonkhano yaikulu ya zipani.
Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Izi zaunikidwa ndi otsogolera zitukuko kumidzi ena ndi katswiri pandale potsatira zochitika kumsonkhano waukulu wa chipani cha Peoples Party (PP) komwe mpando wa pulezidenti ndi wachiwiri wake kuchigawo cha kumpoto padalibe kupikisana.
Kusapezeka opikisana mmipandoyo kudapereka danga kuti mwini chipanichi, yemwenso ndi mtsogoleri wa dziko lino, Joyce Banda adutse popanda omugwedeza.
Naye wachiwiri kwa Banda, Khumbo Kachali adadutsa moyera.
Mboma lomwe langopita kumene la DPP, mwini chipanicho komanso yemwe adaali pulezidenti, Bingu wa Mutharika samachititsa msonkhano waukuluwu nkomwe, mmalo mwake iye amangoloza anthu mmaudindo a mchipanicho.
Chitsanzo, Mutharika adaloza Hetherwick Ntaba kukhala mneneri wachipani.
Mtsogoleri wakale yemwenso adali pulezidenti mchipani cha UDF, Bakili Muluzi atangotula udindo kwa Friday Jumbe kudali kukokanakokana mpaka pano pomwe chipanichi chagawikana.
Zitadziwika kuti kukhala msonkhano waukulu kuchipani cha PP, anthu ena monga mkulu wina wa bizinesi, Caesar Fatch, adabwera poyera kuti adzapikisana ndi Banda.
Koma poyandikira chisankhocho, Fatch adalengeza kuti wazisiya, ati adzayeseranso kutsogoloku.
Malinga ndi operekera ndemangawa, izi ndizo zikuchititsa kuti zipani za mdziko muno zizisokonekera pomwe pulezidenti wachipanicho wachoka paudindo chifukwa ofuna mpandowo amakhala akukokana, ena nkumathiothoka mchipani.
Katswiri wa pa zandale, Blessings Chinsinga wati zipanizi zitamakhala ndi msonkhanowu nkupezekanso olimbirana nawo mmaudindo onse, achipani si bwezi mavuto omwe adachitika ku UDF ndi DPP atachitika.
Izi si zachilendo mdziko; ngakhale mmaiko akunja mavutowa alipo. Koma mathero a zonse, chipani chimatha chifukwa anthu amayamba kukokana pomwe pulezidentiyo wachoka pampando.
Ndibwino mipandoyi idziphangiridwa chifukwa pomwe pulezidenti wachoka, amene adayamba kupikisana naye ndiwo amakhala patsogolo, adatero Chinsinga.
Makiyi Matukuta, mkulu wa bungwe la Malawi Carer ku Mayani mboma la Dedza, wati anthu kumeneko adali odabwa kumva kuti Banda wadutsa pampando wa pulezidenti popanda opikisana naye.
Padzikhala kupikisana; anthu amakhala ndi chidwi kumva zomwe opikisanawo akonza. Zateremu ndiye kuti ufune usafune mtsogoleri wanu amakhala yemwe wadutsayo.
Izi zimapha chidwi cha anthu ena omwe amafuna adzasankhe mtsogoleri yemwe amukonda, adatero Matukuta.
| 2 |
Mlonda anjatidwa kaamba kosolola Pamene kampani ya Inovantis mboma la Machinga imanyadira kuti izigona tulo tozuna chifukwa yalemba ntchito Ibrahim Justin, wa zaka 23, ngati mlonda woteteza katundu wawo ku ndipsi, kampaniyi sinadziwe kuti yatuma galu kumalondera nyama ya mbuzi yowotcha kale.
Wapolisi wotengera milandu kukhothi pa Liwonde Police Post, Ezekiel Kalunga, adauza bwalo la milandu la Liwonde kuti pa April 19 chaka chino akuluakulu a kampani ya Inovantis adakagwada kupolisi kukadandaula kuti chipangizo chopanga mphamvu ya magetsi kuchokera kudzuwa (solar panel) chidasowa pakampanipo.
Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Kafukufuku woyangana chipangizochi ali mkati mkulu wa alonda pakampanipo adakumana ndi munthu wina atanyamula chipangizocho, chimene adachizindikira kuti ndi cha kampani yawo.
Alonda onse adatengeredwa kupolisi ndipo atapanikizidwa ndi mafunso kuti adazembetsa chipangizocho ndani, Justin adavomera kuti ndiyeyo adasolola.
Kalunga adapempha khothi kuti limuthyape Justin ndi chilango chachikulu popeza khalidwe lakelo ndi lothawitsa anthu, makamaka a maiko akunja monga Inovantis, kudzakhazikitsa bizinesi zawo mdziko muno.
Popereka dandaulo, Justin adapempha bwalo kuti limupatse chilango chochepa popeza iye ndi nsanamira ya banja lake.
Woweruza milandu, Esther Phiri, adagwirizana ndi Kalunga ponena kuti khaliwe lakuba limabwezeretsa chitukuko mmbuyo kotero adamugamula kuti mlondayo akaseweze ndende kwa zaka ziwiri akugwira ntchito yakalavulagaga.
Justin amachokera mmudzi wa Kaudzu mdera la mfumu yaikulu Sitola mbomalo.
| 7 |
Mwapasa achokeHRDC Zipani za Malawi Congress Party (MCP) ndi UTM Party zati ziunika mwakuya ganizo la mgwirizano wa mabungwe omenyera ufulu wa anthu la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) lomema aphungu kuti akakane Duncan Mwapasa kukhala mkulu wa apolisi.
Mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika adasankha Mwapasa ngati ogwirizira mpandowo potsatira kupuma kwa yemwe adali paudindowo Rodney Jose yemwe wakwanitsa zaka zake zokapuma.
Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Ena akufuna kuti achoke: Mwapasa Mwapasa akugwirizira mpandowo kudikira kuti aphungu a Nyumba ya Malamulo akaunike mbiri ndi luntha lake pankhani za chitetezo nkuvomereza kapena kukana kuti mkuluyu akhale pampandowu.
Izi zili choncho potsatira zomwe ndime 154 (2) ya Malamulo a dziko lino imanena pakasankhidwe ka mkulu wa apolisi.
Pulezidenti akuyenera kusankha mkulu wa apolisi pogwiritsa ntchito mphamvu zake koma Nyumba ya Malamulo ili ndi mphamvu zounika wosankhidwayo nkumuvomereza kapena kukana. Akatero, komiti younika za kasankhidwe ka maudindo ya Public Appointments Committee (PAC) ikhoza kuunika kagwiridwe ntchito ka mkulu wa apolisiyo nthawi iliyonse, akutero malamulo.
Koma wachiwiri kwa wapampando wa HRDC Gift Trapence adati akuona ngati Mwapasa sangatsogolere bwino apolisi chifukwa amaoneka kuti amagwirizana ndi chipani cholamula cha Democratic Progressive (DPP) kotero sangatsogolere apolisiwo.
Iye adati pachifukwachi, bungwelo lakonza zomema aphungu a Nyumba ya Malamulo kuti asakamuvomere Mwapasa akamakumana podzakambirana za ndondomeko ya zachuma ya 2019/2020 mwezi wa mawa.
Mwapasa ndi wa DPP kutanthauza kuti chilichonse amapanga nchokomera chipani cha DPP. Kukhala mkulu wa apolisi, ndiye kuti polisi isanduka chida cha DPP mmalo mokhala chida cha Amalawi, watero Trapence.
Mwapasa adakana kulankhulapo pa nkhaniyi pocheza ndi nyuzipepala ya The Nation Lolemba HRDC itangolengeza ganizo lake pa msonkhano wa atolankhani.
Mneneri wa MCP Maurice Munthali wati chipanicho chili nchikhulupiliro mwa aphungu ake kuti akaona zochita nthawiyo ikadzafika pomwe mneneri wa UTM Party Joseph Chidanti Malunga adati chipani chiona zochita HRDC ikachipeza.
Poti iyi ndi nkhani ya ku Nyumba ya Malamulo, tiyisiya mmanja mwa aphungu athu omwe tili nawo chikhulupiliro chonse kuti akaunike Mwapasa mopanda mantha kapena kunyengereredwa. Nthawi yopatsirana maudindo patebulo idatha, adatero Munthali.
