sent_id
stringlengths
3
7
english
stringlengths
3
1.06k
chichewa
stringlengths
4
3.03k
topic
stringclasses
8 values
source
stringclasses
17 values
en13818
Cyst
Chotupa
Medical
Book of medical terms
en13819
Ulcer
zilonda za pa khungu
Medical
Book of medical terms
en13820
Wound
Bala/chilonda
Medical
Book of medical terms
en13821
Mass
Chotupa
Medical
Book of medical terms
en13822
Boil
chithupsya
Medical
Book of medical terms
en13823
Scar
Chiphyera
Medical
Book of medical terms
en13824
Scales
Mamba
Medical
Book of medical terms
en13825
Ringworm
Zipere
Medical
Book of medical terms
en13826
Urticaria
Zidzolo
Medical
Book of medical terms
en13827
Rash
Nsungu
Medical
Book of medical terms
en13828
I would like to perform a general exam on you to check if everything is fine. It will involve me touching and looking at different areas of your body, I will also be using different instruments. If at any point you want me to stop, you can let me know.
Ndikufuna ndikuyezeni thupi lanu kuti ndiwone ngati thupi lanu lilibwino, ndikhala ndikukuyang’anani, kukukhudzani, kukugwirani komanso ndi kuyang’ana madela osiyanasiyana pa thupi lanu. Ndigwiritsa nchito zipangizo zosiyanasiyana, ngati mukuwona kuti ndisapitilize kukuyezani ndiwuzeni kuti ndisiye pa kukweza nkono kapena kuyankhula.
Medical
Book of medical terms
en13829
What is the date today?
Lero ndi tsiku lanji?
Medical
Book of medical terms
en13830
Do you know where you are right now?
Mukudziwa kumene muli pano?
Medical
Book of medical terms
en13831
Do you know why you are here?
Mukudziwa chimene mwaberera kuno lero?
Medical
Book of medical terms
en13832
Do you know what year we are in?
Mukudziwa chaka chimene tili lero?
Medical
Book of medical terms
en13833
I will now be touching your head
Ndikugwirani m’mutu.
Medical
Book of medical terms
en13834
I will now be touching your face
Ndikugwirani nkhope.
Medical
Book of medical terms
en13835
Close your eyes tight and open them again.
Tsekani maso mofinyika ndikuwatsegulanso.
Medical
Book of medical terms
en13836
Can you open your eyes against my resistance?
Mutha kutsegula maso anu ngakhale ndawa gunda chonchi?
Medical
Book of medical terms
en13837
Can you raise your eyebrows?
Mungathe kukweza zikope zanu za mwamba?
Medical
Book of medical terms
en13838
Can you smile?
Mungathe kumwetulira?
Medical
Book of medical terms
en13839
Can you bite down your teeth?
Mungathe kuluma mano anu pakamodzi?
Medical
Book of medical terms
en13840
Can you open your mouth? Close it.
Mungathe kutsegula mkamwa mwanu? Tsekani.
Medical
Book of medical terms
en13841
Can you open your mouth against my resistance?
Mungathe kutsegula mkamwa mwanu, ngakhale ndakutsekani?
Medical
Book of medical terms
en13842
Relax your jaw, so that I tap your chin.
Fewetsani masagwidi anu ndi masaya anu kuti ndikhudze nawo chibwanocho?
Medical
Book of medical terms
en13843
Close your eyes, I will use this cotton on your face to touch you, tell me everytime you feel I’ve touched you.
Tsekani maso, ndigwiritsa nchito thonje kukhudza nkhope yanu, ndipo mundiwuze ngati mukumva kena kalikonse pamene ndakukhuzani.
Medical
Book of medical terms
en13844
Close your eyes, I will use this object on your face to touch you, tell me everytime you feel I’ve touched you.
Tsekani maso, ndigwiritsa nchito ichi kukhudza nkhope yanu, ndipo mundiwuze ngati mukumva kena kalikonse pamene ndakukhuzani.
Medical
Book of medical terms
en13845
Does it feel the same on both sides?
Zikumveka chimodzimodzi mbali zonse?
Medical
Book of medical terms
en13846
I will pull your eyelids down, look up, look down, look to the side.
Ndigwira nawo zikope zanu, muyang’ane pansi, muyang’ane mmwamba, muyang’ane kumbali.
Medical
Book of medical terms
en13847
Follow the movement of my finger with your eyes, keep your head straight.