Ndipo Malunga adati: Padakalipano sitinena zambiri koma a HRDC akatipeza nayo nkhaniyi tidzayilandira nkupanga chiganizo mozama kuti Amalawi asataye chikhulupiliro mwa ife.
Katswiri pa ndale George Phiri wati ndondomeko yosankhira mkulu wapolisi ndi yomveka bwino ndiye ngati HRDC yaonapo vuto ndi Mwapasa, zili ndi iwo kutengera nkhawa zawo kwa aphungu.
Pulezidenti wasankha, koma zonse zikutsalira aphungu ku Nyumba ya Malamulo. HRDC ikawapatse nkhawa zake ndipo aphunguwo akaona kuti akatani pa nkhawazo. Koma khulupilirani kuti ngati Mwapasa wasankhidwira ndale kapena mtundu, akavutika kudutsa, watero Phiri.
Nyumba ya Malamuloyi ikakakana Mwapasa ndiye kuti akhala munthu wachiwiri kukanidwa ndi nyumbayo kukhala mkulu wa apolisi kutsatira kukanidwa kwa Mary Nangwale mu 2006 yemwe adasankhidwa ndi mtsogoleri wakale Bingu Wa Mutharika.
Aphungu ataunika maiyo adaona kuti samakwanira kutsogolera nthambi ya apolisi ndipo adamukana nkuunikira kuti Mutharika asankhe munthu wina woti atsogolere nthambi ya apolisi.
Mwapasa wakhalanso mdindo wachiwiri yemwe bungwe la HRDC silikufuna akhale pampando kutsatira wapampando wa bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) Jane Ansah yemwe pakali pano HRDC ikutsogolera zionetsero zoti atule pansi udindo wake.
| 11 |
Mkulu wa kunyumba ya chisoni agwidwa ndi ziwalo Abambo awiri omwe amagwira ntchito kunyumba yachisoni kuchipatala cha Kamuzu Central (KCH) akuzengedwa mlandu wodula maliseche a mtembo wa munthu wamwamuna omwe unali mnyumbayo poyembekezera kuti abale ake adzautenge.
Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mneneri wa polisi ya Lilongwe, Ramsy Mushani, watsimikiza za nkhaniyi ponena kuti aganiziridwawa, Lufeyo Mphimbi, wa zaka 54, ndi Samalani Jabu, wa zaka 58, adadula ziwalozo anthu ena atawauza kuti pali msika wa K8 miliyoni wa ziwalo za munthu wamwamuna.
Mushani wati anthu omwe akuwaganizira kuti adapeza msikawo, Sebita Mwale, wa zaka 27, ndi Eric Mwandira, wa zaka 34, adalonjeza ogwira ntchito kunyumba yachisoniwo kuti malonda akatheka adzawapatsa theka la ndalamazo.
Mushani wati apolisi adagwira ndi kumanga Mwale ndi Mwandira pamalo omwetsera mafuta a galimoto a Kaunda pamsewu wopita ku Mchinji atatsinidwa khutu ndi anthu ena kuti awiriwo adali ndi maliseche a munthu wamwamuna omwe amagulitsa.
Atafunsidwa za ziwalozo iwo adaulula kuti adachita kupatsidwa ndi abambo Awiri, Mphimbi ndi Jabu, omwe amagwira ntchito kunyumba yachisoni ku KCH ndipo onse anayiwa adavomera kuti adatenga nawo gawo pankhaniyi, adatero Mushani.
Iye adati Mwandira adapita kunyumba ya chisoniyo kukakumana ndi Mphimbi, yemwe ndi mnzake wakalekale, kukakambirana za nkhaniyo ndipo anthuwo adakambiranadi muofesi ya Jabu nkumvana.
Atagwirizana za malipiro Mphimbi ndi Jabu adalowa mchipinda chosungiramo mitembo momwe adatulukamo ndi malisechewo nkuwapereka kwa Mwandira yemwe adatengana ndi Mwale kuti akagulitse koma anthu adatsina khutu apolisi msanga, adatero Mushani.
Mwale ndi Mwandira akuwazenga mlandu wopezeka ndi ziwalo za munthu, zomwe zitsutsana ndi ndime 16 yokhudzana ndi thupi la munthu mmalamulo a dziko lino, pomwe Mphimbi ndi Jabu akuyankha mlandu wodula ziwalo za munthu wakufa kutsutsana ndi ndime 18 ndinso wopereka ziwalozo kuti zitsatsidwe malonda kutsutsana ndi ndime 16 (gawo B) la malamulo okhudza za thupi la munthu.
Bwalo la milandu ku Lilongwe Lachiwiri lapitali lidakana kutulutsa anthu anayiwa pabelo chifukwa ati likuopa kuti akhoza kuthawa.
Pogamula pempho la owayimira anayiwo pamlanduwo, Alemekezeke Mando ndi Chris Tukula, kuti apatsidwe belo, woweluza milandu kubwaloli magisitiriti Patrick Chirwa adati kupatsa belo anthuwo nkovuta chifukwa mlandu wawowo ndi woopsa.
Ndili ndi mantha kwambiri paganizo lopatsa anthuwa belo chifukwa pali chiopsezo chakuti chilungamo chikhoza kusokonezeka komanso chikhulupiriro chomwe anthu ali nacho mubwalo lino chikhoza kuonongeka, adatero Chirwa.
Mkulu wa chipatala cha KCH, Noordeen Alide, samapezeka pafoni yake yammanja kuti alankhuleko pankhaniyi makamaka mmene ntchito ya kunyumba yachisoniyo imayendera.
Mphimbi amachokera mmudzi mwa Chipazi, T/A Msakambewa, ku Dowa ndipo Jabu amachokera mmudzi mwa Msimbi, T/A Masula, ku Lilongwe. Mwale kwawo ndi kwa Chipoza, T/A Santhe, ku Kasungu, pomwe Mwandira ngwa ku Mwazisi, kwa Themba la Mathemba Chikulamayembe ku Rumphi.
| 15 |
MEC Yayamba Kupereka Zotsatira Za Chisankho Zotsimikizika Bungwe loyendetsa chisankho mdziko muno la Malawi Electoral Commission (MEC) layamba kutulutsa zotsatira zotsimikizika za chisankho cha president chomwe chachitika lachiwiri lapitali.
Malingana ndi wapampando wa bungweli Justice Dr. Chifundo Kachale, pofika 10 koloko ya mmawa wa tsiku la lero, bungweli linali litalandira zotsatira za maboma 26.
Kachale: Tili mkati mowunika zotsatirazi Mwa mabomawa anali atawunguza ndi kutsimikizira zotsatira za maboma anayi okha omwe ndi a Mulanje, Chiradzulu, Mwanza komanso Likoma.
Padakalipano zotsatira zomwe zatsala kuti zitipeze kuno ndi za boma la Mzimba ndi Dowa. Komanso padakalipano tili mkati mowunika zotsatira za maboma 22 omwe afika kalewa ndipo tibweranso nthawi ina kuti tifotokozere mtundu wa Malawi za nkhaniyi, anatero Dr. Kachale.
Mwazina Dr. Kachale ati ngakhale akazembe a mabungwe akunja sanabwere kudzawonelera chisankhochi, koma akulumikizana nawo ndi kuwadziwitsa mmene chisankhochi chikuyendera kudzera mwa anthu ena a mdziko muno omwe amagwira ntchito ndi mabungwewa.
| 11 |
Ulemu kwa Geoffrey Mwale Mkuluyo adali msilikali. Aliyense pa Wenela amamudziwa bwino. Akangoti waledzera, tsikulo ndiye kumakhala ndewu zafumbi. Akapanda kupeza womenyana naye pa Wenela, zonse zimakathera kwa mkazi wake.
Tonse tikudziwa kuti samasiya ndalama za ndiwo pakhomo msirikaliyo. Mkazi amati akafunsa ndalama ya pakhomo, makofi. Akati anawa chakudya, kukunthidwa ngakhale ndi zitsulo.
Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Ukhoza kukachita ngakhale uhule upeze yodyetsa anawa, adali kutero msirikaliyo.
Koma akangomva kuti mwamuna wina kumsika wamupatsa mkaziyo bonya waulere, nayenso ali pamoto.
Adali wozunguza.
Ngakhale kupita kutchalitchi adaleka kalekale. Ena ankamutcha Boko, ena akuti Isisi. Koma adali msirikali basi.