Mutsatire chala changachi ndi maso anu, musasunthe mutu wanu.
Medical
Book of medical terms
en13848
Can you cover one eye with your hand and read these letters on the line with your other eye?
Phimbani diso limodzi, ndi dzanja lanu, ndipo muwerengele diso linalo malembo awa?
Medical
Book of medical terms
en13849
I will now shine a light in your eye.
Ndiunikako mmaso mwanu.
Medical
Book of medical terms
en13850
Can you look over there and then look over here? (at my pen)
Muthakuyang’ana uko, ndikuyang’ananso kuno?
Medical
Book of medical terms
en13851
Can you cover one eye with your hand, can you see my fingers? Tell me when you see they have disappeared.
Phimbani diso limodzi ndi dzanja lanu, mukuwona zala zanga zi? Mundiwuze mukawona kuti zabisika.
Medical
Book of medical terms
en13852
Look to the side, I will now use a cotton to touch your eye.
Yang’anani kumbali, ndigwiritsa nchito thonje kukhudza diso lanu.
Medical
Book of medical terms
en13853
I will insert this otoscope inside your ear to see inside.
Ndilowetsa nawo ka chida aka nkhutu mwanu kuti tiwunike mo.
Medical
Book of medical terms
en13854
I will close one ear, and I will speak in the other ear and you should repeat what I’m saying.
Nditseka khutu lanu limodzi ndipo munditsatizire chimene ndikunena mu khutu lanu linali.
Medical
Book of medical terms
en13855
Can you hear the sound of this tuning fork?
Mukumva kulira kwa chidachi?
Medical
Book of medical terms
en13856
I will put this instrument (tuning fork) behind your ear, then beside your ear and you should compare which is the loudest.
Ndiyika chidachi kuseli kwa khutu lanu, ndi kutsogolo kwa khutu lanu ndipo mufananiza kuti mbali imene likumveka kulira kwambiri ndi litiro.
Medical
Book of medical terms
en13857
I will place this instrument (tuning fork) in the middle of your forehead and let me know which ear you hear it the loudest, or if it’s the same in both ears, and tell me when you stop hearing the sound.
Ndiyika chidachi pa chipumi chanu, ndipo mundiwuze khutu limene chikumveka kwambiri ndi liti, kapena ngati chikumveka chimodzimodzi makutu onse. Mundiwuzenso chikasiya kulira.
Medical
Book of medical terms
en13858
I will now look inside your nose with this light.
Ndiunika nawo nkati mwa mphuno mwanumo.
Medical
Book of medical terms
en13859
Close your eyes, I will put something under your nose and you should tell me what you are smelling.
Mutseke maso anu, ndiyika chinthu pansi pa mphuno yanu ndipo mundiwuze kuti mukumva fungo lanji
Medical
Book of medical terms
en13860
Block one nostril and breath in and out with your nose.
Mutseke mphuno imodzi nde muzipumira yinayo, nkati ndi kunja.
Medical
Book of medical terms
en13861
Open your mouth and move your tongue side to side.
Tsegulani pakamwa, nde mugwedeze lilime.
Medical
Book of medical terms
en13862
Open your mouth and raise your tongue.
Tsegulani pakamwa, nde mukweze lilime mwamba.
Medical
Book of medical terms
en13863
Relax your tongue and cheeks.
Fewetsani lilime ndi masaya anu.
Medical
Book of medical terms
en13864
Say “aaah”
Nenani “aah”
Medical
Book of medical terms
en13865
I will touch your uvula (back of throat), you will feel like vomiting or feel uncomfortable.
Ndikhudzanawo kummeroko, nde apa mumva ngati mukufuna kusanza kapena kusowa mtendere.
Medical
Book of medical terms
en13866
Lift your head.
Kwezani mutu mwamba.
Medical
Book of medical terms
en13867
Turn your head to the side.
Tembenuzani mutu wanu kumbali uku.
Medical
Book of medical terms
en13868
Turn your head to the side against my resistance.
Tembenuzani mutu wanu kumbali uku ngakhale ndakugwirani.
Medical
Book of medical terms
en13869
Lift your shoulders against my resistance.
Kwezani mapewa anu ngakhale ndakugwirani.
Medical
Book of medical terms
en13870
will now touch the lymph nodes in your neck to check for any swelling.
Ndigwira nawo masagwidi anu kuti ndimveko ngati muli ndi zotupa.
Medical
Book of medical terms
en13871
Breathe in and out while I touch the blood vessels in your neck.