Tsiku lina adautunga kuyambira mmawa mpaka usiku. Amachoka kumowako nthawi itangodutsa 10 koloko. Wapamalopo atafunsa kuti amulipire, adalandira zibakera.
Atafika kunyumba, adapeza kalata ili pakhonde.
Chigawenga msirikali woipitsa dzina la asirikali anzako, munthu wa nkhanza kuposa Satana. Wandizunza mokwanira, ndamanga ulendo wakwathu. Komabe ndakusiyira chakudya chimene anzako anagula. Ndatengedwa ndi anzakowo, munthu wopanda nzeru iwe. Kukhakhala mtima ngati wakwananda kapena msana wa fulu. Estere.
Estere adali mkazi wa msirikaliyo. Adalowa mnyumba. Adafikira patebulo pomwe padali mbale ziwiri zovindikira. Adadziwiratu kuti mwinamo mudali nsima, mwinamo ndiwo. Kukhosi kudachita kuti dyokodyoko. Dovu lidati liyambe kuchucha.
Adayamba wasamba mmanja. Nthawi yopemphera adalibe. Mtima udali kugunda. Adavundukula mbale yoyamba, mudali miyala itatu. Miyala, osati mitanda itatu! Adatsegula mbale yachiwiri. Mudali masamba awiri a gwafa osaphika nkomwe. Adali atathiridwa tomato ndi mchere.
Msirikali adakwiya. Adayatsa fodya wamkulu amene ankasunga mujombo. Adayamba kukoka. Utsi sumatuluka nkomwe, amaupanirira. Amachita ngati akubanika.
Atatha kusutako, adakhala pansi. Momwe adagonera sadadziwe! Adayamba kulota.
Adalota kuti adali atamwalira. Adafika kumwamba, pampando wachifumu. Woweruza anthu abwino ndi oipa adamuuza mkuluyo kuti adamupatsa mwayi wolapa koma iye sadafune kulapa. Adamupulumutsa kungozi komanso matenda koma sadafune kulapa. Udali kukonda ndewu, kumenya mkazi ndi ana ako. Tsono ndikupatsa mwayi umodzi wobwerera kudziko lapansi. Subwerera ngati munthu. Sankha chinyama chimene ukufuna, adatero woweruzayo.
Msirikali uja adayamba kudya mutu: Ndisanduke mkango? Ndikaphaphalitsa nyama zina zakutchire. Koma ayi, alenje akandipha chifukwa akufuna chikopa, mchira ndi matumbo anga. Ndisanduke njovu, nyama ndi anthu azikandiopa. Koma ayinso, mnyanga wanga ukandiphetsa! Nanjinanji kusanduka nyani ndiye sindikalimba. Akandipha kuopa kuwapatsira ebola.
Pamapeto pake, adasankha kukhala kangaude. Choncho nditsetsereka kudziko nkukakhala mnyumba yogumuka zakazaka. Womulenga adamuuza: Chabwino, usanduka kangaude. Bwerera kudziko lapansi.
Apa mpomwe mkulu uja adadziwa kuti tsopano azitulutsa ulusi muja achitira kangaude. Hmmmmm! Hmmmmm! adali kutero, uku akumva kuti ulusi ukutuluka ndipo iye akutsikira kudziko lapansi.
Hmmmm! Hmmmmm! adapitiriza, ulusi ukutuluka. Posakhalitsa adayamba kuona dziko lapansi.
Hmmmm! Hmmmmm! adatsikirabe, ulusi ukutuluka. Kenako adafika padziko lapansi.
Adayangana kumwamba ndipo dzuwa lidamuthobwa mmaso. Apa mpamene msirikaliyo adadzidzimuka kutulo kwakeko. Poti atembenuke, adazindikira kuti wadzionongera.
Abale anzanga, mwinatu sindidakuuzeni, msirikaliyo ndi mmodzi mwa asirikali amene adamenya mnyamata wina timu yawo itagonja pampira wa dolola umene udalipo pa Wenela. Mnyamatayo adatisiya momvetsa chisoni, ndipo pano msirikaliyo limodzi ndi anzakewo sakudziwika kumene ali.
| 15 |
Zaka 18 kwa mphunzitsi wochimwitsa mwana Mphunzitsi yemwe adachimwitsa mtsikana wasukulu wa zaka zosadutsa 16 komanso kumupatsa mankhwala ochotsera pathupi wapukusa mutu wopanda nyanga bwalo la milandu la majisitireti ku Mzuzu litagamula kuti akalangidwe kundende kwa zaka 18.
Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Apa nkutitu mbwaloli muli ziii pomwe majisitireti Gladys Gondwe amapereka chigamulo chake kwa Mtendere Phiri, wa zaka 31, wochokera ku Bembeke, T/A Kachindamoto mboma la Dedza, yemwe amaphunzitsa pasukulu ina ya pulaimale ku Ekwendeni mboma la Mzimba.
Zidaonekeratu kuti mphunzitsiyu sadali wokonzeka kuti alandira chigamulo cha mtunduwu chifukwa majisitiretiyu asadafike mbwaloli, Phiri adamveka akufunsa apolisi omwe adali kumuyanganira ngati zingatheke kutuluka patsikuli.
Apolisiwo adamuyankha momupatsa chikhulupiriro chonse kuti zikuoneka kuti zimuyendera ndipo akonzeke chifukwa patsikuli akagona pofewa kunyumba.
Komatu zinthu sizidamuyendere chifukwa mmphindi zisanu zokha, majisitireti adali atapereka chigamulochi. Phiri adangoti zyoli mchitokosi cha bwaloli.
Popereka chigamulo chake Lolemba, Gondwe adati Phiri akuyenera kuseweza zaka 16 ndi kugwira ntchito yakalavula gaga pogona ndi mtsikana wosakwana zaka 16, ndipo pamlandu wopereka mankhwala ochotsetsa mimba adampatsa zaka ziwiri zomwe ziyendere limodzi ndi za mlandu woyambawu.
Iye adati wapereka chilango chokhwimachi pofuna kupereka phunziro kwa aphunzitsi ena omwe ali ndi khalidwe logonana ndi ana awo asukulu mmalo mowalimbikitsa pamaphunziro awo.
| 7 |
Kanduku achotsa mfumu Thambala: Ankandituma kutolera ndalama Kwathina ku Mwanza pamene T/A Kanduku wachotsa gulupu Thambala komanso kulamula ena awiri kuti alipe mbuzi.
Bwanamkubwa wa bomalo Gift Rapozo watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati anakumana ndi mbali ziwirizi Lachitatu msabatayi ndipo agwirizana kuti akumanenso zofufuza zina zikatheka.
Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Rapozo wati wayitanitsa kuti amve zokambirana zomwe zimachitika kufikira kuti mpaka Thambala agumulidwe pa mpando.
Padali nkhani zingapo zomwe zikukambidwa kuti mpaka a Thambala achotsedwe ufumu komanso mafumuwa amakumana pomwe amakambirana zinthu zomwe zapherezera kuchotsedwako ndiye pakhala zokambirana zomwe akhala akuunikira pa nkhaniyi mmbuyomu nkhaniyi tisadayitengere pena, adatero Rapozo.
Lachisanu lapitalo Thambala adauza Tamvani kuti Kanduku wamuchotsa ufumuwo chifukwa adakakhala nawo pamsonkhano wa mtsogoleri wa dziko lino Joyce Banda omwe udachitikira ku Chikhwawa.
Msonkhanowo, omwe cholinga chake kudali kutsekulira ntchito za chitukuko kwa Gulupu Chibwalizo kwa T/A Chapananga udachitika pa 7 August chaka chino.
Koma Kanduku wati ndizoonadi kuti Thambala wagumulidwa pampando koma wati ndi za ziii! kuti iye wachotsedwa pa mpando chifukwa chopezeka pamsonkhano wa pulezidenti ponena kuti sizikugwirizana.
Iye wati Thambala wakhala akubera anthu ndalama mwachinyengo powauza kuti Kanduku ndiye wamutuma.
Ugulupu ndidawapatsa ndine, zomwe achita ndi mlandu, mfumu imayenera kukhala ya chitsanzo chabwino osati kumabera anthu ake, ndichifukwa ndawachotsera ugulupuwo ndikuwasiira unyakwawa, adatero Kanduku yemwe adati wakweza mfumu ina kukhala gulupu.
Koma Thambala wati pa 7 adaitanidwa kukakhala nawo pamsonkhanowo koma ngakhale amapita adasiya milandu ina yomwe imayenera izengedwe.
Iye wati atabwerako adalandira kalata yomwe imachokera kubwalo la Inkosi Kanduku kuti akufunika kubwalo lawo.
Kumeneko kudali nkhani yokhudza malo yomwe ndidazenga ndiye munthu amene ndidamuzengayo samakhutira ndi chigamulo changa kotero adakagwada kwa Inkosi.
Tili pabwalo kukamba za nkhaniyo ndi pamene ndidafunsidwa chifukwa chomwe ndimapitira ku msonkhano wa Pulezidenti kusiya nkhaniyo pambuyo. Apa adandichotsa ufumu ndipo adati ugulupu wanga waperekedwa kwa nyakwawa Lupiya. Magulupu ena monga gulupu Tulonkhondo ndi Ngadziwe adawalipitsa mbuzi, adatero Thambala movomerezana ndi mkazi wake.
Iye wati atamva kuti ufumu wake wagumulidwa adalembera Rapozo kalata yomudandaulira. Kalatayo yomwe yaonedwa ndi Tamvani idali ndi mutu woti Dandaulo lakutsitsidwa udindo ndi kulipiritsidwa chindapusa yomwe mkatimo idatchula zopozeka kwake pamsonkhano wa pulezidenti.
Ndikukhulupirira kuti sadagwirizane ndi kupezeka kwanga pamsonkhanowo, adatero Thambala.
Koma Kanduku wati ndikutheka kuti Thambala akubweretsa dala nkhani yokapezeka kumsonkhano wa pulezidenti kuti ufumu wake uthenso.
Iwo akhala akunamiza anthu kuti alamulidwa ndi ine kuti atolere ndalama kwa anthu. Anthu omwe akhala akundidandaulira anabwera kwa ine kundifunsa zomwe ndidakana. Adatolera ndalama zoposa K70 000, adatero Kanduku.
Iye adati adaitanitsa Thambala kumufunsa za nkhaniyo. Kanduku wati chifukwa Thambala adapezeka wolakwa adamuchotsa pampandowo.
Ndapereka kale ugulupu kwa mfumu ina, poti nkhaniyi ili kwa DC ndiye tikamva momwe zilili, adatsindika Kanduku.
Iye adati walipitsa mfumu Ngadziwe pazifukwa zina osati zokakhala nawo pamsonkhano wa pulezidenti.
Titafunsa Thambala ngatidi adatenga ndalamazo iye adavomera kuti amatenga ndalamazo motumidwa ndi Kanduku.
Adatiuza kuti popeza kudera lathu kukudutsa njanji ndiye alembetsa mayina a anthu amene adzalandire nawo chipepeso ngati njanji yadutsa pakhomo pako. A Kanduku adati nditolere ndalama kuti tikawathokoze, adatero Thambala.
Iye adati poyamba adapititsa K200 000 ya mthumba mwake kuti asatolerenso ndalama kwa anthu koma Kanduku adakana ponena kuti yachepa.
Kenaka ndi pamene ndimauza anthu kuti andithandize, sindidachite mwakufuna kwanga, adatero.
Rapozo adati nkhanizi zafika kuofesi kwake ndipo chenicheni chidziwika zokambiranazo zimatheka.
| 8 |
Bande Walimbikitsa Aphungu Anzake Kuti Agwire Ntchito Ndi Boma Latsopano Phungu wa dera la kumvuma kwa mzinda wa Blantyre, John Bande walimbikitsa aphungu a madera osiyanasiyana mdziko muno kuti agwire ntchito limodzi ndi boma latsopano kuti madera awo atukuke mwamsanga.
Bande walankhula izi ndi Radio Maria Malawi potsatira ntchito zosiyanasiyana zomwe boma likugwira mdera lake.
Bande: Posachedwa tiyika tala Iye wati kulumizana kwabwino ndi boma lomwe linalipo kwathandiza kwambiri kulandira ntchito zosiyanasiyana pa miyezi isanu ndi umodzi yomwe wakhala akutumikira mderali ngakhale kuti kuti iye ndi phungu woyima payekha.
Bande anati zimenezi zathandizira kusintha mawonekedwe a dera lake makamaka pa ntchito za chitukuko.
Tithokoze Mulungu kuti kuno ku Blantyre City East misewu yathu ndi yabwino popeza tapala koma posachedwapa ina mwa misewu imeneyi izakhala ya tala, anatero a Bande.
Iwo atsindikanso kuti akhala akugwira ntchito ndi boma latsopano lomwe likutsogoleredwa ndi Dr. Lazarus Chakwera kuti ntchito za chitukuko zomwe zinayamba ndi boma la chipani cha DPP mdelaro zipitilire ndi kupindulira anthu awo.
| 11 |
Bokoharam Idakasungabe Msungwana Wachikhristu Wolemba: Thokozani Chapola s/2019/09/boko-haram.jpg 303w" sizes="(max-width: 576px) 100vw, 576px" />Zigawenga za Boko Haram Msungwana wina wa chikhristu amene anagwidwa ndi gulu la zauchifwamba la Boko Haram mchaka cha 2018 akuti ali moyo.
Malingana ndi malipoti a Independent Catholic News msungwana-yu anamugwira mu February chaka chatha pamodzi ndi atsikana ena oposera dzana limodzi a pasukulu ina ya ukachenjede mdzikomo.
Malipoti ati atsikana enawo anawatulutsa patangopita mwezi umodzi ati kamba koti anali a chisilamu, koma kuti msungwana-yu Leah Sharibu anamuuza kuti amutulutsa pokhapokha atavomera zosiya chikhristu ndi kulowa chisilamu koma kuti iye anakakamirabe chikhristu chake zomwe zinachititsa kuti asatuluke ku malo a zigawengazo.
Padakalipano boma la dzikolo lauza atolankhani kuti msungwana-yu adakali ku malo a zigawengazi, koma kuti likuchita zokambirana kuti zigawengazo zitulutse msungwanayu.
| 13 |
Anthu a ku Likoma alirira Ilala Anthu okhala pazilumba za Likoma ndi Chizumulu ati akulira ndipo moyo ukutentha chifukwa cha kusiya kuyenda kwa sitima ya Ilala.
Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC T/A Mkumpha wa ku Likoma yati kuleka kuyenda kwa sitimayo kwachititsa miyoyo ya anthu pa zilumbazo kukhala yovuta.
Malinga ndi iye, kuonongeka kwa sitimayo kwachititsa chiyembekezo chimene anthuwo adali nacho kwa miyezi 10 pomwe sitimayo imakozedwa kuti chilowe mmadzi akuya.
Moyo ukuvuta pa Likoma chifukwa sitimayo si ikuyenda. Ntchito za chitukuko zaimiratu chifukwa cha vuto la mayendedwe, adatero Mkumpha.
Sitimayo idafa sabata zitatu zapitazo chifukwa cha mavuto ena. Izi zidachitika sitimayo itangoyenda maola ochepa, patatha miyezi 10 akuikonza. Kukonzako kudadya US$2 miliyoni (zoposa K800 miliyoni).
Mneneri wa kampani yoyendetsa sitimayi ya Malawi Shipping Company adati ayambanso kuikonza zitsulo zina zikafika mdziko muno.
Tikuyembekeza zitsulo zimene kampani ya Barloworld ipeze ndipo sitimayi iyambanso kuyenda ikangokonzedwa, adatero Msowoya.
Iye adati zonse zikayenda, sitimayi ayamba kuikonza Lolemba.
Aliyense ndi wokhudzidwa ndi momwe zinthu zilili. Ngakhalenso amene amabweretsa zitsulo zikuwakhudza koma tikuchita zotheka kuti sitimayi iyambenso kuyenda, adatero Msowoya.
Ilala ndi sitima yokhayo yaikulu imene imayenda panyanja ya Malawi.
Sitimayi idayamba kuyenda panyanjayo mchaka cha 1951 ndipo imanyamula anthu oposa 300.
| 17 |
Kasanthuleni za chisankho Pamene aphungu a Nyumba ya Malamulo akukonzekera kukumana kuyambira Lolemba likudzali, akadaulo ena awapempha kuti akalunjike pa za chisankho cha 2019.