Pumirani mkati ndi kunja pamene ndikugwira nawo misempha ya pa khosi.
Medical
Book of medical terms
en13872
Roll up your sleeves of your shirt, I want to test the function of your arms and your hands
Pindani mikono ya malaya anu mwamba, kuti ndiwone nawo mikono yanu ndi manja anu kuti zikugwira ntchito bwanji.
Medical
Book of medical terms
en13873
Spread your fingers.
Tambasulani zala zanu.
Medical
Book of medical terms
en13874
I will check the blood flow in your hands and fingers
Ndiwonako mmene magazi akuyendera mmanja ndi muzala zanu.
Medical
Book of medical terms
en13875
I will squeeze your finger a little bit
Ndifinya chala chanu pang’ono.
Medical
Book of medical terms
en13876
I will pinch your hand a little bit
Nditsina dzanja lanu pang’ono.
Medical
Book of medical terms
en13877
Can you put your fingers like this?
Mutha kuyika zala zanuzi chonchi?
Medical
Book of medical terms
en13878
With your finger, touch your nose, then touch my finger then your nose again.
Ndi chala chanu, mukhuze mphuno yanu, kenako mukhuze chala changa kenakonso mukhuze mphuno yanu.
Medical
Book of medical terms
en13879
Can you relax your arm/hand, I will move it around myself.
Fewetsani mkono wanu,/dzanja lanu ndikhala ndikuyiyendetsa.
Medical
Book of medical terms
en13880
Can you extend your arms and close your eyes, I will apply resistance but try to keep them in the same place.
Mutambasule mikono ndi kutseka maso, ndiyesela kuyika mphamvu zanga koma inu muyesetse kukhazika mikono yo malo amodzi.
Medical
Book of medical terms
en13881
Put both hands on your thighs and make them face down at the same time, then face up at the same time and do this as fast as possible.
Muyike manja anu pa ntchafu zanu ndikuwatembenuza kuyang’ana pansi ndikuwatembenuzanso kuyang’ana mwamba kwa nthawi imodzi ndipo mupange mwachangu pamene mungathele.
Medical
Book of medical terms
en13882
Squeeze my hand as hard as possible.
Finyani dzanja langa ndi mphamvu zanu zonse.
Medical
Book of medical terms
en13883
Push my hand while I push yours.
Kankhani dzanja langa pamene ndikukankha lanu.
Medical
Book of medical terms
en13884
Bend your arm.
Pindani mkono wanu.
Medical
Book of medical terms
en13885
Can you make a fist?
Mutha kukunga bakera?
Medical
Book of medical terms
en13886
Drop your wrist.
Gwetsani dzanja lanu.
Medical
Book of medical terms
en13887
Close your eyes and tell me if I’m moving your finger/toe up or down.
Tsekani maso anu, mundiwuze ngati ndikukweza chala chanu mwamba kapena ngati ndikutsitsa chala chanu pansi.
Medical
Book of medical terms
en13888
I will put this instrument on your arm can you feel the vibrations of it? Tell me when it stops vibrating.
Ndiyika chidachi pamkono wanu, mukumva kunjenjemela kwa chidachi? Mundiwuze chikasiya kunjenjemela.
Medical
Book of medical terms
en13889
Close your eyes I will use this cotton to touch your arm, tell me everytime you feel I’ve touched you.
Tsekani maso, ndigwiritsa nchito thonje kukhudza mkono wanu, ndipo mundiwuze ngati mukumva kena kalikonse pamene ndakukhuzani.
Medical
Book of medical terms
en13890
Close your eyes I will use this object to touch your arm, tell me everytime you feel I’ve touched you.
Tsekani maso, ndigwiritsa nchito chinthu ichi kukhudza mkono wanu, ndipo mundiwuze ngati mukumva kena kalikonse pamene ndakukhuzani.
Medical
Book of medical terms
en13891
Does it feel the same on both sides?
Zikumveka chimodzimodzi mbali zonse?
Medical
Book of medical terms
en13892
will tap you with this instrument here to test your reflexes
Ndikukhuzani ndi chidachi kuti ndiyeze kamvedwe kanu kutengera chidachi
Medical
Book of medical terms
en13893
Can you remove the top half of your clothes (shirt) so that I can listen to your heart, and breathing as well as touching you to see if there are any abnormalities, is that okay with you?