Ngakhale aphunguwo akhale akukambirana za momwe ndondomeko ya zachuma yayendera katswiri pa ndale George Phiri yemwe amaphunzitsa ku University of Livingstonia (Unilia) wati nkhani zina zonse zikhoza kuyamba zaima koma nkhani ya chisankho njofunika kuikambirana chifukwa ikukhudza tsogolo la dziko.
Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Aphungu mNyumba ya Malamulo mmbuyomu Zipani za ndale zakhala zikuthirira ndemanga pa za kalembetsedwe konyentchera mkaundula wachisankho, nkhani zokhudza zipolowe pa ndale, kusowa kwa makina akalembera ndi mphekesera zofuna kudzabera chisankho ndipo Phiri wati uwu ndi mpata woti aphungu akakambirane nkhanizi mwachindunji.
Nkhani ya bajeti ili apo, aphungu asakataye nthawi ndi za ziii ngati momwe amachitira muja. Nthawi yatha, uwu ndi mwayi wawo wokonza Malawi. Kukonza Malawi ndi chisankho chomwe chikubwerachi, adatero Phiri.
Iye adati nkofunikanso kuti aphungu asanthule bwino za momwe akhala akuyendetsera thumba la ndalama za chitukuko la Constituency Development Fund (CDF). Ndemangayo ikudza pomwe lipoti ya nduna ya zachuma Goodall Gondwe kumayambiriro a chaka chino lidaonetsa kuti aphungu 20 adasokoneza ndalama za CDF koma mpaka lero palibe phungu amene adatchulidwa ndi kusololako.
Phungu aliyense amalandira K18 miliyoni mu bajeti iliyonse koma apanga nayo chiyani cholozeka? Anthu akuvutikabe ngati kale, watero Phiri.
Katswiri pa za kayendetsedwe ka dziko Makhumbo Munthali wati aphungu ayenera kukambirana za momwe chisankho chingayendere mwa bata ndi chilungamo. Iye adati pali nkhani zingapo zimene a zipani akhala akudandaula monga kalembera wa zisankho wophotchoka, kusowa kwa makina ku bungwe la zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) zomwe zidadzetsa chikaiko zimene aphungu akuyenera kukaunikira.
Pambali pokambirana mfundo zoti chisankho chidzakhale cha mtendere ndi chilungamo, akumbukirenso nkhani zina monga mabilu okhudza zachuma monga za migodi. Ndalama zankhaninkhani zikutuluka mdziko muno chifukwa chopanda mfundo zokhwima, watero Munthali.
Chipani cha Peoples P(PP) chati chikugwirizana ndi maganizo a anthu ndi akadaulo pa nkhani zofunika ku nkhumano ya aphungu.
Mneneri wachipanichi Ackson Kalaile wati nkhani ya chisankho njosathawika pafikapa chifukwa ikukhudza miyoyo ya aMalawi.
Tafika pano Amalawi adataya chikhulupiliro ndiye ntchito yonse yobwezeretsa chikhulupilirocho ili mmanja mwa aphungu ndipo nthawi yake ndiyomweyi, adatero Kalaile.
Mneneri wa Malawi Congress Party (MCP) Maurice Munthali adati akuluakulu achipanichi ndi aphungu ake akumana mawa Lamulungu kuomba mkota wa mfundo zopita nazo kunyumbayi.
Mneneri wachipani cha Democratic Progressive (DPP) Nicholas Daus adati chipanicho sichingakambe mfundo zake ndi atolankhani chifukwa zopita kunyumba yamalamulo zili ndi njira yake yodzera.
Iye adati zonse zikakonzeka, komiti yoyenera idzalengeza. Sitingamakambirane ndi atolankhani mfundo zomwe takambirana choncho ndilibe yankho, adatero Dausi Posanthula nkhani ya momwe aphungu agwirira ntchito mmbuyomu, iye adayamika momwe aphunguwo adatsatira nkhani yomwe nduna yakale ya malimidwe George Chaponda amamuganizira kuti adachita chinyengo pogula chimanga kuchoka ku Zambia.
Iye adati ngakhale izi zili choncho, aphungu amene adasankhidwa mu 2014-wa akanika mzambiri chifukwa mmalo mothandiza kutukula dziko, iwo adathandizira kulilowetsa pansi.
Aphungu adayesetsa kukoka nkhaniyo ya chimanga ndipo tidayamika, koma tikawayika pasikelo ya udindo wawo, palibe chomwe adachitapo mzaka zonsezi, adatero Munthali Amalawi ena amene tidacheza nawo aonetsa kuti khumbo lawo lagona poti aphungu akambirane zakupsa zokhudza chisankho.
Jane Mapira wa ku Lilongwe wati iye akadakonda aphungu akadakambirana nkhani yokhudza kusintha akuluakulu a MEC omwe wati akhumudwitsa kale anthu nzochitika zawo.
Wilson Thomas wa ku Zomba wati iye sakuona choti aphungu azikatayira nthawi nkukambirana zinthu zomwe sizingasinthe kalikonse ndipo wati kuli bwino aphungu akangokambirana za bajeti nkumabwerako.
Ngakhale atakambirana nkhani za chisankho, palibe chingasinthe chifukwa nthawi yatha kale. Apa akangokambirana za bajeti nkumabwerako kukadikira chipande mu May chaka cha mawachi basi, watero Thomas.
Ukatha msonkhano wa aphungu wa chaka chino, aphunguwo adzaakumana komaliza mwezi wa March chaka cha mawa, kutangotsala miyezi iwiri kuti chisankho cha 2019 chichitike.
| 11 |
Zilango zophweka zivulaza maalubino Miyezi 18 kwa ofuna kugulitsa alubino ku DZ Pali mantha kuti maalubino angapitirire kuona zokhoma mdziko muno ngati boma silichita machawi kuti lamulo latsopano loteteza anthuwa liyambe kugwira ntchito, mkulu wa bungwe lomenyera ufulu wa maalubino la Association of People with Albinism in Malawi (Apam), Bonface Massah, watero.
Mantha a mkuluyu akudza pamene anthu amene apezeka olakwa pozunza kapena kusowetsa maalubino akupitirira kulandira zilango zozizira.
Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Lachisanu sabata yatha, bwalo la milandu mboma la Dedza lidagamula mayi Siyireni Nyata ndi Chrissie Lajabu kukaseweza kundende zaka ziwiri ndi miyezi 6 poopseza mwana wa zaka 14 kuti amupezera kale msika.
Malinga ndi mneneri wa polisi ku Dedza, Edward Kabango, amayiwa akhala akulankhula izi kwa nthawi yaitali.
Amati ndi kanyama kosendasenda ndipo akapezera kale msika woti akakagulitse, adatero Kabango.
Kaamba ka kuopsezedwako, mwanayo akuti adasiya sukulu pochita mantha kuti angakumane ndi anthu amene amati amugulawo. Makolo a mwanayu akuti adakadziwitsa apolisi ndipo pa April 15 amayi awiriwo adanjatidwa.
Bwalo lidawapeza olakwa ndipo lidawaimba mlandu wobweretsa mantha kwa mwanayu ndipo adawalamula kuti akaseweze zaka ziwiri ndi miyezi 6 kundende.
Chilangocho chikudza pamene mkulu winaso ku Machinga, Sinoyo Wyson, wagamulidwa kuti akakhale kundende zaka ziwiri posowetsa mwana wa zaka 11 wachialubino.
Mu May chaka chinonso amuna awiri ku Zomba adawalamula kukaseweza miyezi 12 popezeka ndi mafupa alubino.
Massah akuti si zoona kuti milandu yotere izikhala ndi zilango zofewa ndipo wati bungwe lawo lichitapo kanthu kuti maalubino asamakhale mwamantha.
Ndikumvanso kwa inu za nkhani ya ku Dedzayo, koma tifufuza. Pankhani ya ku Machinga ndiye tidakagwadanso kubwalo lalikulu kuti aunikenso chilangochi, adatero Massah.
Koma iye adati oweruza milandu si olakwa pa zigamulo zomwe akuperekazi chifukwa malamulo a dziko lino amapereka zaka ziwiri kwa wopalamula mlandu wozembetsa munthu.
Iye adati mavuto onsewa angathe ngati lamulo la Anti-Human Trafficking lingayambe kugwira ntchito. Lamuloli lidavomerezedwa kale ndi aphungu a Nyumba ya Malamulo komanso mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika.
Lamulo latsopanoli likupereka zaka khumi kwa amene wapalamula mlandu wonga uwu, chomwe ndi chilango chokhwimirako. Tayesera kufunsa anzathu a boma nthawi yomwe lamuloli liyambe kugwira ntchito koma zomwe tikumva si zopereka chiyembekezo.
Maalubino sakutetezedwa kupatula kungolankhula chabe, zomwe sizingateteze anthuwa, adatero Massah.
Koma mneneri muunduna woona za chilungamo ndi malamulo, Apoche Itimu, akuti lamuloli lidavomerezedwa kale ndi Mutharika.
Chomwe ndikudziwa nchakuti lamuloli lidavomerezedwa, sindingakumbuke kuti lidasindikizidwa liti. Panopa kwangotsala kuti liyambe kugwira ntchito, koma ngati mukufuna kudziwa zenizeni za lamuloli funsani unduna wa zamdziko, adatero Itimu pouza Tamvani.
Mneneri ku unduna wa zamdziko, Rose Banda, Lachiwiri msabatayi adati timuimbire tsikulo lisadathe kuti atipatse zenizeni zokhudza lamuloli.
Koma pakutha pa tsikulo Banda adati sadakumane ndi oyenerera amene angamufotokozere nkhani yonse yokhudza lamuloli.
Lachitatu adatitumizira uthenga pafoni kuti akhala ndi zotsatira zonse pofika Lachinayi.
Maiko monga Tanzania, Mozambique, South Africa ndi Zambia ali ndi lamuloli lomwe limakhaulitsa opezeka kuti apalamula mlanduwu, pamene mtsogoleri wa dziko la Zimbabwe Robert Mugabe adakhazikitsa ndondomeko yapadera yothanirana ndi anthuwa.
Mutharika wakhala akumalankhula pawailesi ya MBC mawu oopseza kuti amene apezeke akusautsa maalubino athana nawo.
Koma ngakhale Mutharika angalankhule maka, kukhoti akuyendera zomwe malamulo amanena posatengera mawu ake. Izi zapangitsa mabungwe monga Apam kuti alimbikitse kupempha boma kuti likhazikitse lamulo lokhwima pofuna kuteteza miyoyo ndi maufulu a maalubino.
Massah akuti nthawi yakwana kuti mabungwe amene amamenyera ufulu wachibadwidwe ndi ena agwirane manja pofuna kuthana ndi mchitidwe wozunza maalubino.
Mdziko muno mukangochitika nkhani mumaona amabungwe akubwera pamodzi kudzudzulapo, koma zomwe zikuchitika mmakhoti athu palibe amene akulankhulapo. Tikufunika tigwirane manja kulimbana ndi nkhaniyi ngati tikufuna tipambane nkhondo yoteteza anthu [amene ali ndi zilema monga maalubino], adatero Massah.
Nkhani zosowetsa maalubino komanso kufukula manda awo zidafika pachimake mu February chaka chino ndipo anthuwa pamodzi ndi amabungwe ena adachititsa msonkhano mumzinda wa Blantyre kudandaulira boma kuti lichitepo kanthu.
Pamsonkhanowo, Senior Chief Kawinga ya mboma la Machinga idati ndi zosamveka kuti chilango cha wosowetsa munthu chizikhala chochepa.
Munthu wina adaba ngombe koma adamupatsa chilango choti akakhale kundende zaka zisanu pamene wosowetsa munthu akumupatsa zaka ziwiri. Pali chilungamo apa? Kodi ngombe ikhale yofunikira kwambiri kuposa munthu? Kodi alubino si munthu? adadandaula Kawinga.
| 7 |
Anatchezera Ukuchita njomba Gogo Natcheteza, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndine mtsikana wa zaka 25 ndipo ndakhala pa chibwenzi ndi mnyamata wina kwa zaka zinayi.
Mnyamatayu ali ndi nyumba yake ndipo akugwira ntchito yabwino pa kampani ina yopanga mafuta wophikira mu mzinda wa Lilongwe.
Tidagwirizana kuti tidzakwatirana, koma mnzanga ndikamufunsa za banja amangozengereza.
Kumuuza kuti abwere kwathu azaonekere amangoti ndidzabwerabe mpaka zaka nkumatha.
Gogo, kodi pamenepa nditani popeza mnyamatayu ndimamukonda ndi mtima wanga wonse? JPJ Lilongwe JPJ Nkhaniyi siyachilendo. Atsikana ambiri amadandaula kuti anyamata adawauza kuti adzawakwatira, koma akuchulutsa njomba.
Mnyamata wofuna banja sasowa. Sazengereza mwayi wokaonekera kwa makolo a mtsikana ukapezeka.
Anyamata ambiri safuna banja. Amangofuna kugona ndi atsikana ndipo chakumtima kwawo chikapwa amawasiya nkukapeza ena. Uku nkulakwa.
Muunikeni bwino bwenzi lanuyo kuopa kudzanongoneza bondo mtsogolo. Paja amati mtsinje wa tinkanena udakathera msiizi.
Gogo Natchereza Mutu wazungulira Ndine mtsikana wa zaka 23 ndipo ndili ndi mwana mmodzi.
Mnyamata wina adandiuza kuti akundifuna chibwenzi ndi cholinga choti adzandikwatire mtsogolo ndipo ndidalola.
Koma makolo ndi abale ake amamukaniza kuti asakwatiwe ndi mtsikana wa mwana moti panopa zochita za bwenzi langa sindikuziona bwino.
Ndikamuimbira foni nthawi zina sayankha. Ndikamutumizira uthenga pa WhatsApp umaonetsa kuti waona, koma sayankha.
Gogo, mutu wanga wazungulira nditani? APA APA Usadandaule, ungozivomereza. Makolo ena amaletsa ana awo kukwatira atsikana oti adaberekapo kumene kuli kulakwa.
Anthu akakondana saona zoti wina ali ndi mwana kapena ayi.
Apa zikuonetsa kuti mnyamatayo wamvera zonena za makolo ake.
Choncho kutha kukhala kovuta kuti chibwenzi chanu chipitirire.
Limba mtima, mudzapeza mnyamata wokukondani posatengere kuti mudaberekapo.
Usada nkhawa. Chachikulu ndi kudekha. Sunga khosi mkanda woyera udzavale.
| 12 |
Kulira, chimwemwe ndi banki mkhonde Ngakhale adali ndi chidwi choyamba bizinezi kuti atukuke, kusowa kwa mpamba kumapondereza khumbolo. Sanderson Yuba wa mmudzi mwa Namalima kwa T/A Nazombe mboma la Phalombe adakanika kutenga ngongole kubanki kaamba kosowa chikole komanso kuopa chiongola dzanja chokwera.
Lero mkuluyu ndi mmodzi mwa makhumutcha mderalo kutsatira ngongole yomwe adatenga kubanki mkhonde ndi kuyamba bizinezi ya matabwa mpaka wamanga nyumba ya malata, kugula njinga ya moto ndi ziweto.
Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mabanki mkhonde afalikira mdziko muno Kupanda banki mkhonde loto langa loyamba bizineziyi si likanakwaniritsidwa. Bwenzi pano ndili mpopangolo wa mmudzi. Bankiyi idandithandiza kupeza mpamba, adatero Yuba.
Yuba ndi mmodzi mwa Amalawi omwe miyoyo yawo yasintha chifukwa cha mabankiwa. Koma si onse otenga nawo mbali akusimba lokoma, ena akumana ndi zikhomo kutsatira kusokoneza ngongole zawo za banki mkhonde ndipo ali muumphawi.
Mmodzi mwa iwo ndi Janet Mawata wa mboma la Phalombe lomwelo yemwe atakanika kubwenza ngongole ya K20 000 adalandidwa katundu.
Mayi wina, yemwe anati tisamutchule dzina, ku Zomba adalandidwa nyumba kaamba ka ngongole ya K250 000 ndipo padakalipano umoyo wake ukuvuta.