Mungavuleko kumtundako kuti ndimve mtima wanu, komanso kuti ndiwone mapumidwe anu, ndigwiranawonso mchifuwamo kuti ndiwone ngati kuli vuto lililonse, mundilora kutero?
Medical
Book of medical terms
en13894
Do you feel pain anywhere on your chest?
Mukumva ululu paliponse mchifuwa mwanu?
Medical
Book of medical terms
en13895
I will now use my stethoscope to listen to your heart.
Ndimvetsera nawo mtima wanu ndi chidachi.
Medical
Book of medical terms
en13896
I will tap on your chest using my hands.
Ndiguguda nawo pachifuwa panu ndi manja anga.
Medical
Book of medical terms
en13897
will hold your chest, please take deep breaths in and out.
Ndigwirako pachifuwapa, nde muzipumira mkati ndi kunja
Medical
Book of medical terms
en13898
Breathe in, breathe out.
Pumirani mkati, pumirani kunja.
Medical
Book of medical terms
en13899
Hold your breath.
Gwirani mpweya.
Medical
Book of medical terms
en13900
Take deep breaths in and out with your mouth while I listen to your chest
Pumirani kwambiri mkati ndi kunja ndi kamwa lanu, pamene ndikumvetsera mtima wanu.
Medical
Book of medical terms
en13901
Turn around so that I listen to your back.
Tembenukani ndimvetsereko ku msana.
Medical
Book of medical terms
en13902
I would like to perform a breast exam on you to assess any abnormalities, I will be looking and touching your breasts, there will be a nurse with us so that you are more comfortable, then you will take off your top and bra, when you are done you can cover yourself with a sheet. Is that okay?
Ndikufuna kuyeza mabere anu, kuti ndiwone ngati pali vuto lililonse, ndikhala ndikukhuza komanso kuyang’ana mabere anu. Pakhala namwino amene angatithangathire mukumasuka kwanu. Ndiye muvule malaya ndi kamisolo yanu, mukatha muzivindikira ndi chofunda ichi. Mutilora pa zimenezi?
Medical
Book of medical terms
en13903
Do you have any problem with any one of your breasts?
Muli ndi vuto ndi bere lina lililonse?
Medical
Book of medical terms
en13904
Put your hands on your waist.
Ikani manja anu mchiuno.
Medical
Book of medical terms
en13905
Lean forward.
Welamani.
Medical
Book of medical terms
en13906
Lie on your back.
Gonani chagada
Medical
Book of medical terms
en13907
Put your hands above your head and put your shoulders back.
ikani manja anu ku mutu, ndipo mukankhile mapewa anu kumbuyo.
Medical
Book of medical terms
en13908
Put your hand behind your head while while I feel your breast.
Muyika dzanja lanu kuseli kwa mutu wanu pamene ndikukhuza bere lanu.
Medical
Book of medical terms
en13909
Make your chest tense.
Tawumitsani chifuwa chanu.
Medical
Book of medical terms
en13910
Lift your arm so that I look at your armpit.
Kwezani mkonowo, kuti ndiwone nawo kunkhwapa.
Medical
Book of medical terms
en13911
I will now squeeze your nipple.
Ndikufinyani nsonga ya bere.
Medical
Book of medical terms
en13912
I would like to perform an abdominal exam on you to assess any abnormalities, I will be looking, touching and listening to your abdomen, lift up your shirt to only expose your abdomen. (Cover your top)
Ndikufuna kuyeza pa mimba panu, kuti ndiwone ngati pali vuto lililonse, ndikhala ndikukhuza komanso kuyang’ana ndi kumvetsera pa mmimba po. Mukwezeko malaya mwamba kuti ndingowona pamimba pokhapa. (Kuntundako, phimbani)
Medical
Book of medical terms
en13913
Do you feel pain anywhere on your abdomen before I start?
Mukumva ululu ulionse pa mimba ndisanayambe?
Medical
Book of medical terms
en13914
Lie down on your back and put your hands to the side.
Gonani chagada, ndi kuyika mikonoyo mbali.
Medical
Book of medical terms
en13915
I will listen to the sounds of your stomach with my stethoscope.
Ndimvetserako maphokoso ammimba mwanu ndi chida ichi.
Medical
Book of medical terms
en13916
I will touch your abdomen now.
Panopa ndikhuza pa mimba panu.
Medical
Book of medical terms
en13917
Breathe in and out while I touch your abdomen.
Pumirani mkati ndi kunja pamene ndikukhuza pa mmimba panu.
Medical
Book of medical terms