Pakutha pa chaka, mmizinda ndi mmatauni anthu akumagawana ndalama zochuluka, ena mpaka K7 miliyoni, kuchoka kubanki mkhonde. Koma ndalamazi zimasungidwa mnyumba mwa membala wosankhidwa kutero, osati kubanki.
Izi zidachititsa mkulu wakale wa banki yaikulu mdziko muno ya Reserve Bank of Malawi (RBM), Charles Chuka kunena kuti mabanki mkhonde sakufunika chifukwa akusokoneza kayendedwe ka chuma.
Mabungwe ena atsutsa izi.
Mkulu wa Community Savings and Investing Promotion (Comsip) bungwe lomwe limayanganira mabanki mkhonde, Tenneson Gondwe, adati kutero ndi kusokoneza cholinga cha ndondomekoyi yomwe imapereka mpata wa ngongole kwa anthu osowa.
Anthuwa amasonkha ndalama zomwe amabwerekana ndi kuyamba mabizinezi komanso kugawana pakutha pa chaka. Kulowerera kwa RBM kungasokoneza miyoyo ya anthu. Ngati akufuna angopanga banki ya kumudzi yomwe izikwaniritsa zosowa za anthu, adatero Gondwe.
Kafukufuku wa bungwe la Finscope adapeza kuti anthu 50 pa 100 ali onse mdziko muno ali ndi kuthekera kofika ku mabanki a pamwamba koma 21 pa 100 wo ndi amene ali ndi mabuku ku mabankiwo.
Zotsatirazi zikupereka mpata kumabanki mkhonde kukhala ndi anthu ochuluka poonjezera chiongola dzanja chochepa chomwe amapereka pa ngongole iliyonse.
| 2 |
Lamulo Lothandiza Anthu Kupeza Mauthenga Mosavuta Liyamba Kugwira Ntchito Posachedwa-Kazako Unduna wa zofalitsa nkhani watsimikizira aMalawi kuti lamulo lothandiza anthu kupeza mauthenga mosavuta la Access to Information (ATI) liyamba kugwira ntchito posachedwapa.
Kazako: Anthu anavota kuti zinthu zisinthe Nduna mu undunawu a Gospel Kazako ndi omwe anena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi.
Iwo ati mtsogoleri w adziko lino anasayinira kale lamuloli koma anthu ena mu ulamuliro wa chipani cha DPP ndi omwe amalepheretsa kuti lamulori liyambe kugwira ntchito yake.
Vuto la dziko lomwe limayendetsedwa ndi mabanja awiri kapena atatu kapena anayi limakhala limeneli ndipo umboni wake ndiwa lamulo limeneli la Acces to Information. Nyumba ya malamulo inavomereza komanso a president anasayinira koma mabanja ena ake ochepa anangoganiza kuti lisayambe kugwira ntchito zomwe ndi zoyipa kwambiri, anatero a Kazako.
Pamenepa a Kazako ati mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera waonetsa kale chidwi choti lamuloli liyambirenso kugwira ntchito ndipo wati boma lomwe lilipo padakalipano lilibe chilichonse choti libise choncho lamuloli liyamba kugwira ntchito.
| 7 |
Ntchito yomanga njanji ya ku Nkaya yaima Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Ntchito yomanga njanji yochoka ku Kachaso kupita ku Nkaya ayiimitsa mpaka kampani ya Mota-Engel ndi ogwira ntchito kukampaniyo atamvana chimodzi.
Ogwira ntchitowo akunyanyala pofuna kukakamiza mabwana awo kuti awakwezere malipiro komanso kuti nzika 300 za ku Thailand zipakire.
Kunyanyalaku kudayambira Lolemba pa 24 June ndipo Lachiwiri Nduna ya za Ntchito Eunice Makangala idatsetserekera kumeneko kukalankhula ndi ogwira ntchitowa kuti abwerere kuntchito koma izi sizidaphule kanthu chifukwa pofika Lachitatu mmawa nkuti ogwira ntchitowa asadabwerere kuntchito.
Mmodzi mwa ogwira ntchito kumeneko ndipo akuchita nawo sitalakayo koma sadafune kutchulidwa dzina adauzaTamvaniLachitatu kuti iwo sagwira ntchito mpaka dandaulo lawo litamveka.
Ndikukamba pano anzathu akubwera kuchokera ku Mwanza kudzatithandiza sitalakayi, sitibwerera kuntchito mpaka titaona malipiro athu akukwera komanso anthu omwe achoka mdziko la Thailand akubwerera kwawo, adatero mkuluyo.
Padakhota nyani mchira mpakuti kampaniyi sabata zitatu zapita akuti inathotha gulu la ogwira ntchito kumeneko omwe ndi a mdziko muno ndi kulemba ena ochokera ku Thailand.
Anthuwa akuti ndi pafupifupi 300 koma chenicheni chomwe amabwerera mdziko muno sichioneka chifukwa ena sadziwa ntchito ndipo amachita kuphunzitsidwa ndi Amalawi.
Chodabwitsa nchakuti malipiro a akunjawo adali okwera kuposa a Amalawi omwe amatha ntchito.
Ntchito yake yomwe akugwira ndi kuyendetsa mathirakitala ndi a mabewula zomwe Amalawi timatha, ena mwa alendowo sakuthanso kugwira ntchito ndipo tikuwaphunzitsa ndife. Tikudabwa kuti izi zikuchitika bwanji? Nanga nchifukwa chiyani akulandira ndalama zoposa ife omwe tikutha ntchito? adadabwa mkuluyo.
Malinga ndi iye, Amalawi akulandira ndalama yosaposa K30 000 pomwe akamuna akunjawa akumatula makwacha owaposa iwo.
Koma Makangala adati walankhula ndi akuluakulu a kampaniyi kuti mamulumuzana a mdziko la Thailand omwe alibe ukadaulo wa ntchito apakire ndipo azipita.
Lolemba, mkulu wa kampaniyi Jose Denis da Silva wati akuluakulu a kampaniyi akukambiranabe ndi ogwira ntchitowa ndipo iye adapereka chiyembekezo kuti kusamvanaku kutha popanda zovuta.
Mota-Engel ndi kampani yomwe yalemba kampani ya ku Brazil yotchedwa Vale kuti imange njanjiyi yomwe ikuchokera ku Moatize ku Tete mpaka ku Nacala Port mdziko la Mozambique kudutsira mdziko la Malawi.
Malinga ndi yemwe amatitsina khuku pankhaniyi, pofika Lachinayi akuti mbali ziwirizi zinalepherabe kugwirizana ndipo zomwe auzana nkuti zokambirana zidzachitike Lachiwiri sabata ikudzayi.
Izi zikusonyeza kuti sitigwira ntchito mpaka Lachiwiri lomwe tidzagwirizane mfundo zenizeni tisanabwerere ku ntchito. Pazokambiranazo akutinso kubwera akuluakulu ena a kampaniyi ochokera mmayiko ena komanso mbali ya boma.
Sitikusinthika pa mfundo zathu kuti akuluakulu a dziko la Thailand azipita ndipo timva kuti pomwe tikumane Lachiwiriro atiuza zotani, adatero mkuluyo.
Pomwe timalemba nkhaniyi nkuti yankho pa kunyanyalako lisanadziwike.
Kampani ya Mota idalemba Amalawi oposa 3 000 omwe akugwira ntchito zosiyanasiyana kumeneko.
| 17 |
Wagolosale ndiye adandipatsa nambala yake Anthuni, njira zophera khoswe nzambiri koma chachikulu khosweyo afe basi.
Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ena pofuna mkazi amachita kugwa mngongole kuti aoneke ngati, komatu nkhani ya mnyamata wodziwika bwino pa zautolankhani, Vincent Phiri, yemwe sabata yathayi wapanga chinkhoswe ndi okondedwa wake Mable Pikani, sidakhale choncho.
Mnyamatayu akuti kumangika pakamwa kudalipo mpaka adachita kufunsa nambala ya lamya pagolosale yomwe msungwanayo amakonda kugula zinthu ku Ndirande munzinda wa Blantyre komwe onse amakhala.
Akufuna kudzakhala banja lachitsanzo: Mable ndi Vincent Iye adati ngakhale adatenga nambala ya lamyayo, sadayende moyera kufika pomwe alipa kaamba kakuti akatumiza timauthenga ta palamya namwaliyo amayankha mosonyeza kuti alibe chidwi. Koma pali khumbo, njira imakhalapo.
Tsiku lina ndidaganiza zomuimbira ndipo ndidamupempha kuti ngati nkotheka tikumane ndili naye mawu ndipo adandiyankha kuti ngati ndikufuna kukumana naye ndikampeze kwawo, adatero Phiri.
Iye adati posakhalitsa ubale udayambika mpakana kugwirizana za banja chifukwa onse adaona kuti kudalembedwa kuti adzakhalira limodzi mpaka imfa.
Chinkhoswe chidalipo pa 28 November ku Kabula Hill mboma la Blantyre ndipo zokonzekera zili mkati kuti chaka chamawachi adzamange ukwati woyera.
Vincent adati Mable ndi munthu yemwe ali ndi mtima wa mayi, wachikondi, wangwiro komanso wolimbikira ndi wodziwa chomwe akufuna mmoyo mwake.
Naye Mable adati Vincent ndi mnyamata wolimbikira, wamasomphenya ndinso wopanda mtopola ndi anthu.
Pano Vincent ndi woyanganira za momwe malonda akuyendera kukampani ya Finca ndipo akuchita maphunziro a zosunga ndi kubwereketsa ndalama, pomwe Mable ndi namandwa wokonza zovala ndipo ali ndi malo akeake osokeramo zovala. Koma onse awiriwa ndi atolankhani.
Vincent amachokera mmudzi mwa Mkutumula kwa mfumu yaikulu Kwataine ku Ntcheu pomwe Mable amachokera mmudzi mwa Kwachama, mfumu yaikulu Khongoni ku Kasiya mboma la Lilongwe.
| 15 |
Alimbikitsa chitetezo cha okhala mmalire Covid-19 Bungwe la Farmers Union of Malawi (FUM) lati pakufunika kulimbikitsa chitetezo cha anthu mmadera akumidzi omwe ali mmalire a dziko lino ndi maiko ena pofuna kupewa kufala kwa matenda a Covid-19.
Mlangizi wamkulu wa bungweli mboma la Mwanza Caswel Kachingwe adanena izi sabata latha pamwambo wopereka mabeseni, ndowa ndi sopo kumidzi ya kwa mfumu Nthache ndi Govati mbomalo polimbikitsa anthu kusamba mmanja ngati njira yopewera matendawa.
Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Nthache (Kumanzere) ndi Kwachingwe (Kumanja) kusamba mmanja pa mwambowo.
Maderawa, omwe ali mmalire a dziko ndi la Mozambique ndi komwe bungwelo likuchitako pulojekiti yolimbikitsa kadyedwe kabwino.
Nthendayi yavuta mmaiko oyandikana nawo ngati Mozambique. Anthu a kwa Nthache ndi Govati ayandikana ndi dzikoli moti akhonza kugwidwa ndi mliliwu ngati satetezedwa ndi kulimbikitsidwa kutsata njira zopewera. Tathandiza ndi zinthuzi ndipo tionetsetsa kuti zigwire ntchito popeza kupewa kumaposa kuchiza, adatero Kachingwe.
Iye adati zipangizozi zikaikidwa mmalo omwe anthu amadutsa kwambiri ndi mokumanirana.
Woona za umoyo mbomalo Ireen Zuze adavomerezana ndi Kachingwe pa zolimbikitsa chitetezo cha anthu mmaderawo.
Zipangizo zothandiza anthu kupewa makamaka kuti azisamba mmanja ndi sopo pafupifupi zikufunika. Tikuthokoza FUM pothangatira ntchito yathu yolimbikitsa umoyo wabwino mboma lino, adatero Zuze.
Mfumu Nthache idali yokondwa ndi kunena kuti ukhondo uyanja dera lake ndipo chitetezo ku Covid-19 chikula.
| 6 |
Fodya nkunazale Pamene alimi a fodya ali yakaliyakali kukonzekera ulimi wa 2015/16, mlangizi wa zaulimi wa fodya mboma la Rumphi, Charles Jere, walangiza alimi kuti atsatire ndondomeko ndi malangizo oyenera popanga nazale ya fodya pofuna kupindula ndi ulimi wawo.
Pocheza ndi Uchikumbe posachedwapa, Jere adati nazale ya fodya si ili ngati ya ndiwo zamasamba kaamba koti imafuna chisamaliro chapadera chifukwa kupanda kutero palibe chimene mlimi wa fodya angapindule ndi fodya nchifukwa chake pali mawu akuti fodya nkunazale.
Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Choyamba mlimi akuyenera kupeza malo omwe aikepo nazale yake. Malowa akuyenera kukhala kufupi ndi madzi oyenda kapena omwe akuoneka opanda tizilombo toyambitsa matenda a mtundu wina ulionse, adatero Jere.
Jere adati mlimi akuyenera kutipula nazale kutengera ndi kukula kwa munda wake. Mlangiziyu adati paekala imodzi bedi la nazale likuyenera kukhala lotalika mamita 30 ndi mita imodzi mlifupi pomwe hekitala imafunika mabedi atatu a muyezo woterewu.
Akapanga bedi lija mlimi akuyenera kutenga mapesi a chimanga nkuwasanja pabedi lija ndipo akatero awaotche ndi cholinga chofuna kupha tizilombo tomwe tidali mudothi tomwe tikadatha kuononga fodya panazalepo.
Apa adikire masiku awiri kapena atatu kuti ayambe kufesa fodya panazalepo, adafotokoza Jere.
Iye adati mlimi ayenera kuthira feteleza wokwana makilogalamu atatu asadafese fodya uja. Akafesa fodyayo athire mankhwala kuti aphe tizilombo monga nyerere zomwe zikhoza kudya mbewuyo.
Mankhwala ena ofunika kuthira panazale ndi amene amapha tizilombo toyambitsa matenda ena mufodya, adatero Jere.
Malinga ndi Jere, mankhwalawa amafunika kusungunula mutheka la madzi a mukheni ndi kuwathira panazale paja pataikidwa kale maudzu.
| 4 |
Boma Lati Dongosolo La Zachuma Lithandza Anthu Kupeza Ngongole Wolemba: Sylvester Kasitomu w.radiomaria.mw/wp-content/uploads/2019/09/botomani.jpg" alt="" width="294" height="333" />Wati anthu apeza ngongole mosavuta-Botomani Boma lati dongosolo la zachuma la mchaka cha 2019 mpaka 2020 lithandiza kuti anthu adzitha kubwereka ndalama zoti adzitha kutukulira maanja awo kaamba koti boma laika ndalamazi mu dongosololi.
Nduna ya zofalitsa nkhani a Mark Botomani anena izi pachilumba cha Chisi pa nyanja ya Chirwa mboma la Zomba, pamsonkhano othokoza anthu a pachilumbacho powavotera pa chisankho cha pa 21 May chaka chino.
A Botomani omwenso ndi phungu wa kunyumba ya malamulo mdera la Zomba Chisi, ati ena mwa anthu omwe adzapindule ndi ngongoleyi ndi asodzi omwe amapha msomba pa chilumbacho.
Pankhani za umoyo, iwo ati boma liyesetsa kumanga chipinda chochilira amai oyembekezera pachilumbacho ndipo powonjezera apo ati boma lachotsanso msonkho omwe anthu amaitanitsira magetsi a mphamvu ya dzuwa ndi cholinga choti anthu adzitha kugula magetsiwa.
Mmawu ake Gulupu Village Headman Tchuka ya pa chilumbacho, yapempha anthu kuti asiye kumanga nyumba za udzu okhaokha mmadzi a mnyanja ya Chirwa pofuna kuchepetsa vuto lakuphwa kwa madzi pa nyanjayo.
Anthu ambiri omwe akumanga mbowera zawo mmphepete mwa nyanjayi amagwiritsa ntchito udzu omwe amaumweta mphepete mwa nyanjayi choncho tipepha boma kuti libweretse anthu achitetezo ku nyanjayi kuti athamangite omwe akumanga zimbowera zawo mphepete mwa nyanjayi, anatero Group Tchuka.
Mwazina iyo yapempha boma kuti lipereke achitetezo omwe adzithamangitsa asodzi omwe akumamanga mbowelazi mmadzimo.
| 2 |
End of preview. Expand
in Data Studio
No dataset card yet
- Downloads last month
- 2